Levitiko 20:1-27

20  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli, ndiponso mlendo aliyense wokhala mu Isiraeli, wopereka mwana wake aliyense kwa Moleki,*+ aziphedwa ndithu. Nzika za m’dziko lanu zizimupha mwa kum’ponya miyala.  Ine ndidzam’kana* munthu ameneyo, ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake,+ chifukwa wapereka mwana wake kwa Moleki kuti aipitse malo anga oyera+ ndi kuipitsa dzina langa loyera.+  Koma nzikazo zikanyalanyaza mwadala munthu ameneyo mwa kusamupha+ pamene wapereka aliyense mwa ana ake kwa Moleki,  pamenepo ineyo ndidzam’kana munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake,+ ndipo ndidzamupha pamodzi ndi onse ogwirizana naye pochita chiwerewere+ ndi Moleki, kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.  “‘Munthu wotembenukira kwa olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo,+ komwe n’kuchita mosakhulupirika kwa ine,* ndidzam’kana ndithu ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+  “‘Choncho mudzipatule monga anthu oyera,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.  Muzisunga malamulo anga.+ Ine ndine Yehova amene ndikukupatulani monga anthu oyera.+  “‘Munthu akatemberera bambo ndi mayi ake,+ aziphedwa ndithu.+ Iye watemberera bambo ndi mayi ake. Mlandu wa magazi ake ukhale wa iye mwini.+ 10  “‘Munthu wochita chigololo ndi mkazi wa munthu wina, wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake.+ Mwamuna ndi mkazi amene achita chigololowo aziphedwa ndithu.+ 11  Mwamuna wogona ndi mkazi wa bambo ake, wavula* bambo ake.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni. 12  Mwamuna akagona ndi mpongozi wake wamkazi, onse awiri aziphedwa ndithu.+ Iwo achita chinthu chosemphana ndi chibadwa. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni.+ 13  “‘Mwamuna akagona ndi mwamuna mnzake, mmene mwamuna amagonera ndi mkazi, onse awiri achita chinthu chonyansa.+ Iwo aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni. 14  “‘Mwamuna akakwatira mkazi n’kugonanso ndi mayi a mkaziyo, limenelo ndi khalidwe lotayirira.+ Aziphedwa ndi kutenthedwa,+ onse mwamunayo ndi akaziwo, kuti khalidwe lotayirira+ lisapitirire pakati panu. 15  “‘Mwamuna akagona ndi nyama,*+ aziphedwa ndithu ndipo muziphanso nyamayo. 16  Mkazi akadzipereka kwa nyama kuti agone nayo,+ muzipha mkaziyo ndi nyamayo. Anthu ochita zimenezi aziphedwa ndithu. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni. 17  “‘Mwamuna akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake, n’kugona naye, chimenecho ndi chinthu chochititsa manyazi.+ Chotero onse awiri aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu awo. Iye wavula mlongo wake ndipo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho. 18  “‘Mwamuna akagona ndi mkazi amene ali pa nyengo ya kusamba, onse awiri sanalemekeze magazi ake.+ Choncho onse awiri aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu awo. 19  “‘Usavule m’bale* wa mayi ako+ ndi mlongo wa bambo ako,+ chifukwa wochita zimenezi wavula wachibale wake.+ Aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho. 20  Ndipo mwamuna wogona ndi mkazi wa m’bale wa bambo ake, wavula m’bale wa bambo akewo.+ Mwamuna ndi mkaziyo aziyankha mlandu wa tchimo lawolo. Ayenera kufa kuti asabereke ana.+ 21  Mwamuna akakwatira mkazi wa m’bale wake, wachita chinthu chonyansa.+ Iye wavula m’bale wake. Mwamuna ndi mkaziyo ayenera kufa kuti asabereke ana. 22  “‘Motero inu muzisunga malangizo anga onse+ ndi zigamulo zanga zonse,+ kuti dziko limene ndikukulowetsani kuti mukhalemo lisakusanzeni.+ 23  Ndipo musatsatire mfundo za mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+ 24  N’chifukwa chake ndinakuuzani+ kuti: “Inuyo mudzatenga dzikolo ndipo ine ndidzalipereka m’manja mwanu kuti likhale lanu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndakupatulani kwa anthu a mitundu ina.”+ 25  Muzisiyanitsa nyama yoyera ndi yodetsedwa, mbalame yodetsedwa ndi yoyera.+ Musadziipitse+ ndi nyama, mbalame kapena chilichonse choyenda padziko lapansi, chimene ine ndachipatula kuti musadye pogamula kuti ndi chodetsedwa. 26  Mukhale oyera kwa ine,+ chifukwa ine Yehova ndine woyera.+ Ine ndikukupatulani kwa anthu a mitundu ina kuti mukhale anthu anga.+ 27  “‘Mwamuna kapena mkazi amene amalankhula ndi mizimu kapena amene amalosera zam’tsogolo+ aziphedwa ndithu.+ Aziphedwa mwa kuponyedwa miyala. Mlandu wa magazi awo ukhale wa iwo eni.’”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Le 18:21.
Onani mawu a m’munsi pa Le 17:10.
Mawu ake enieni, “kuchita nawo chiwerewere.”
Onani mawu a m’munsi pa Le 18:6.
Mawu ake enieni, “akapereka umuna wake kwa nyama.”
Onani mawu a m’munsi pa Le 18:13.