Levitiko 3:1-17

3  “‘Ngati akupereka nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova, ndipo akufuna kupereka ng’ombe yamphongo kapena yaikazi, azipereka yopanda chilema.+  Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu+ pa ng’ombeyo, ndipo aziipha pakhomo la chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni, ansembe, aziwaza magazi ake mozungulira paguwa lansembe.  Pamenepo azipereka mbali ina ya nsembe yachiyanjanoyo monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. Azipereka mafuta+ okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo.+  Aziperekanso impso ziwiri+ ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi,* aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.  Kenako ana a Aroni+ azitentha+ zinthu zimenezi paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yomwe ili pankhuni+ zimene zili pamoto. Imeneyi ikhale nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi+ kwa Yehova.  “‘Ngati akupereka nkhosa kapena mbuzi monga nsembe yachiyanjano kwa Yehova, azipereka yamphongo kapena yaikazi, yopanda chilema.+  Ngati akupereka nkhosa yaing’ono yamphongo monga nsembe yake, aziipereka kwa Yehova.+  Pamenepo aziika dzanja lake pamutu+ pa nkhosayo, ndipo aziipha+ patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero, ana a Aroni aziwaza magazi ake mozungulira guwa lansembe.  Ndipo pansembe yachiyanjanoyo azitengapo mafuta ake ndi kuwapereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto.+ Azichotsa mchira wonse wamafuta+ pafupi ndi fupa la msana ndiponso mafuta okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo.+ 10  Azichotsanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta+ a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 11  Ndipo wansembe azitentha+ zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya,+ kuti chikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. 12  “‘Ngati akupereka mbuzi+ monga nsembe yake, aziibweretsa pamaso pa Yehova. 13  Ndiyeno aziika dzanja lake pamutu pa mbuziyo,+ ndipo aziipha+ patsogolo pa chihema chokumanako. Akatero ana a Aroni, aziwaza magazi ake mozungulira guwa lansembe. 14  Ndipo pambuziyo azitengapo mafuta okuta matumbo, mafuta onse amene ali pamatumbo,+ ndi kuwapereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto. 15  Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo. 16  Ndipo wansembe azitentha zinthu zonsezi paguwa lansembe monga chakudya. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto yafungo lokhazika mtima pansi. Mafuta onse ndi a Yehova.+ 17  “‘Musamadye mafuta kapena magazi+ alionse. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale,* kulikonse kumene mungakhale.’”

Mawu a M'munsi

“Chiwindi” ena amati “mphafa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.