Levitiko 24:1-23

24  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Lamula ana a Isiraeli kuti akupezere mafuta ounikira+ oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale iziyaka nthawi zonse.+  Aroni azikhazika nyale pamalo ake, kunja kwa nsalu yotchinga ya Umboni m’chihema chokumanako. Nyaleyo iziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka m’mawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale m’mibadwo yanu yonse.  Nyalezo+ azikhazike pachoikapo nyale+ chagolide woyenga bwino, ndipo zizikhala pamaso pa Yehova nthawi zonse.+  “Ndiyeno utenge ufa wosalala ndi kuphika mikate 12 yozungulira yoboola pakati. Mkate uliwonse uzipangidwa ndi ufa wokwanira magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.  Ndipo usanjikize mikateyo m’magulu awiri. Gulu lililonse likhale ndi mikate 6.+ Uike mikateyo patebulo lagolide woyenga bwino pamaso pa Yehova.+  Pagulu lililonse la mikateyo uike lubani weniweni. Lubaniyo aziperekedwa nsembe yotentha ndi moto kwa Yehova monga chikumbutso+ choimira mkate.  Sabata lililonse azikhazika mkatewo pamaso pa Yehova, ndipo uzikhala pamenepo nthawi zonse.+ Limeneli ndi pangano pakati pa ine ndi ana a Isiraeli mpaka kalekale.  Mkatewo uzikhala wa Aroni ndi ana ake,+ ndipo aziudyera m’malo oyera,+ chifukwa wapatsidwa kwa iye monga chinthu choyera koposa kuchokera pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale.” 10  Ndiyeno panali mnyamata wina amene mayi wake anali Mwisiraeli, koma bambo wake anali Mwiguputo.+ Mnyamatayu analowa pakati pa ana a Isiraeli ndipo anayamba kulimbana ndi Mwisiraeli+ wina mumsasa. 11  Kenako mnyamatayo anayamba kunyoza ndi kutukwana+ dzina la Mulungu.+ Chotero anabwera naye kwa Mose.+ Dzina la mayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani. 12  Ndiyeno anam’tsekera+ kudikira kuti Yehova awauze zochita naye.+ 13  Pamenepo Yehova analankhula ndi Mose kuti: 14  “Munthu wotemberera dzina la Mulungu uja, mum’tulutsire kunja kwa msasa.+ Onse amene anamumva aike manja awo+ pamutu pake ndipo khamu lonse lim’ponye miyala.+ 15  Ndiyeno uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu aliyense wotemberera Mulungu wake, aziyankha mlandu wa tchimo lake. 16  Wonyoza dzina la Yehova aziphedwa ndithu.+ Khamu lonse lizim’ponya miyala. Kaya ndi mlendo wokhala pakati panu kapena nzika, aziphedwa chifukwa chonyoza Dzinalo.+ 17  “‘Munthu aliyense amene wakantha ndi kupheratu mnzake, nayenso aziphedwa ndithu.+ 18  Munthu amene wakantha ndi kupha chiweto cha mnzake, azibweza chiweto china, chiweto kulipira chiweto.+ 19  Munthu akapundula mnzake, zimene wachitira mnzakezo iyenso muzim’chitira zomwezo.+ 20  Kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Mmene wapundulira mnzake nayenso muzim’pundula chimodzimodzi.+ 21  Wokantha ndi kupheratu chiweto cha mnzake+ azilipira,+ koma wokantha ndi kupha munthu nayenso aziphedwa.+ 22  “‘Chigamulo chilichonse chigwire ntchito mofanana pakati panu, kwa mlendo wokhala pakati panu ndi kwa nzika,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+ 23  Kenako Mose anafotokoza zimenezi kwa ana a Isiraeli, ndipo iwo anatulutsa munthu wotemberera uja kunja kwa msasa ndi kum’ponya miyala.+ Motero ana a Isiraeli anachita zonse monga mmene Yehova analamulira Mose.

Mawu a M'munsi