Levitiko 15:1-33

15  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose ndi Aroni, kuti:  “Lankhula ndi ana a Isiraeli kuti, ‘Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda ya kukha+ kumaliseche, nthenda yakeyo ndi yodetsedwa.  Ndipo adzakhala wodetsedwa ndi nthendayo ngati akukha kumaliseche, kapena ngati maliseche ake atsekeka ndi zimene zikukhazo. Zikatere azikhala wodetsedwa.  “‘Bedi lililonse limene munthu wakukhayo angagonepo lizikhala lodetsedwa, ndipo chilichonse chimene angakhalepo chizikhala chodetsedwa.  Komanso munthu wokhudza bedi lakelo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+  Ndipo aliyense wokhala pachinthu chimene wakukhayo anakhalapo, azichapa+ zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.  Aliyense wokhudza thupi la munthu wanthenda yakukhayo+ azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+  Ndipo wanthenda yakukhayo akalavulira munthu woyera, munthu woyerayo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.  Chishalo+ chilichonse chimene wanthenda yakukhayo anakhalapo chizikhala chodetsedwa. 10  Aliyense wokhudza chilichonse chimene munthuyo wakhalapo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo munthu wonyamula zinthu zimenezi azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 11  Aliyense amene munthu wanthenda yakukhayo+ wamukhudza asanasambe m’manja, azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 12  Chiwiya chadothi chimene munthu wanthenda yakukhayo wakhudza chiziswedwa,+ ndipo chikakhala chamtengo+ chizitsukidwa. 13  “‘Ndiyeno munthu akachira nthenda yake yakukhayo, pazipita masiku 7 kuti akhale woyera,+ kenako azichapa zovala zake ndi kusamba madzi otunga kumtsinje,+ ndipo iye azikhala woyera. 14  Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri+ kapena ana awiri a nkhunda ndipo azibwera nazo pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako, ndi kupereka mbalamezo kwa wansembe. 15  Pamenepo wansembe azipereka nsembe mbalamezo, imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza.+ Wansembe azim’phimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha nthenda yake yakukhayo. 16  “‘Mwamuna akatulutsa umuna,+ azisamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 17  Chovala chilichonse ndi chikopa chilichonse chimene pagwera umunawo chizichapidwa, ndipo chizikhala chodetsedwa kufikira madzulo.+ 18  “‘Mkazi akagonana ndi mwamuna, onse awiri azisamba thupi lonse, ndipo azikhala odetsedwa+ kufikira madzulo. 19  “‘Ngati mkazi akukha ndipo zimene akukhazo ndi magazi,+ azikhala masiku 7 ali wodetsedwa+ chifukwa cha kusamba+ kwakeko, ndipo aliyense womukhudza azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 20  Chilichonse chimene angagonepo pamene ali wodetsedwa chifukwa cha kusamba kwake chizikhala chodetsedwa,+ ndiponso chilichonse chimene wakhalapo chizikhala chodetsedwa. 21  Aliyense wokhudza bedi lake azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 22  Aliyense wokhudza chilichonse chimene mkaziyo anakhalapo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ 23  Ndipo ngati mkaziyo anakhala pabedi kapena pachinthu china, wokhudza+ chinthu chimenecho azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 24  Mwamuna akagonana ndi mkazi ameneyu, azikhala wodetsedwa chifukwa chakuti mkaziyo akusamba.+ Zikatero, mwamunayo azikhala wodetsedwa masiku 7, ndipo bedi lililonse limene angagonepo lizikhala lodetsedwa. 25  “‘Mkazi akakha magazi kwa masiku ambiri+ pamene si nthawi yake yokhala wodetsedwa chifukwa cha kusamba,+ kapena akapitiriza kukha magazi nthawi yake yokhala wodetsedwa chifukwa cha kusamba kwake itatha, masiku onse pamene iye akukha magaziwo azikhala ngati mmene amakhalira pa nthawi yake yokhala wodetsedwa chifukwa cha kusamba. Iye ndi wodetsedwa. 26  Bedi lililonse limene angagonepo pa tsiku lililonse mwa masiku amene akukha magaziwo, lizikhala ngati bedi limene amagonapo pa nthawi ya kusamba kwake.+ Ndipo chinthu chilichonse chimene angakhalepo, chizikhala chodetsedwa mmene chingakhalire chodetsedwa pa nthawi ya kusamba kwake. 27  Aliyense wokhudza+ zinthuzo azikhala wodetsedwa, ndipo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo. 28  “‘Akasiya kukha magaziko, pazipita masiku 7, kenako azikhala woyera.+ 29  Ndiyeno pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri+ kapena ana awiri a nkhunda, ndi kubwera nawo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako.+ 30  Pamenepo wansembe azipereka mbalame imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza.+ Wansembe azim’phimbira machimo+ pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwakeko. 31  “‘Muzionetsetsa kuti ana a Isiraeli akupewa choipitsa chilichonse, kuopera kuti angafe chifukwa choipitsa chihema changa chopatulika chimene chili pakati pawo.+ 32  “‘Limeneli ndi lamulo lokhudza mwamuna wanthenda yakukha kumaliseche,+ ndi mwamuna amene watulutsa umuna+ n’kudetsedwa nawo. 33  Lamulo limeneli ndi lokhudzanso mkazi wodetsedwa chifukwa cha kusamba+ kwake, ndi aliyense amene ali ndi nthenda yakukha kumaliseche,+ kaya mwamuna kapena mkazi ndiponso mwamuna wogonana ndi mkazi wodetsedwa.’”

Mawu a M'munsi