Levitiko 6:1-30

6  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Munthu akachimwa mwa kuchita mosakhulupirika kwa Yehova+ chifukwa wanyenga+ mnzake pa chinthu chimene chili m’manja mwake, kapena chimene mnzake wam’sungitsa,+ kapena wafwamba mnzake, kapena wam’bera mwachinyengo,+  kapena watola chinthu chotayika+ koma akukana kuti sanachitole, ndipo walumbira monama+ pa chilichonse chimene munthu angachite n’kuchimwa nacho,  iye akachimwa mwa njira imeneyi, ndipo wapalamuladi,+ azibweza zinthu zimene anafwambazo, kapena zinthu zimene analanda mwachinyengo, kapena chimene chili m’manja mwake chimene anam’sungitsa, kapena chinthu chotayika chimene anatola,  kapena chilichonse chimene angalumbirire monama. Azibweza+ chinthucho ndi kuwonjezerapo limodzi mwa magawo ake asanu. Iye azibweza zimenezi kwa mwiniwake, tsiku limene kulakwa kwake kwatsimikizidwa.  Monga nsembe yake ya kupalamula, azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo yopanda chilema.+ Azipereka kwa wansembe nkhosa ya mtengo wofanana ndi mtengo umene wagamulidwa, kuti ikhale nsembe ya kupalamula.+  Ndiyeno wansembe aziphimba machimo+ a munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo azikhululukidwa chilichonse mwa zonse zimene angachite zom’palamulitsa.”  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Lamula Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza+ lili motere: Nsembe yopsereza izikhala pamoto, paguwa lansembe, usiku wonse kufikira m’mawa, ndipo moto wa paguwapo uzisonkhezeredwa. 10  Ndiyeno wansembe azivala zovala zake zogwirira ntchito,+ ndi kuvala kabudula wansalu+ wobisa thupi lake. Kenako azichotsa phulusa losakanizika ndi mafuta,+ la nsembe yopsereza imene izitenthedwa pamoto wa paguwa nthawi zonse, ndipo aziika phulusalo pambali pa guwa lansembe. 11  Ndiyeno azivula zovalazo+ ndi kuvala zina. Akatero, azitenga phulusa losakanizika ndi mafutalo kupita nalo kumalo oyera, kunja kwa msasa.+ 12  Ndipo moto wa paguwa lansembe uziyaka nthawi zonse. Usamazime. Wansembe aziponyapo nkhuni+ m’mawa uliwonse ndi kuikapo nsembe yopsereza pankhunipo. Akatero, azitentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamotopo.+ 13  Motowo+ uziyaka nthawi zonse paguwa lansembe. Usamazime. 14  “‘Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ lili motere: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe. 15  Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi, ndi kutengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, azizitentha paguwa lansembe kuti zikhale fungo la chikumbutso,+ lokhazika mtima pansi, kwa Yehova. 16  Aroni ndi ana ake azidya zotsala za nsembe imeneyi.+ Azipanga mkate wopanda chofufumitsa+ ndi kudya mkatewo m’malo oyera. Aziudyera m’bwalo la chihema chokumanako. 17  Pophika, musaikemo chofufumitsa chilichonse.+ Ndaupereka monga gawo lawo kuchokera pansembe zanga zotentha ndi moto.+ Zimenezi n’zopatulika+ koposa mofanana ndi nsembe yamachimo ndi nsembe ya kupalamula. 18  Mwamuna aliyense+ mwa ana a Aroni azidya mkatewo. Limeneli ndi gawo lawo lochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale.+ Chilichonse chimene chingakhudze nsembezi chidzakhala choyera.’” 19  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 20  “Aroni ndi ana ake apereke nsembe+ iyi kwa Yehova monga nsembe yambewu: ufa wosalala+ wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ Hafu imodzi m’mawa ndipo hafu inayo madzulo. Aliyense wa iwo azichita zimenezi nthawi zonse pa tsiku la kudzozedwa kwake.+ 21  Nsembeyo ikhale yosakaniza ndi mafuta, yophika m’chiwaya.+ Ikhale yosakaniza bwino ndi mafuta. Upereke mitanda ya nsembe yambewu monga fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. 22  Ndipo wansembe, amene adzadzozedwa kulowa m’malo mwake, wochokera pakati pa ana ake,+ azipereka nsembeyo. Azitentha nsembe yonseyo kuti ikhale nsembe+ yoperekedwa kwa Yehova. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 23  Nsembe iliyonse yambewu ya wansembe+ izitenthedwa yonse. Siiyenera kudyedwa.” 24  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti: 25  “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yamachimo+ lili motere: Nyama ya nsembe yamachimo iziphedwa pamaso pa Yehova, pamalo+ ophera nyama ya nsembe yopsereza nthawi zonse. Chimenechi ndi chinthu chopatulika koposa.+ 26  Wansembe amene waipereka monga nsembe yamachimo aziidya.+ Aziidyera kumalo oyera,+ m’bwalo+ la chihema chokumanako. 27  “‘Chilichonse chimene chingakhudze mnofu wake chidzakhala choyera,+ ndipo ngati munthu wadonthezera ena mwa magazi a nyamayo pachovala,+ chovala chimene wadonthezera magazicho muzichichapira kumalo oyera.+ 28  Ndipo chiwiya chadothi+ chimene mungawiritsiremo nyamayo muzichiswa. Koma mukawiritsira m’chiwiya chamkuwa, muzichikwecha ndi kuchitsukuluza ndi madzi. 29  “‘Mwamuna aliyense amene ndi wansembe azidya nyamayo.+ Ndi yopatulika koposa.+ 30  Koma musadye nyama ya nsembe yamachimo imene ena mwa magazi+ ake adzalowa nawo m’chihema chokumanako kuti aphimbire machimo m’malo oyerawo. Imeneyo muziitentha ndi moto.

Mawu a M'munsi