Levitiko 12:1-8

12  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mkazi akatenga pakati+ n’kubereka mwana wamwamuna, azikhala wodetsedwa masiku 7. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira akamasamba.+  Ndipo pa tsiku la 8, khungu la mwanayo lizidulidwa.+  Kwa masiku enanso 33, mkaziyo azikhala panyumba kuti ayeretsedwe ku magazi ake. Asakhudze chilichonse chopatulika, ndipo asalowe m’malo oyera, kufikira masiku a kuyeretsedwa kwake atakwanira.+  “‘Akabereka mwana wamkazi, azikhala wodetsedwa kwa masiku 14. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira akamasamba. Kwa masiku enanso 66 azikhala panyumba kuti ayeretsedwe ku magazi ake.  Ndiyeno masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa+ kuti ikhale nsembe yamachimo.  Ndipo wansembeyo aziipereka kwa Yehova ndi kum’phimbira machimo, pamenepo mkaziyo azikhala woyera pa kukha magazi kwake.+ Limeneli ndi lamulo la mkazi amene wabereka mwana wamwamuna kapena wamkazi.  Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi ikhale nsembe yopsereza, inayo ikhale nsembe yamachimo. Pamenepo wansembe azim’phimbira machimo+ ndipo mkaziyo azikhala woyera.’”

Mawu a M'munsi