Levitiko 17:1-16

17  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Uza Aroni ndi ana ake ndi ana onse a Isiraeli kuti, ‘Yehova walamula kuti:  “‘“Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli akapha ng’ombe, nkhosa kapena mbuzi mumsasa, kapena kunja kwa msasa,  koma osabwera nayo pakhomo la chihema chokumanako,+ kuti aipereke monga nsembe kwa Yehova patsogolo pa chihema cha Yehova, ameneyo adzakhala ndi mlandu wa magazi. Munthu ameneyo wakhetsa magazi, ndipo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+  Lamulo limeneli laperekedwa kuti nsembe zimene ana a Isiraeli akuzipereka kunja,+ azibwera nazo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako kuti azipereke kwa Yehova.+ Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe zachiyanjano kwa Yehova.+  Wansembe aziwaza magazi a nyamazo paguwa lansembe la Yehova+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako, ndipo azitentha mafuta+ ake kuti likhale fungo lokhazika mtima pansi loperekedwa kwa Yehova.+  Chotero asamaperekenso nsembe zawo ku ziwanda zooneka ngati mbuzi*+ zimene akuchita nazo chiwerewere.+ Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale, m’mibadwo yanu yonse.”’  “Uwauzenso kuti, ‘Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, amene wapereka nsembe yopsereza+ kapena nsembe iliyonse,  koma osabwera nayo pakhomo la chihema chokumanako kuti aipereke kwa Yehova,+ munthu ameneyo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 10  “‘Munthu aliyense wa nyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, akadya magazi alionse,+ ndidzam’kana*+ ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake. 11  Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi+ ndipo ine ndakuikirani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbirani machimo.+ Zili choncho popeza magazi+ ndiwo amaphimba machimo,+ chifukwa moyo uli m’magaziwo. 12  N’chifukwa chake ndauza ana a Isiraeli kuti: “Pasapezeke munthu wodya magazi ndipo pasapezeke mlendo wokhala pakati panu+ wodya magazi.”+ 13  “‘Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli kapena mlendo amene akukhala pakati panu akapita kosaka nyama, ndipo wapha nyama kapena mbalame yololeka kudya, azithira magazi ake pansi+ ndi kuwafotsera ndi dothi.+ 14  Pakuti moyo wa nyama iliyonse ndi magazi ake, chifukwa m’magazimo ndi mmene muli moyo. N’chifukwa chake ndauza ana a Isiraeli kuti: “Musamadye magazi a nyama iliyonse, chifukwa moyo wa nyama ina iliyonse ndi magazi ake.+ Aliyense wodya magaziwo ayenera kuphedwa.”+ 15  Munthu aliyense amene wadya nyama imene waipeza yakufa, kapena yophedwa ndi chilombo,+ kaya akhale nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, munthu ameneyo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ Kenako azikhala woyera. 16  Koma ngati sanachape zovala zakezo komanso sanasambe thupi lonse, ameneyo ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chake.’”+

Mawu a M'munsi

Olambira ziwanda zooneka ngati mbuzizo anali kuganiza kuti ziwandazo zinali zolengedwa za ubweya wambiri zooneka ngati tonde wa mbuzi.
Mawu ake enieni, “ndidzaika nkhope yanga motsutsana naye.”