Levitiko 10:1-20

10  Ndiyeno Nadabu ndi Abihu,+ ana a Aroni, aliyense anatenga chofukizira,+ n’kuikamo moto ndi zofukiza+ pamwamba pake. Pamenepo anayamba kupereka zofukiza pamoto wosaloledwa+ ndi Yehova, umene iye sanawalamule.  Atatero, moto unatsika kuchokera kwa Yehova ndi kuwawononga,+ moti anafa pamaso pa Yehova.+  Chotero Mose anauza Aroni kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Anthu amene ali pafupi ndi ine+ ayenera kundiona kukhala woyera,+ ndipo anthu onse azindipatsa ulemerero.’”+ Pamenepo Aroni anangokhala chete.  Zitatero, Mose anaitana Misayeli ndi Elizafana, ana a Uziyeli,+ bambo aang’ono a Aroni, n’kuwauza kuti: “Bwerani muchotse abale anu patsogolo pa malo oyera, mupite nawo kunja kwa msasa.”+  Iwo anabweradi ndi kuwanyamula osawavula mikanjo yawo n’kupita nawo kunja kwa msasa, monga mmene Mose ananenera.  Atatero Mose anauza Aroni ndi ana ake ena, Eleazara ndi Itamara, kuti: “Musalekerere tsitsi lanu osalisamala,+ ndipo musang’ambe zovala zanu kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire khamu lonseli.+ Abale anu, nyumba yonse ya Isiraeli ndiwo alire chifukwa cha kuwononga ndi moto kumene Yehova wachita.  Musachoke pakhomo la chihema chokumanako kuopera kuti mungafe,+ chifukwa mwadzozedwa ndi mafuta odzozera a Yehova.”+ Choncho iwo anachita monga mwa mawu a Mose.  Kenako Yehova anauza Aroni kuti:  “Pamene mukubwera kuchihema chokumanako, iwe ndi ana ako musamamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeretsa,+ kuti mungafe. Limeneli ndi lamulo ku mibadwo yanu yonse mpaka kalekale, 10  kuti muzisiyanitsa pakati pa chinthu chopatulika ndi choipitsidwa ndiponso pakati pa chodetsedwa ndi choyera.+ 11  Kutinso muziphunzitsa ana a Isiraeli+ malamulo onse amene Yehova wanena kwa iwo kudzera mwa Mose.” 12  Ndiyeno Mose analankhula ndi Aroni komanso ndi Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala, kuti: “Tengani nsembe yambewu+ imene yatsala pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, ndipo muidye yopanda chofufumitsa pafupi ndi guwa lansembe, chifukwa nsembeyo ndi yopatulika koposa.+ 13  Mudye nsembeyo m’malo oyera,+ chifukwa ndi gawo lanu komanso ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova. Zimenezi n’zimene ndalamulidwa. 14  Mudyenso nganga ya nsembe yoweyula,*+ ndi mwendo umene ndi gawo lopatulika.+ Muzidyere m’malo oyera, inuyo, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ Muyenera kutero chifukwa zapatsidwa kwa inu monga gawo lanu ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zachiyanjano za ana a Isiraeli. 15  Iwo azibweretsa mwendo wa gawo lopatulika ndi nganga ya nsembe yoweyula,+ pamodzi ndi mafuta a nsembe zotentha ndi moto, kuti woperekayo aziweyule uku ndi uku pamaso pa Yehova. Zimenezi zizikhala gawo lanu+ ndi gawo la ana anu mpaka kalekale, monga mmene Yehova walamulira.” 16  Ndiyeno Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yamachimo,+ koma anaona kuti yonse inali itatenthedwa pamoto. Pamenepo iye anakwiyira Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni amene anatsala, ndipo anati: 17  “N’chifukwa chiyani simunadye nsembe yamachimo m’malo oyera?+ Nsembe imeneyi ndi yopatulika koposa, ndipo Mulungu wakupatsani kuti munyamule zolakwa za khamu lonse, ndi kuphimba machimo a khamu lonseli pamaso pa Yehova.+ 18  Taonani, simunabweretse magazi ake mkati, m’malo oyera.+ Munafunika kudya nsembeyo m’malo oyera, monga mmene Mulungu anandilamulira.”+ 19  Pamenepo, Aroni analankhula ndi Mose kuti: “Lerotu apereka nsembe yawo yamachimo ndi nsembe yawo yopsereza kwa Yehova,+ pamene zinthu izi zikundigwera. Kodi ndikanati ndadya nsembe yamachimo lero, zikanakhala zokhutiritsa pamaso pa Yehova?”+ 20  Mose atamva zimenezi, zinam’khutiritsa.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.