Levitiko 23:1-44

23  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Zikondwerero+ za Yehova zimene muyenera kulengeza+ ndiyo misonkhano yopatulika. Izi ndi zikondwerero zanga:  “‘Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Limeneli ndi tsiku la msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito iliyonse chifukwa limeneli ndi sabata la Yehova kulikonse kumene mungakhale.+  “‘Zikondwerero+ za Yehova, kapena kuti misonkhano yopatulika+ imene muyenera kulengeza pa nthawi yake yoikidwiratu+ ndi iyi:  M’mwezi woyamba,* pa tsiku la 14 m’mweziwo,+ madzulo kuli kachisisira,* lizikhala tsiku la pasika+ wa Yehova.  “‘Pa tsiku la 15 m’mwezi umenewu, muzichita chikondwerero cha Yehova cha mikate yopanda chofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda chofufumitsa imeneyi masiku 7.+  Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika+ ndipo musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa.  Kwa masiku 7, muzipereka kwa Yehova nsembe zotentha ndi moto. Pa tsiku la 7 muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa.’”  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 10  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mukalowa m’dziko limene ndikukupatsani, n’kukolola mbewu za m’dzikomo, muzibweretsa kwa wansembe mtolo umodzi wa zipatso zanu zoyambirira.+ 11  Ndipo wansembe aziweyulira mtolowo uku ndi uku+ pamaso pa Yehova kuti Mulungu akuyanjeni. Sabata likatha, ndiyeno tsiku lotsatira, wansembe aziweyulira mtolowo uku ndi uku. 12  Pa tsiku loweyulira mtolo wanu uku ndi uku, muzipereka mwana wa nkhosa wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, kuti akhale nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova. 13  Popereka nsembe imeneyi muziperekanso nsembe yambewu. Nsembeyo izikhala ufa wosalala wothira mafuta, muyezo wake magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa, kuti ikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova, yafungo lokhazika mtima pansi. Muziperekanso vinyo wa nsembe yachakumwa, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini.* 14  Musadye mkate, mbewu zokazinga kapena mbewu zatsopano kufikira tsiku limeneli,+ mpaka mutabweretsa nsembe ya Mulungu wanu. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale. 15  “‘Kuchokera pa tsiku lotsatana ndi sabata, pamene munabweretsa mtolo kuti ukhale nsembe yoweyula,* muziwerenga masabata* 7,+ ndipo akwane ndendende. 16  Kuchokera pa tsiku limene sabata la 7 lakwanira, pazidutsa masiku 50,+ ndipo muzipereka nsembe yambewu zatsopano+ kwa Yehova. 17  Muzibweretsa mitanda iwiri ya mkate+ wa m’nyumba mwanu kuti ikhale nsembe yoweyula. Mitandayo izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Poiphika izikhala ndi chofufumitsa,+ ndipo muziipereka kwa Yehova monga zipatso zoyambirira kucha.+ 18  Popereka mitanda ya mkateyi muziperekanso ana a nkhosa amphongo opanda chilema okwana 7,+ aliyense wa chaka chimodzi, komanso ng’ombe imodzi yaing’ono yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo. Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe yopsereza, nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. Ziziperekedwa pamodzi ndi nsembe yambewu, ndi nsembe zachakumwa kuti zikhale fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 19  Muziperekanso mwana wa mbuzi mmodzi+ monga nsembe yamachimo, ndi ana a nkhosa amphongo awiri, aliyense wachaka chimodzi, monga nsembe yachiyanjano.+ 20  Ndipo wansembe aziweyulira uku ndi uku+ ana a nkhosa awiriwo pamodzi ndi mitanda ya mkate ya zipatso zoyambirira kucha, monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi zizikhala zinthu zopatulika kwa Yehova ndipo zizikhala za wansembe.+ 21  Muzilengeza+ pa tsiku lomweli kuti muchite msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale kulikonse kumene mungakhale m’mibadwo yanu yonse. 22  “‘Mukamakolola zinthu za m’munda m’dziko lanu, musamachotseretu zonse m’mphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha m’munda mwanumo.+ Zotsalazo muzisiyira wovutika+ ndi mlendo wokhala pakati panu.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’” 23  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 24  “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘M’mwezi wa 7,+ pa tsiku loyamba m’mweziwo, muzipuma pa ntchito zanu zonse. Limeneli ndi tsiku la chikumbutso, tsiku loliza lipenga,+ tsiku la msonkhano wopatulika.+ 25  Musamagwire ntchito iliyonse yolemetsa pa tsikuli, ndipo muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova.’” 26  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 27  “Tsiku la 10 m’mwezi wa 7 umenewu ndi tsiku la mwambo wophimba machimo.+ Muzichita msonkhano wopatulika ndipo muzidzisautsa*+ ndi kupereka nsembe+ yotentha ndi moto kwa Yehova. 28  Pa tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wophimba machimo+ anu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 29  Munthu aliyense amene sadzisautsa pa tsiku limeneli aphedwe kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 30  Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limeneli, ndidzamuwononga ndi kum’chotsa pakati pa anthu amtundu wake.+ 31  Musamagwire ntchito iliyonse.+ Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale ku mibadwo yanu yonse, kulikonse kumene mungakhale. 32  Ili ndi sabata lopuma pa ntchito zanu zonse,+ ndipo muzidzisautsa+ madzulo pa tsiku la 9 m’mweziwo. Muzisunga sabata kuyambira madzulo kufikira madzulo tsiku lotsatira.” 33  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 34  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Tsiku la 15 m’mwezi wa 7 umenewu, ndi tsiku lochitira Yehova chikondwerero cha misasa kwa masiku 7.+ 35  Tsiku loyamba la chikondwererocho ndi la msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito iliyonse yolemetsa. 36  Kwa masiku 7 muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova. Pa tsiku la 8 muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzipereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova. Umenewu ndi msonkhano wapadera. Musagwire ntchito iliyonse yolemetsa. 37  “‘Zimenezi ndizo zikondwerero+ za Yehova zimene muyenera kulengeza monga misonkhano yopatulika+ yoperekera nsembe zotentha ndi moto+ kwa Yehova. Imeneyi ndiyo misonkhano yoperekera nsembe zopsereza,+ nsembe zambewu+ ndi nsembe zachakumwa+ motsatira ndandanda ya tsiku ndi tsiku. 38  Muzichita zimenezi kuwonjezera pa kusunga masabata a Yehova,+ kupereka mphatso zanu,+ nsembe zanu zonse za lonjezo+ ndi nsembe zanu zonse zaufulu+ zimene muyenera kupereka kwa Yehova. 39  Pa tsiku la 15 m’mwezi wa 7, pamene mwakolola zinthu za m’munda m’dziko lanu, muzichita chikondwerero+ cha Yehova masiku 7.+ Tsiku loyamba la chikondwererocho ndi tsiku lopuma pa ntchito zanu zonse, ndipo muzipumanso pa ntchito zanu zonse pa tsiku la 8.+ 40  Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza,+ nthambi zikuluzikulu za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi ya m’chigwa.* Mukatero muzisangalala+ kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 41  Muzichitira Yehova chikondwerero chimenechi masiku 7 pa chaka,+ m’mwezi wa 7. Limeneli ndi lamulo m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale. 42  Muzikhala m’misasa masiku 7.+ Mbadwa zonse za Isiraeli zizikhala m’misasa,+ 43  kuti anthu a m’mibadwo yanu yonse azidziwa+ kuti ana a Isiraeli ndinawakhalitsa m’misasa powatulutsa m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’” 44  Pamenepo Mose anafotokozera ana a Isiraeli za zikondwerero+ za Yehova.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mwezi wa Abibu kapena kuti Nisani, umene ndi mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda kuyambira pamene anachoka ku Iguputo. Mwezi wa Abibu umayambira chakumapeto kwa mwezi wa March mpaka mkatikati mwa mwezi wa April. Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 12:6.
“Muyezo wa hini” ndi wofanana ndi malita atatu ndi hafu.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.
Kapena kuti “milungu.”
Onani mawu a m’munsi pa Le 16:29.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.