Levitiko 16:1-34

16  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose pambuyo pa imfa ya ana awiri a Aroni, amene anafa+ chifukwa choonekera pamaso pa Yehova mosavomerezeka.  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni m’bale wako, kuti asamalowe konse m’malo oyera+ kuseri kwa nsalu yotchinga,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, kuopera kuti angafe,+ chifukwa ine ndidzaonekera mu mtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+  “Polowa m’malo oyera,+ Aroni azitenga zotsatirazi: ng’ombe yaing’ono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo,+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.+  Azivala mkanjo wopatulika wowomba,+ kabudula wansalu+ wobisa thupi lake, lamba wansalu wa pamimba,+ ndipo azikulunga kumutu kwake ndi nduwira yansalu.+ Zimenezi ndi zovala zopatulika.+ Iye azivala zimenezi atasamba thupi lonse.+  “Ndiyeno khamu la ana a Isiraeli+ lizim’patsa ana a mbuzi awiri, amphongo, kuti akhale nsembe yamachimo,+ ndi nkhosa yamphongo imodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+  “Ndiponso Aroni azitenga ng’ombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo,+ ndipo aziphimba machimo+ ake+ ndi a nyumba yake.+  “Kenako azitenga mbuzi ziwiri zija ndi kuziimika pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.  Ndipo Aroni azichita maere+ pa mbuzi ziwirizo. Maere amodzi akhale a Yehova, ndipo ena akhale a Azazeli.*+  Ndiyeno Aroni azitenga mbuzi imene maere+ asonyeza kuti ndi ya Yehova, ndipo izikhala nsembe yamachimo.+ 10  Koma mbuzi imene maere asonyeza kuti ndi ya Azazeli, aziiimika yamoyo pamaso pa Yehova kuti aiphimbire machimo. Akatero aziitumiza+ m’chipululu monga ya Azazeli.+ 11  “Choncho Aroni azipereka ng’ombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo, kuti aphimbe machimo ake ndi a nyumba yake. Akatero azipha ng’ombe ya nsembe yake yamachimoyo.+ 12  “Kenako iye azitenga chofukizira+ chodzaza ndi makala amoto ochokera paguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova. Azitenganso zofukiza zonunkhira zabwino kwambiri+ zokwana manja awiri+ odzaza, ndi kulowa nazo kuchipinda, kuseri kwa nsalu yotchinga.*+ 13  Akatero, aziika zofukizazo pamoto umene uli pamaso pa Yehova,+ ndipo utsi wa zofukizazo uzikuta chivundikiro cha Likasa,+ chimene chili pa Umboni,+ kuopera kuti angafe. 14  “Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ng’ombe yamphongoyo,+ ndi kuwadontheza ndi chala chake patsogolo pa chivundikiro, chakum’mawa. Azidontheza+ magaziwo ndi chala chake maulendo 7 patsogolo pa chivundikirocho.+ 15  “Kenako azipha mbuzi ya nsembe yamachimo yoperekera anthuwo,+ n’kulowa ndi magazi ake kuchipinda, kuseri kwa nsalu yotchinga.+ Kumeneko magaziwo+ azichita nawo zimene anachita ndi magazi a ng’ombe yamphongo ija. Azidontheza magaziwo patsogolo pa chivundikiro. 16  “Ndipo aziphimba machimo a malo oyera chifukwa cha zodetsa+ za ana a Isiraeli ndi kusamvera kwawo m’machimo awo onse.+ Zimenezi azichitiranso chihema chokumanako chimene chili pakati pa ana a Isiraeli, amene ndi odetsedwa. 17  “Musamapezeke munthu wina mu chihema chokumanako kuyambira pamene iye walowa m’malo oyera kukaphimba machimo kufikira atatulukamo. Ndipo aziphimba machimo ake,+ a nyumba yake ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.+ 18  “Akatero azituluka ndi kupita kuguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova kuti akaliphimbire machimo. Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ng’ombe yamphongo ndi a mbuzi n’kuwapaka panyanga zonse za guwa lansembe.+ 19  Ena mwa magaziwo aziwadonthezera+ paguwalo ndi chala chake maulendo 7, kuti aliyeretse ku zodetsa za ana a Isiraeli ndi kulipatula. 20  “Akamaliza kuphimbira machimo+ malo oyera, chihema chokumanako ndi guwa lansembe, azibweretsanso mbuzi yamoyo ija.+ 21  Ndipo Aroni aziika manja ake onse+ pamutu pa mbuziyo ndi kuvomereza+ zolakwa zonse+ za ana a Isiraeli ndiponso kusamvera kwawo m’machimo awo onse.+ Zonsezi aziziika pamutu pa mbuzi ija+ ndi kuipereka kwa munthu amene am’sankhiratu+ kuti akaisiye kuchipululu.+ 22  Mbuziyo izinyamula zolakwa zawo zonse+ pamutu pake ndipo aziitumiza kuchipululu.+ 23  “Pamenepo Aroni azilowa m’chihema chokumanako ndi kuvula zovala zake zimene anavala polowa m’malo oyera, n’kuzisiya momwemo.+ 24  Akatero azisamba thupi lonse+ m’malo oyera+ ndi kuvala zovala zake.+ Kenako azituluka kukapereka nsembe yake yopsereza+ ndi nsembe yopsereza ya anthuwo+ ndipo aziphimba machimo ake ndi a anthuwo.+ 25  Ndiyeno azitentha mafuta a nsembe yamachimo paguwa lansembe.+ 26  “Munthu+ amene anapititsa mbuzi ya Azazeli uja+ azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse.+ Akatero angathe kulowa mumsasa. 27  “Koma ng’ombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndi mbuzi ya nsembe yamachimo zimene magazi ake analowa nawo m’malo oyera pokaphimba machimo, azizitulutsira kunja kwa msasa ndipo azitentha pamoto zikopa zake, nyama ndi ndowe zake.+ 28  Munthu amene watentha zimenezi azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, akatero angathe kulowa mumsasa. 29  “M’mwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo,+ muzidzisautsa*+ ndipo aliyense wa inu asamagwire ntchito ina iliyonse,+ kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale.+ 30  Pakuti pa tsiku limeneli machimo anu adzaphimbidwa+ kuti muyesedwe oyera. Mudzakhala oyeretsedwa ku machimo anu onse pamaso pa Yehova.+ 31  Limeneli ndi sabata+ lanu lopumula pa zonse ndipo muzidzisautsa. Limeneli likhale lamulo mpaka kalekale. 32  “Wansembe amene adzadzozedwa+ ndi kupatsidwa mphamvu* kuti atumikire monga wansembe,+ kulowa m’malo+ mwa bambo ake, aziphimba machimo ndipo azivala zovala za nsalu.+ Zovala zimenezo ndi zopatulika.+ 33  Iye aziphimba machimo a malo opatulika+ koposa, chihema+ chokumanako ndi guwa lansembe.+ Aziphimbanso machimo a ansembe ndi a mpingo wonse wa anthu.+ 34  Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale,+ kuti machimo onse a ana a Isiraeli aziphimbidwa kamodzi pa chaka.”+ Motero, iye anachita monga mmene Yehova analamulira Mose.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “mkati mwa nsalu yotchinga.”
“Kudzisautsa” pano kungatanthauze kusala chakudya ndiponso kudzimana zinthu zina.
Onani mawu a m’munsi pa Eks 28:41.