Levitiko 2:1-16

2  “‘Munthu akafuna kupereka nsembe yambewu+ kwa Yehova, nsembe yakeyo izikhala ufa wosalala.+ Azithira mafuta ndi kuika lubani* pa ufawo.  Akatero azibweretsa nsembe yakeyo kwa ana a Aroni, ansembe. Ndipo wansembe azitapa ufa wothira mafutawo pamodzi ndi lubani yense kudzaza dzanja limodzi, ndi kuutentha paguwa lansembe kuti ukhale chikumbutso+ cha nsembeyo. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.  Ndipo zotsala za nsembe yambewu ndi za Aroni ndi ana ake,+ popeza ndi zopatulika koposa,+ zochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.  “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophikidwa mu uvuni, izikhala ya ufa wabwino kwambiri. Muzipereka mkate wozungulira woboola pakati,+ wopanda chofufumitsa, wothira mafuta, kapena timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa,+ topaka mafuta.+  “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika m’chiwaya,+ izikhala ya ufa wabwino kwambiri wothira mafuta, yopanda chofufumitsa.  Muziibenthula zidutswazidutswa ndi kuithira mafuta.+ Imeneyi ndi nsembe yambewu.  “‘Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika mumphika wa mafuta ambiri, izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala ndiponso mafuta.  Ndipo nsembe yambewu yopangidwa moteremu muzibwera nayo kwa Yehova. Muziipereka kwa wansembe, ndipo iye azipita nayo paguwa lansembe.  Kenako wansembe azitengako pang’ono nsembe yambewu kuti ikhale chikumbutso,+ ndipo azitentha zimene watengazo paguwa lansembe. Imeneyi ndi nsembe yotentha ndi moto, yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ 10  Ndipo zotsala za nsembe yambewu ndi za Aroni ndi ana ake, popeza ndi zopatulika koposa zochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+ 11  “‘Nsembe yambewu imene mudzapereka kwa Yehova ikhale yopanda chofufumitsa,+ chifukwa simuyenera kutentha mtanda wofufumitsa wa ufa wokanda ndiponso uchi,* monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova. 12  “‘Zimenezi mudzazipereka kwa Yehova monga nsembe ya zipatso zoyambirira,+ chotero simuyenera kuzibweretsa paguwa lansembe kuti zikhale nsembe yafungo lokhazika mtima pansi. 13  “‘Nsembe yanu iliyonse yambewu muziikoleretsa ndi mchere.+ Musapereke nsembe yanu yambewu yopanda mchere wokukumbutsani pangano+ la Mulungu. Popereka nsembe yanu iliyonse muziperekanso mchere. 14  “‘Ngati mukupereka kwa Yehova nsembe yambewu ya zipatso zoyambirira kucha,+ muzipereka tirigu* wamuwisi wotibula, wokazinga pamoto, kuti akhale nsembe yambewu ya zipatso zanu zoyambirira kucha. 15  Muzithira mafuta ndi kuika lubani pansembeyo. Imeneyi ndi nsembe yambewu.+ 16  Ndipo wansembe azitentha chikumbutso+ cha nsembeyo, kapena kuti, tirigu wotibula uja pang’ono ndi mafuta, pamodzi ndi lubani wake yense, kuti zikhale nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Uchi.” Zikuoneka kuti uwu si uchi wa njuchi koma ndi madzi azipatso, chifukwa ukutchedwa zipatso zoyambirira. (Le 2:12; 2Mb 31:5)
N’kutheka kuti anali kuperekanso balere.