Levitiko 14:1-57

14  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Ili likhale lamulo lokhudza wakhate+ pa tsiku limene adzam’bweretsa kwa wansembe kudzagamulidwa kuti ndi woyera.+  Wansembe azipita kunja kwa msasa kukamuona. Ngati munthuyo wachira khate lake,+  wansembe azim’lamula kuti atenge zofunika pa kudziyeretsa kwake. Azitenga mbalame zamoyo ziwiri zosadetsedwa,+ nthambi ya mtengo wa mkungudza,+ ulusi wofiira kwambiri+ ndi kamtengo ka hisope.+  Ndipo wansembe azilamula kuti mbalame imodzi aiphere pamwamba pa madzi otunga kumtsinje,+ amene ali m’chiwiya chadothi.  Koma azitenga mbalame inayo pamodzi ndi nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope, n’kuziviika pamodzi ndi mbalame yamoyo ija m’magazi a mbalame imene aiphera pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija.  Kenako wansembe azidontheza+ magaziwo maulendo 7+ pamunthu amene akudziyeretsa ku khateyo, ndipo azigamula kuti munthuyo ndi woyera.+ Akatero, aziulutsa mbalame yamoyo ija pabwalo.+  “Ndiyeno wodziyeretsayo azichapa zovala zake+ ndi kumeta tsitsi lake lonse, kenako azisamba+ ndipo azikhala woyera. Akatero, angathe kulowa mumsasa, koma azikhala kunja kwa hema wake masiku 7.+  Pa tsiku la 7 azimeta tsitsi lake lonse lakumutu,+ ndevu zake zonse ndi nsidze zonse. Azimeta tsitsi lake lonse, ndipo azichapa zovala zake ndi kusamba madzi otunga kumtsinje. Akatero, azikhala woyera. 10  “Tsopano pa tsiku la 8,+ iye azitenga nkhosa zazing’ono zamphongo ziwiri zopanda chilema, ndi nkhosa yaing’ono yaikazi + imodzi yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi. Azitenganso ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake ya mbewu+ yothira mafuta, ndi muyezo umodzi* wa mafuta.+ 11  Pamenepo wansembe amene wagamula kuti munthuyo ndi woyera, azikaonetsa amene akudziyeretsayo, ndi zinthu zakezo kwa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako. 12  Kenako wansembeyo azitenga nkhosa yaing’ono yamphongo imodzi ndi kuipereka monga nsembe ya kupalamula+ pamodzi ndi muyezo umodzi+ wa mafuta uja. Zimenezi aziziweyulira* uku ndi uku monga nsembe yoweyula+ yoperekedwa kwa Yehova. 13  Ndipo azipha nkhosa yaing’ono yamphongoyo pamalo+ amene nthawi zonse amapherapo nyama ya nsembe yamachimo ndi nsembe yopsereza, pamalo oyera.+ Azichita zimenezi chifukwa nsembe ya kupalamula ndi ya wansembe+ mofanana ndi nsembe yamachimo. Nsembe ya kupalamula ndi yopatulika koposa. 14  “Pamenepo wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe ya kupalamula, n’kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja.+ 15  Akatero, wansembeyo atengeko mafuta pamuyezo umodzi+ uja ndi kuwathira pachikhatho cha dzanja lake lamanzere. 16  Ndiyeno wansembe aziviika chala chake cha kudzanja lamanja m’mafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzere, ndipo azidontheza pansi ena mwa mafutawo ndi chala chakecho maulendo 7,+ pamaso pa Yehova. 17  Koma mafuta amene atsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja pamene anam’paka magazi a nsembe ya kupalamula.+ 18  Ndiyeno mafuta otsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu pa munthu amene akudziyeretsayo, ndipo wansembe azim’phimbira machimo+ ake pamaso pa Yehova. 19  “Pamenepo wansembe azipereka nsembe yamachimo+ ndi kuphimba machimo a munthu amene akudziyeretsa ku chodetsa chakeyo. Kenako wansembe azipha nyama ya nsembe yopsereza. 20  Ndiyeno wansembe azipereka nsembe yopsereza ndi nsembe yambewu+ paguwa lansembe. Akatero, wansembe+ azim’phimbira machimo,+ ndipo munthuyo azikhala woyera.+ 21  “Koma ngati munthuyo ali wosauka+ ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi,+ azibweretsa nkhosa yaing’ono yamphongo imodzi monga nsembe ya kupalamula. Nsembeyo aziiweyulira uku ndi uku kuti am’phimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa, monga nsembe yake yambewu. 22  Komanso azibweretsa ana awiri a njiwa+ kapena ana awiri a nkhunda, malinga ndi zimene iye angakwanitse. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. 23  Ndipo azibweretsa zimenezi kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako+ pamaso pa Yehova. Azibweretsa zinthuzi pa tsiku la 8+ kuti wansembe agamule kuti munthuyo ndi woyera.+ 24  “Kenako wansembe azitenga nkhosa yaing’ono yamphongo ya nsembe ya kupalamula,+ ndi muyezo umodzi wa mafuta uja, ndipo wansembeyo aziweyulira zinthu zimenezi uku ndi uku, monga nsembe yoweyula yoperekedwa kwa Yehova.+ 25  Ndiyeno wansembe azipha nkhosa yaing’ono yamphongo ya nsembe ya kupalamula. Akatero azitenga ena mwa magazi a nsembe ya kupalamulayo n’kuwapaka m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja.+ 26  Pamenepo wansembeyo azithira ena mwa mafutawo pachikhatho cha dzanja lake lamanzere.+ 27  Akatero azidontheza+ ndi chala chake cha dzanja lamanja ena mwa mafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzerewo maulendo 7, pamaso pa Yehova. 28  Kenako wansembe azipaka ena mwa mafuta amene ali pachikhatho chake m’munsi pakhutu la kudzanja lamanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu chakumwendo wa kudzanja lamanja pamene anam’paka magazi a nsembe ya kupalamula.+ 29  Ndiyeno mafuta otsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu+ pa munthu amene akudziyeretsayo, kuti am’phimbire machimo ake pamaso pa Yehova. 30  “Kenako wansembe azipereka mmodzi mwa ana a njiwa kapena m’modzi mwa ana a nkhunda, malinga ndi zimene munthuyo angakwanitse.+ 31  Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo+ ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza,+ azipereka imene angakwanitse pamodzi ndi nsembe yambewu. Pamenepo wansembe aziphimba machimo+ a munthu amene akudziyeretsayo pamaso pa Yehova. 32  “Limeneli ndi lamulo lokhudza munthu amene ali ndi nthenda ya khate, amene sangakwanitse kupeza zinthu zofunika kuti amugamule kukhala woyera.” 33  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti: 34  “Mukakafika m’dziko la Kanani,+ limene ine ndikukupatsani kuti likhale lanu,+ ndipo ndikakaika nthenda ya khate m’nyumba iliyonse m’dziko lanulo,+ 35  mwiniwake wa nyumbayo azibwera kwa wansembe ndikumuuza kuti, ‘Pakhoma* la nyumba yanga ndaona chinachake chooneka ngati nthenda yakhate.’ 36  Pamenepo wansembe azilamula kuti atulutse katundu m’nyumbamo iye asanafike kudzaona nthendayo. Azichita zimenezi kuti wansembe asagamule kuti chilichonse m’nyumbamo n’chodetsedwa. Akatero wansembe azibwera kudzaona nyumbayo. 37  Akaona nthendayo, n’kupeza kuti ili m’makoma a nyumba, ndipo ikuoneka ngati mawanga obiriwira monkera ku chikasu kapena ofiirira, komanso mawangawo akuoneka ozama, 38  wansembe azituluka m’nyumbamo n’kukaima pakhomo, ndipo azitseka+ nyumbayo masiku 7. 39  “Pa tsiku la 7, wansembe azibweranso kudzaona nyumbayo.+ Ngati nthendayo yafalikira m’makoma ake, 40  wansembe azilamula kuti achotse+ miyala imene ili ndi nthendayo, ndi kuti akaiponye kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 41  Ndiyeno wansembe alamule kuti apale mkati mwa nyumba yonseyo, ndi kutaya dothi lomangira limene agumulalo kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 42  Akatero azitenga miyala ina ndi kumanga pamene panali miyala yakaleyo. Kenako aziwalamula kumata nyumbayo ndi dothi lina. 43  “Koma ngati nthendayo yabwerera n’kufalikiranso m’nyumbamo, atachotsa miyala ija, kupala nyumbayo ndi kuimata, 44  wansembe+ azibweranso kudzaiona. Ngati nthendayo yafalikira m’nyumbamo, limenelo ndi khate loopsa.+ Nyumbayo ndi yodetsedwa. 45  Pamenepo azilamula kuti nyumbayo aigwetse pamodzi ndi miyala yake, matabwa ake ndi dothi lake lonse lomangira, ndipo zonsezi azitengere kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa.+ 46  Koma aliyense wolowa m’nyumbayo pa masiku amene wansembe walamula kuti munthu asalowemo,+ azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 47  Ndipo aliyense amene wagona m’nyumbayo, ndi aliyense amene wadyeramo chakudya azichapa zovala zake.+ 48  “Koma ngati wansembe wabwera kudzaona nyumbayo ataimata, n’kupeza kuti nthendayo sinafalikire m’nyumbayo, wansembe azigamula kuti nyumbayo ndi yoyera chifukwa nthendayo yatha.+ 49  Ndiyeno kuti achite mwambo woyeretsa nyumbayo, azitenga mbalame ziwiri,+ nthambi ya mtengo wa mkungudza,+ ulusi wofiira kwambiri+ ndi kamtengo ka hisope. 50  Ndipo wansembe azipha mbalame imodzi pamwamba pa madzi a kumtsinje,+ amene ali m’chiwiya chadothi. 51  Kenako azitenga nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope,+ ulusi wofiira kwambiri ndi mbalame yamoyo ija. Zimenezi aziziviika m’magazi a mbalame imene yaphedwa pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija, ndipo azidontheza magaziwo+ maulendo 7+ cha kumene kuli nyumbayo. 52  Ndiyeno aziyeretsa nyumbayo pogwiritsa ntchito magazi a mbalame ija, madzi otunga kumtsinje, mbalame yamoyo ija, nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope ndi ulusi wofiira kwambiri. 53  Pamenepo aziulutsa mbalame ya moyo ija pabwalo, kunja kwa mzinda. Akatero aziyeretsa+ nyumbayo, ndipo izikhala yoyera. 54  “Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda iliyonse yakhate,+ nthenda yothothoka tsitsi,+ 55  khate la pachovala+ ndi la m’nyumba, 56  chotupa, nkhanambo ndi chikanga.+ 57  Lamulo limeneli laperekedwa kuti likhale malangizo+ osonyeza pamene chinthu chili chodetsedwa ndi pamene chili choyera. Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda yakhate.”+

Mawu a M'munsi

“Muyezo umodzi” umenewu ndi wofanana ndi gawo limodzi mwa magawo atatu a lita.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”