Levitiko 25:1-55

25  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose paphiri la Sinai kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Mukakalowa m’dziko limene ndikukupatsani,+ muzikapumitsa dzikolo ndi kulisungitsa sabata la Yehova.+  Kwa zaka 6 muzilima minda yanu, ndipo m’zaka 6 zomwezo muzidulira mitengo yanu ya mpesa ndi kukolola mbewu zanu.+  Koma m’chaka cha 7 dzikolo lizisunga sabata lopuma pa zonse,+ sabata la Yehova. Musalime minda yanu, ndipo musatengulire mitengo yanu ya mpesa.  Musakolole mbewu zomera zokha zochokera pa zimene munakolola chaka chapita, ndipo musakololenso mphesa za m’mitengo yanu yosadulirayo. M’chaka chimenecho dziko lizipumula pa zonse.  Ndipo inuyo, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, waganyu wanu, mlendo wokhaliratu amene akukhala pakati panu, ndi alendo ena okhala m’nyumba mwanu, muzidya zimene zamera m’chaka cha sabatacho.  Zimene zamerazo zikhalenso chakudya cha ziweto zanu ndi zilombo zakutchire. Mbewu zonse zomera zokha zikhale chakudya.  “‘Muziwerenga masabata 7 azaka, zaka 7 kuchulukitsa maulendo 7. Masiku onse a masabata 7 azaka azikwana zaka 49.  Ndipo m’mwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo,+ muziliza lipenga la nyanga ya nkhosa lolira mokwera kwambiri.+ Muziliza lipenga la nyanga ya nkhosalo m’dziko lanu lonse pa tsiku lochita mwambo wophimba machimo.+ 10  Chaka cha 50 chizikhala chopatulika, ndipo muzilengeza ufulu* kwa anthu onse okhala m’dzikolo.+ Chizikhala Chaka cha Ufulu+ kwa inu, ndipo aliyense wa inu azibwerera kumalo ake ndi kubanja lake.+ 11  Chaka cha 50 ndi Chaka cha Ufulu kwa inu.+ Musalime minda yanu kapena kukolola mbewu zomera zokha, kapenanso kukolola mphesa za m’mitengo yosadulirayo.+ 12  Chimenecho ndi Chaka cha Ufulu. Chizikhala chopatulika kwa inu. Mutha kudya zimene zamera m’minda yanu.+ 13  “‘M’Chaka cha Ufulu chimenechi, aliyense wa inu azibwerera kumalo ake.+ 14  Ukamagulitsa malonda kwa mnzako kapena kugula zinthu kwa mnzako, musamachitirane chinyengo.+ 15  Ukamagula malo kwa mnzako, uziwerenga zaka zimene zapitapo kuchokera m’Chaka cha Ufulu. Azikugulitsa malowo mogwirizana ndi zaka zimene udzakhala ukukololapo.+ 16  Ngati zaka zimene udzakhala ukukololapo n’zambiri, azikugulitsa pa mtengo wokwera,+ koma ngati zakazo zili zochepa azitsitsa mtengo wa malowo, chifukwa akukugulitsa mbewu zimene udzakhala ukukololapo. 17  Musamachitirane chinyengo,+ ndipo muziopa Mulungu wanu,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ 18  Muzisunga malangizo anga ndi zigamulo zanga. Mukatero mudzakhala otetezeka m’dzikolo.+ 19  Dzikolo lidzakupatsani zipatso zake.+ Mudzadya ndi kukhuta, ndipo mudzakhala otetezeka mmenemo.+ 20  “‘Mwina munganene kuti: “Popeza sitidzalima minda yathu ndi kukolola mbewu zathu, tidzadya chiyani m’chaka cha 7?”+ 21  Dziwani kuti ndidzakudalitsani m’chaka cha 6, ndipo dzikolo lidzakupatsani chakudya cha zaka zitatu.+ 22  Mudzalima minda yanu m’chaka cha 8, ndipo mudzakhala mukudyabe chakudya chimene munakolola chija kufikira m’chaka cha 9. Mudzadya chakalecho kufikira mutakololanso china. 23  “‘Choncho musamagulitsiretu malo anu mpaka kalekale+ chifukwa dzikolo ndi langa.+ Kwa ine, inu ndinu alendo m’dziko langa.+ 24  Ndipo m’dziko lanu lonselo, munthu azikhala ndi ufulu wogulanso malo ake.+ 25  “‘M’bale wanu akasauka n’kugulitsa ena mwa malo ake, wowombola amene ndi wachibale wake wapafupi azibwera ndi kugulanso zimene m’bale wakeyo anagulitsa.+ 26  Munthu akakhala wopanda womuwombola, koma wapanga phindu lalikulu ndipo wapeza ndalama moti atha kuwombola malo ake, 27  aziwerenga zaka zimene zapitapo kuchokera pamene anagulitsa malowo, ndipo azibweza ndalama zotsala kwa munthu amene anagula malowo. Akatero azibwerera kumalo akewo.+ 28  “‘Koma ngati munthu wogulitsa malo sanapeze ndalama zoti angabwezere kwa wogulayo, malo amene anagulitsawo apitirizebe kukhala a munthu amene anawagulayo kufikira Chaka cha Ufulu.+ M’chaka chimenecho malowo azibwezedwa kwa mwiniwake ndipo wogulitsa maloyo azibwerera kumalo akewo.+ 29  “‘Munthu akagulitsa nyumba mumzinda wokhala ndi linga, azikhala ndi ufulu woiwombola chaka chimodzi chisanathe kuchokera pamene anaigulitsa. Azikhala ndi ufulu umenewu+ kwa chaka chathunthu. 30  Koma ngati sanaiwombole chaka chimodzicho chisanathe, nyumba imene ili mumzinda wokhala ndi linga izikhala ya wogulayo mpaka kalekale, m’mibadwo yake yonse, ndipo isabwezedwe m’Chaka cha Ufulu. 31  Koma nyumba zimene zili m’midzi yopanda linga zizitengedwa monga mbali ya munda wa kunja kwa mzinda. Ufulu woiwombola+ uzikhalapobe, ndipo m’Chaka cha Ufulu+ izibwezedwa kwa mwiniwake. 32  “‘M’mizinda ya Alevi, Aleviwo azikhala ndi ufulu wowombola nyumba zawo za m’mizindamo mpaka kalekale.+ 33  Ndipo ngati Mlevi anagulitsa nyumba mumzinda wawo ndipo sanaiwombole, izibwezedwa kwa Mleviyo m’Chaka cha Ufulu.+ Zizikhala choncho chifukwa nyumba za m’mizinda ya Alevi pakati pa ana a Isiraeli ndi za Aleviwo basi.+ 34  Komanso, asagulitse malo odyetserako ziweto+ ozungulira mizinda yawo, chifukwa amenewo ndi malo awo mpaka kalekale. 35  “‘M’bale wanu akasauka pakati panu+ ndipo sangathe kudzisamala, muzim’thandiza.+ Iye ayenera kukhala ndi moyo mmene mlendo wokhala pakati panu+ alili ndi moyo. 36  Musamalandire chiwongoladzanja kwa iye kapena kumukongoza mwa katapira,*+ koma muziopa Mulungu wanu.+ Mnansi wanu ayenera kukhala ndi moyo pakati panu. 37  Musam’kongoze ndalama kuti adzabweze chiwongoladzanja,+ ndipo musakongoze chakudya chanu mwa kuchititsa katapira. 38  Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo, kuti ndikupatseni dziko la Kanani.+ Ndinachita izi kuti ndikusonyezeni kuti ine ndine Mulungu wanu.+ 39  “‘M’bale wanu akasauka pakati panu n’kudzigulitsa kwa inu,+ musam’gwiritse ntchito ngati kapolo.+ 40  Mum’tenge ngati waganyu,+ ndiponso ngati mlendo. Akutumikireni kufikira Chaka cha Ufulu. 41  M’chaka chimenecho iye ndi ana ake amasuke ndi kubwerera kwa achibale ake. Abwerere kumalo a makolo ake.+ 42  Pakuti ana a Isiraeli ndi akapolo anga amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ Asamadzigulitse mmene amadzigulitsira akapolo. 43  Musamupondereze ndi kumuchitira nkhanza,+ ndipo muziopa Mulungu wanu.+ 44  Kapolo wanu wamwamuna ndi kapolo wanu wamkazi azichokera ku mitundu yokuzungulirani. Muzigula kapolo wamwamuna kapena wamkazi kuchokera ku mitundu imeneyi. 45  Muzigulanso akapolo kuchokera kwa ana a alendo okhala pakati panu,+ ndi ku mabanja okhala pakati panu, amene ana a alendowo anaberekera m’dziko lanu. Muzigula amenewa kuti akhale akapolo anu. 46  Ndipo akapolowa muzisiyira ana anu monga cholowa chawo mpaka kalekale.+ Amenewa ndiwo azikhala akapolo* anu, koma abale anu, ana a Isiraeli, musawapondereze ndi kuwachitira nkhanza.+ 47  “‘Mlendo wokhala pakati panu akalemera, ndipo m’bale wanu amene akukhala naye pafupi wasauka, moti wakadzigulitsa kwa mlendoyo, kapena kwa wina wa m’banja la mlendoyo, 48  m’bale wanuyo azikhalabe ndi ufulu wowomboledwa.+ Mmodzi mwa abale ake angathe kumuwombola.+ 49  Komanso m’bale wa bambo ake, mwana wa m’bale wa bambo akewo, wachibale wake aliyense wapafupi,+ kapena kuti aliyense wa m’banja lake angathe kumuwombola. “‘Kapenanso mwiniwakeyo akalemera, azidziwombola.+ 50  Iye aziwerengera wom’gulayo zaka zotsala kuchokera pamene anadzigulitsa kukafika Chaka cha Ufulu,+ ndipo ndalama zimene anam’gulira zizigwirizana ndi kuchuluka kwa zaka.+ Azim’gwirira ntchito mofanana ndi waganyu.+ 51  Ngati kwatsala zaka zochuluka, ndalama zake zodziwombolera zizigwirizana ndi zaka zimene zatsala, kuchotsera pa ndalama zimene anam’gulira. 52  Koma ngati kwatsala zaka zochepa kuti Chaka cha Ufulu chifike,+ aziwerenga zaka zotsalazo, ndipo azipereka ndalama zodziwombolera zogwirizana ndi zaka zotsalazo. 53  Azim’gwirira ntchito mofanana ndi waganyu+ chaka ndi chaka. Asamamupondereze ndi kumuchitira nkhanza+ pamaso panu. 54  Koma ngati sangathe kudziwombola mwa njira imeneyi, azimasuka m’Chaka cha Ufulu,+ iye pamodzi ndi ana ake. 55  “‘Pakuti kwa ine ana a Isiraeli ndi akapolo. Ndi akapolo anga+ amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “kumasulidwa kwa akapolo.”
Onani mawu a m’munsi pa Eks 22:25.
Mawu ake enieni, “antchito.”