Levitiko 18:1-30

18  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+  Musachite+ zimene amachita anthu a ku Iguputo kumene munali kukhala, ndipo musakachite+ zimene amachita m’dziko la Kanani, kumene ndikukulowetsani. Musakatsatire mfundo zawo.  Muzisunga zigamulo zanga+ ndi kutsatira+ mfundo zanga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.  Muzisunga mfundo zanga ndi zigamulo zanga, zimene ngati munthu azitsatira adzakhaladi ndi moyo chifukwa cha mfundo ndi zigamulo zimenezo.+ Ine ndine Yehova.+  “‘Mwamuna aliyense pakati panu asayandikire wachibale wake aliyense kuti am’vule.*+ Ine ndine Yehova.  Usavule bambo ako+ ndi mayi ako. Amenewo ndi mayi ako. Usawavule.  “‘Usavule mkazi wa bambo ako,+ chifukwa kumeneko n’kuvula bambo ako.  “‘Usavule mlongo wako, mwana wamkazi wa bambo ako kapena mwana wamkazi wa mayi ako, kaya wobadwa naye m’banja limodzi kapena wobadwira m’banja lina, usawavule.+ 10  “‘Usavule mwana wamkazi wa mwana wako wamwamuna ndipo usavule mwana wamkazi wa mwana wako wamkazi. Usawavule chifukwa kumeneko n’kudzichititsa manyazi. 11  “‘Usavule mwana wamkazi wa mkazi wa bambo ako, mwana wa bambo ako, chifukwa ameneyo ndi mlongo wako. 12  “‘Usavule mlongo wa bambo ako. Ameneyo ndi wachibale wa bambo ako.+ 13  “‘Usavule m’bale* wa mayi ako, chifukwa ndi wachibale wa mayi ako. 14  “‘Usachitire chipongwe m’bale wa bambo ako mwa kuyandikira mkazi wake kuti um’vule, chifukwa amenewo ndi mayi ako.+ 15  “‘Usavule mpongozi wako wamkazi,+ chifukwa ndi mkazi wa mwana wako. Usam’vule. 16  “‘Usavule mkazi wa m’bale wako,+ chifukwa kumeneko n’kuvula m’bale wako. 17  “‘Ukakwatira mkazi, usavule mwana wake wamkazi.+ Usatenge mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wa mkazi wakoyo kuti um’vule. Usatengenso mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi kuti um’vule. Limeneli ndi khalidwe lotayirira+ chifukwa amenewa ndi achibale. 18  “‘Ukakwatira mkazi usakwatirenso m’bale wake kuti akhale mkazi wako wachiwiri+ ndi kum’vula. Usachite zimenezi pamene mkazi wako ali moyo. 19  “‘Usayandikire mkazi kuti um’vule+ pamene ali wodetsedwa chifukwa cha kusamba+ kwake. 20  “‘Usagone ndi mkazi wa mnzako* n’kukhala wodetsedwa.+ 21  “‘Usalole kuti aliyense mwa ana ako aperekedwe+ kwa Moleki.*+ Usanyoze+ dzina la Mulungu wako mwa njira imeneyi. Ine ndine Yehova.+ 22  “‘Usagone ndi mwamuna+ mmene umagonera ndi mkazi.+ N’chonyansa chimenechi. 23  “‘Usagone ndi nyama iliyonse*+ n’kukhala wodetsedwa, ndipo mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agone nayo.+ Kumeneko n’kuchita zosemphana ndi chibadwa. 24  “‘Musadzidetse ndi chilichonse cha zinthu zimenezi, chifukwa mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu yadzidetsa ndi zonse zimenezi.+ 25  Ndiye chifukwa chake dzikolo n’lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha kulakwa kwake. Pamenepo dzikolo lidzataya anthu ake kunja.+ 26  Motero inu muzisunga mfundo zanga ndi zigamulo zanga.+ Ndipo aliyense wa inu, kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu,+ musachite chilichonse cha zinthu zonyansa zimenezi. 27  Pakuti anthu amene akukhala m’dzikolo musanafikemo inuyo achita zinthu zonyansa zonsezi,+ motero dzikolo n’lodetsedwa. 28  Mukapewa kuchita zimenezi, dziko silidzakusanzani chifukwa choliipitsa mmene lidzasanzira mitundu imene ikukhalamo musanafike inu.+ 29  Aliyense wa inu akadzachita chilichonse mwa zinthu zonse zonyansazi, anthu ochita zimenezi adzaphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu awo.+ 30  Chotero muzisunga malamulo anga kuti musamachite iliyonse mwa miyambo yonyansa imene anthu akhala akuchita inu musanafike.+ Pamenepo mudzapewa kudzidetsa ndi miyamboyo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”

Mawu a M'munsi

Apa akunena za kugonana.
Ameneyu ndi wamkazi.
Mawu ake enieni, “Usapereke umuna wako kwa mkazi wa mnzako.”
Zimenezi ziyenera kuti zinaphatikizapo kupereka ana nsembe.
Mawu ake enieni, “Usapereke umuna wako kwa nyama iliyonse.”