Levitiko 27:1-34

27  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu akapanga lonjezo lapadera+ lopereka munthu mnzake kwa Yehova pa mtengo woikidwiratu,  ngati munthu woperekedwayo ndi wamwamuna, wazaka zapakati pa 20 ndi 60, mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli asiliva 50, pamuyezo wolingana ndi sekeli la kumalo oyera.*  Koma ngati munthuyo ndi wamkazi, mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 30.  Ndipo ngati munthu woperekedwayo ndi wazaka zapakati pa 5 ndi 20, akakhala wamwamuna mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 20, koma akakhala wamkazi mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 10.  Ngati msinkhu wa munthuyo ndi wapakati pa mwezi umodzi ndi zaka zisanu, akakhala wamwamuna mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli asiliva asanu,+ ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli asiliva atatu.  “‘Ndiyeno ngati zaka za munthu woperekedwayo ndi zoyambira pa 60 kupita m’tsogolo, akakhala wamwamuna, mtengo wake woikidwiratu ndi masekeli 15, ndipo akakhala wamkazi ndi masekeli 10.  Koma ngati wolonjezayo ndi wosauka moti sangakwanitse mtengo woikidwiratuwo,+ azikaonetsa munthu woperekedwayo kwa wansembe, ndipo wansembe azinena mtengo wa munthuyo.+ Wansembe adzanena mtengo umene wolonjezayo angakwanitse.+  “‘Koma ngati chopereka chake ndi nyama yonga imene anthu amapereka nsembe kwa Yehova, iliyonseyo imene angapereke kwa Yehova izikhala yopatulika.+ 10  Asaichotse ndi kuikapo ina, ndipo asasinthanitse yabwino ndi yoipa kapena yoipa ndi yabwino. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndiponso imene waisinthanitsa nayo, zizikhala zopatulika. 11  Koma ngati chopereka chake ndi nyama yodetsedwa+ imene anthu sangaipereke nsembe kwa Yehova,+ azikaonetsa nyamayo kwa wansembe.+ 12  Ndipo wansembe azinena mtengo wake. Mtengowo uzidalira mmene nyamayo ilili, kaya ndi yabwino kapena yoipa. Mtengo wa nyamayo+ umene wansembe wanena uzikhala womwewo. 13  Koma ngati akufuna kuiwombola, azipereka mtengo woikidwiratu wa nyamayo ndi kuwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu+ a mtengowo. 14  “‘Munthu akapereka* nyumba yake kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, wansembe aziiona ndi kunena mtengo wake. Mtengowo uzidalira mmene nyumbayo ilili, kaya ndi yabwino kapena ayi.+ Mtengo umene wansembe wanena uzikhala womwewo. 15  Koma wopereka nyumbayo akafuna kuiwombola, azipereka mtengo woikidwiratu wa nyumbayo ndi kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo asanu a mtengowo.+ Akatero azitenganso nyumbayo kukhala yake. 16  “‘Ngati wapereka mbali ina ya munda wake+ kwa Yehova kuti ikhale yopatulika, mtengo wa malowo uzikhala wogwirizana ndi mbewu zimene angabzalepo. Ngati angabzalepo balere wokwanira muyezo umodzi wa homeri,*+ ndiye kuti mtengo wa malowo ndi masekeli asiliva 50. 17  Ngati wapereka mundawo kuyambira m’Chaka cha Ufulu+ kupita m’tsogolo, mtengo wake woikidwiratu uzikhala womwewo, wogwirizana ndi mbewu. 18  Koma ngati wapereka mundawo Chaka cha Ufulu chitadutsa, wansembe azimuwerengera mtengo wake mogwirizana ndi zaka zimene zatsala kukafika m’Chaka cha Ufulu chotsatira, ndipo azichotsera pa mtengo wake woikidwiratu.+ 19  Koma ngati wopereka mundayo angauwombole, azipereka mtengo wake woikidwiratu ndi kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo ake asanu, akatero mundawo uzikhaladi wake.+ 20  Ngati mundawo sanauwombole ndipo wagulitsidwa kwa munthu wina, sangathenso kuuwombola. 21  Ndiyeno pamene mundawo ukubwezedwa m’Chaka cha Ufulu, uziperekedwa kwa Yehova mpaka kalekale.+ Mundawo ndi wopatulika ndipo uzikhala wa wansembe.+ 22  “‘Koma ngati wapatula munda umene anachita kugula kuti ukhale wa Yehova, munda umene sunali wake weniweni,+ 23  wansembe azimuwerengera mtengo wake, malinga ndi zaka zimene zatsala kuti Chaka cha Ufulu chifike, ndipo tsiku lomwelo azipereka mtengo umene wansembe wawerengerawo.+ Ndalamazo ndi zopatulika kwa Yehova.+ 24  M’Chaka cha Ufulu mundawo udzabwezedwa kwa mwiniwake weniweni amene anaugulitsa.+ 25  “‘Mtengo woikidwiratu uliwonse uzikhala wolingana ndi sekeli la kumalo oyera. Sekeli limodzi lizikwana magera* 20.+ 26  “‘Munthu asapatule nyama iliyonse yoyamba kubadwa kuti ikhale yoyera, chifukwa iliyonse yoyamba kubadwa ndi ya Yehova.+ Kaya ndi ng’ombe kapena nkhosa, ndi za Yehova.+ 27  Koma nyama yodetsedwa+ yoyamba kubadwa angaiwombole. Ngati munthu akufuna kuiwombola azipereka mtengo wa nyamayo n’kuwonjezerapo limodzi mwa magawo asanu a mtengowo.+ Koma ngati mwiniwake wa nyamayo saiwombola wansembe aziigulitsa pa mtengo woikidwiratu. 28  “‘Ngati munthu watenga munthu mnzake, nyama kapena munda wake n’kuupatula kuti ukhale woyera kwa Yehova kwamuyaya,* kapena akapereka munthuyo, nyama kapena munda kwa Mulungu kuti auwononge,+ sungagulitsidwe kapena kuwomboledwa.+ Munthu, nyama kapena munda umenewo ndi wopatulika koposa. Zimenezi ndi za Yehova. 29  Munthu aliyense woperekedwa kwa Mulungu kuti awonongedwe sangathe kuwomboledwa.+ Ameneyo aziphedwa ndithu.+ 30  “‘Chakhumi* chilichonse+ cha zinthu za m’dzikolo, kaya ndi zokolola m’munda kapena zipatso za m’mitengo, ndi cha Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova. 31  Ndipo munthu akafuna kuwombola chakhumi chake, azipereka mtengo wa chakhumicho n’kuwonjezerapo gawo limodzi mwa magawo asanu a mtengowo.+ 32  Ng’ombe kapena nkhosa iliyonse ya 10, pa nyama zonse zodutsa pansi pa ndodo,*+ iliyonse ya 10 iziperekedwa kwa Yehova ndipo izikhala yopatulika. 33  Asaifufuze ngati ili yabwino kapena yoipa, ndiponso asaisinthanitse ndi ina. Koma ngati waisinthanitsa ndi nyama ina, zonse ziwiri, yoyambayo ndi imene waisinthanitsa nayo, zizikhala zopatulika.+ Sangathe kuiwombola.’” 34  Amenewa ndiwo malamulo+ amene Yehova anapatsa Mose paphiri la Sinai+ kuti apereke kwa ana a Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 30:13.
Mawu ake enieni, “akapatula.”
“Homeri” imodzi ndi yofanana ndi malita 220.
Onani Zakumapeto 12.
Kapena kuti “kuupereka ku chiwonongeko.”
Kapena kuti “gawo limodzi mwa magawo 10.”
M’busa anali kuwerenga ziweto zake mwa kuzidutsitsa pansi pa ndodo yake.