Levitiko 5:1-19

5  “‘Tsopano munthu+ akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo,+ munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo* kuti akachitire umboni za wochimwayo koma iye osapita kukanena,+ ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.  “‘Munthu akakhudza chinthu chodetsedwa, kaya ikhale nyama yakufa yakuthengo, nyama yakufa yoweta, kapena kamodzi mwa tizilombo topezeka tambiri,+ ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake,+ iye ndi wodetsedwa ndipo wapalamula mlandu.+  Munthu akakhudza mosadziwa chodetsa chilichonse chochokera kwa munthu,+ chinthu chilichonse chodetsedwa chimene chingam’chititse kukhala wodetsedwa, koma wadziwa kuti wakhudza chodetsa, pamenepo wapalamula mlandu.  “‘Munthu akalumbira mpaka kulankhula mosalingalira bwino,+ mwa kunena kuti achita choipa+ kapena chabwino, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, koma akadziwa kuti walankhula mosalingalira bwino pa chilichonse chimene walumbira,+ pamenepo wapalamula mlandu pa chimene walumbiracho.  “‘Ndipo akadziwa kuti wapalamula mlandu pa chilichonse mwa zimenezi, pamenepo aziulula+ kuti wachimwa motani.  Ndiyeno azibweretsa kwa Yehova nsembe yake ya kupalamula+ chifukwa cha tchimo limene wachita. Azibweretsa nkhosa yaing’ono yaikazi+ kapena mbuzi yaing’ono yaikazi kuti ikhale nsembe yamachimo. Akatero wansembe aziphimba tchimo la munthuyo.+  “‘Koma ngati sangakwanitse kupereka nkhosa,+ azibweretsa kwa Yehova njiwa ziwiri+ kapena ana awiri a nkhunda kuti zikhale nsembe za kupalamula chifukwa cha tchimo limene wachita. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo+ ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.  Pamenepo azizibweretsa kwa wansembe, ndipo wansembeyo azipereka nsembe yamachimo choyamba, ataicheka+ pakhosi koma osaduliratu mutu wake.  Kenako azidontheza ena mwa magazi a nsembe yamachimo m’mbali mwa guwa lansembe, koma magazi otsalawo aziwathira pansi pa guwa lansembelo.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10  Mbalame inayo aziipereka ngati nsembe yopsereza motsatira ndondomeko ya nthawi zonse.+ Choncho wansembe aziphimba machimo+ amene munthuyo wachita, ndipo azikhululukidwa.+ 11  “‘Koma ngati sangakwanitse+ kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.*+ Azibweretsa ufa umenewu monga nsembe yake chifukwa cha tchimo limene anachitalo, kuti ukhale nsembe yamachimo. Asauthire mafuta+ ndipo asaikemo lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 12  Akatero azibweretsa ufawo kwa wansembe, ndipo wansembeyo autape kudzaza dzanja limodzi kuti ukhale chikumbutso+ cha nsembeyo. Kenako autenthe paguwa lansembe pamene pali nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 13  Ndiyeno wansembeyo aziphimba+ tchimo limene munthuyo wachita. Aziphimba tchimo lililonse mwa machimo amenewa, ndipo azikhululukidwa. Ufa wotsalawo uzikhala wa wansembe+ mofanana ndi nsembe yambewu.’” 14  Pamenepo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 15  “Munthu akachita mosakhulupirika mwa kuchimwira zinthu zopatulika za Yehova+ mosadziwa, pamenepo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yake ya kupalamula.+ Nkhosayo mtengo wake uzikhala masekeli* asiliva+ ofanana ndi sekeli la kumalo oyera* kuti ikhale nsembe ya kupalamula. 16  Ndiyeno chifukwa choti wachimwira malo oyera azilipira mwa kubweza zinthu zopatulikazo ndiponso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu+ a malipirowo. Malipirowo aziwapereka kwa wansembe, ndipo mwa kupereka nkhosa ya nsembe ya kupalamula, wansembeyo aziphimba machimo+ a munthuyo ndipo azikhululukidwa.+ 17  “Munthu akachimwa mwa kuchita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite, ngakhale kuti anachita mosazindikira,+ komabe wapalamula mlandu, pamenepo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho.+ 18  Azibweretsa kwa wansembe nkhosa yopanda chilema kuti ikhale nsembe ya kupalamula.+ Mtengo wa nkhosayo uzikhala wofanana ndi mtengo wake woikidwiratu. Ndiyeno wansembe aziphimba machimo+ a munthuyo chifukwa cha cholakwa chimene wachita mosadziwa, ngakhale kuti sanazindikire zotsatira zake, ndipo azikhululukidwa.+ 19  Imeneyi ndi nsembe ya kupalamula. Munthu ameneyo wapalamula mlandu+ kwa Yehova.”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “temberero.” Popereka chilengezo chimenechi ankatchulanso temberero kwa wochimwayo kapena mboni imene ikudziwa za nkhaniyo ngati italephera kudzapereka umboni wake.
“Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi muyezo wokwana pafupifupi kilogalamu imodzi.
“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 30:13.