Levitiko 21:1-24

21  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Uza ansembe, ana a Aroni, kuti, ‘Aliyense wa inu asadziipitse chifukwa cha munthu amene wamwalira pakati pa anthu a mtundu wake.*+  Koma angathe kudzidetsa ngati womwalirayo ndi wachibale wake wapafupi, mayi ake, bambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi ndi m’bale wake weniweni.  Angathenso kudzidetsa ngati womwalirayo ndi mlongo wake, amene ndi namwali wosakwatiwa ndiponso ndi wachibale wake weniweni.  Asadziipitse chifukwa cha mkazi wa mwini pakati pa anthu amtundu wake ndi kudziipitsa.  Asamete mpala mitu yawo,+ asamete ndevu za m’masaya mwawo+ ndipo asadzitemeteme thupi lawo.+  Azikhala oyera kwa Mulungu wawo+ ndipo asaipitse dzina la Mulungu wawo,+ chifukwa iwowa amapereka nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, mkate wa Mulungu wawo,+ choncho azikhala oyera.+  Wansembe asakwatire hule+ kapena mkazi amene wataya unamwali wake. Asakwatirenso+ mkazi amene mwamuna wake anamusiya ukwati,+ chifukwa wansembeyo ndi woyera kwa Mulungu wake.  Choncho muzim’patula+ chifukwa ndiye wopereka mkate wa Mulungu wanu. Azikhala woyera kwa inu,+ chifukwa ine Yehova, amene ndikukupatulani, ndine woyera.+  “‘Mwana wamkazi wa wansembe akadziipitsa mwa kuchita uhule, pamenepo waipitsa bambo ake. Aziphedwa ndi kutenthedwa.+ 10  “‘Ndipo mkulu wa ansembe wokhala pakati pa abale ake ansembe, wodzozedwa mafuta pamutu pake,+ ndi kupatsidwa mphamvu* kuti avale zovala zaunsembe,+ asalekerere tsitsi lake osalisamala+ ndipo asang’ambe zovala zake.+ 11  Iye asayandikire munthu wakufa+ ndipo asadziipitse bambo ndi mayi ake akamwalira. 12  Asatuluke m’malo opatulika ndipo asadetse malo opatulika a Mulungu wake,+ chifukwa pamutu pake pali chizindikiro cha kudzipereka ndi mafuta odzozera a Mulungu wake.+ Ine ndine Yehova. 13  “‘Mkulu wa ansembe akafuna kukwatira, azikwatira namwali.+ 14  Asakwatire mkazi wamasiye kapena amene mwamuna wake anamusiya ukwati, mkazi amene wataya unamwali wake kapena hule, koma azikwatira namwali pakati pa anthu amtundu wake. 15  Asaipitse ana ake pakati pa anthu amtundu wake,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndam’patula.’”+ 16  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 17  “Lankhula ndi Aroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana ako, ku mibadwo yawo yonse, amene ali ndi chilema+ asayandikire malo opatulika kudzapereka mkate wa Mulungu wake.+ 18  Munthu akakhala ndi chilema chilichonse, asayandikire malo opatulika. Kaya akhale wakhungu, wolumala, wamphuno yokhadzuka, wa chiwalo chimodzi chachitali kwambiri kuposa chinzake,+ 19  wovulala phazi kapena dzanja, 20  wanundu, woonda,* wa diso lamatenda, wa nkhanambo, wa zipere kapena wotswanyika mavalo.+ 21  Munthu aliyense mwa ana a Aroni wansembe, amene ali ndi chilema, asayandikire guwa lansembe kudzapereka nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova.+ Iye ali ndi chilema. Asayandikire guwa lansembe kudzapereka mkate wa Mulungu wake.+ 22  Iye angadye mkate wa Mulungu wake kuchokera pa zinthu zopatulika koposa+ ndi pa zinthu zopatulika.+ 23  Koma asayandikire nsalu yotchinga+ ndiponso guwa lansembe,+ chifukwa iye ali ndi chilema.+ Asaipitse malo anga opatulika,+ chifukwa ine ndine Yehova amene ndikuwapatula kuti akhale oyera.’”+ 24  Pamenepo Mose anafotokoza zimenezi kwa Aroni ndi ana ake, ndiponso kwa ana onse a Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Wansembe akanatha kudziipitsa mwa kukhudza mtembo kapena kulira nawo maliro.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.
Apa mwina akunena za munthu wamfupi monyanyira kapena woonda chifukwa cha matenda.