Levitiko 7:1-38

7  “‘Lamulo la nsembe ya kupalamula+ lili motere: Nsembeyi ndi yopatulika koposa.+  Nyama ya nsembe ya kupalamula aziiphera pamalo+ amene nthawi zonse amaphera nyama ya nsembe yopsereza, ndipo magazi ake+ aziwazidwa+ mozungulira paguwa lansembe.  Pa mafuta ake onse+ azipereka mchira wamafuta ndi mafuta okuta matumbo.  Aziperekanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.+  Ndipo wansembe azitentha zinthu zimenezi paguwa lansembe monga nsembe yotentha ndi moto yoperekedwa kwa Yehova.+ Imeneyi ndi nsembe ya kupalamula.  Mwamuna aliyense yemwe ndi wansembe azidya nyamayo.+ Azidyera m’malo oyera. Nsembeyi ndi yopatulika koposa.+  Nsembe ya kupalamula ndi yofanana ndi nsembe yamachimo. Zonsezi lamulo lake ndi limodzi.+ Nyama ya nsembe yophimba machimo izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo.  “‘Chikopa+ cha nyama ya nsembe yopsereza, imene munthu aliyense wapereka kwa wansembe, chizikhala cha wansembe amene wapereka nsembeyo.  “‘Nsembe iliyonse yambewu imene ingaphikidwe mu uvuni,+ iliyonse yophika mu mphika wa mafuta ambiri+ ndiponso yophika m’chiwaya+ izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo. Ndithu izikhala yake.+ 10  Koma nsembe yambewu iliyonse yothira mafuta+ kapena youma+ izikhala ya ana onse aamuna a Aroni, azigawana mofanana. 11  “‘Tsopano lamulo la nsembe yachiyanjano+ imene aliyense azipereka kwa Yehova lili motere: 12  Ngati akupereka nsembeyo posonyeza kuyamikira,+ pamenepo azipereka nsembe yoyamikira pamodzi ndi mkate wozungulira woboola pakati, wopanda chofufumitsa, wothira mafuta. Aziperekanso timitanda ta mkate topyapyala topanda chofufumitsa, topaka mafuta,+ ndi mkate wozungulira woboola pakati, wothira mafuta, wophika ndi ufa wosalala wosakaniza bwino kwambiri ndi mafuta. 13  Popereka nsembe zachiyanjano, zimene ndi nsembe yoyamikira pamodzi ndi nsembe yake ya mkate, aziperekanso makeke okhala ndi chofufumitsa,+ ozungulira oboola pakati. 14  Ndipo pa zimenezi azipereka mtanda umodzi wa nsembe iliyonse kuti ikhale gawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova.+ Mtandawo uzikhala wa wansembe+ amene wawaza magazi a nsembe zachiyanjanozo paguwa lansembe. 15  Nyama ya nsembe zachiyanjano zoperekedwa monga nsembe yoyamikira aziidya pa tsiku limene waipereka. Asasunge iliyonse ya nyamayo kufika m’mawa.+ 16  “‘Ngati akupereka lonjezo+ monga nsembe yake kapena ngati akupereka nsembe yaufulu,+ aziidya pa tsiku limene wapereka nsembeyo, ndipo angathenso kudya imene yatsala pa tsiku lotsatira. 17  Nyama ya nsembeyo, imene yatsala kufika tsiku lachitatu, ayenera kuitentha ndi moto.+ 18  Koma ngati nyama iliyonse ya nsembe yachiyanjano yadyedwa pa tsiku lachitatu, wopereka nsembeyo sadzayanjidwa ndi Mulungu.+ Nsembe yakeyo sadzapindula nayo.+ Idzakhala chinthu chonyansa, ndipo amene wadyako nsembeyo adzadziyankhira mlandu wa cholakwa chake.+ 19  Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa,+ siyenera kudyedwa. Muziitentha ndi moto. Koma nyama imene sinadetsedwe, aliyense woyera angathe kuidya. 20  “‘Munthu amene wadya nyama ya nsembe yachiyanjano, imene ndi ya Yehova, pamene munthuyo ali wodetsedwa, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 21  Ndipo munthu akakhudza chodetsa chilichonse, kaya chodetsa cha munthu+ kapena nyama yodetsedwa,+ kapenanso chinthu chilichonse chonyansa chodetsedwa,+ n’kudyako nyama ya nsembe yachiyanjano, imene ndi ya Yehova, munthu wotero aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’” 22  Ndipo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 23  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Musamadye mafuta+ alionse a ng’ombe, a mwana wa nkhosa, kapena a mbuzi. 24  Mafuta a nyama yofa yokha ndi mafuta a nyama yokhadzulidwa ndi chilombo,+ mungawagwiritse ntchito ina iliyonse imene mungafune, koma musawadye ngakhale pang’ono. 25  Pakuti aliyense wodya mafuta a nyama imene waipereka kwa Yehova monga nsembe yotentha ndi moto, munthu ameneyo aziphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake. 26  “‘Musamadye magazi+ alionse kulikonse kumene mungakhale, kaya akhale magazi a mbalame kapena a nyama. 27  Munthu aliyense wodya magazi alionse aziphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’” 28  Ndipo Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 29  “Lankhula ndi ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu amene akupereka nsembe yake yachiyanjano kwa Yehova, azipereka kwa Yehova mbali ya nsembe yake yachiyanjanoyo.+ 30  Iye azibweretsa mafuta+ pamodzi ndi nganga monga nsembe kwa Yehova yotentha ndi moto. Azibweretsa mafutawo pamodzi ndi nganga kuti aziweyule* uku ndi uku, monga nsembe yoweyula+ yoperekedwa kwa Yehova. 31  Ndiyeno wansembe azitentha mafutawo+ paguwa lansembe, koma ngangayo izikhala ya Aroni ndi ana ake.+ 32  “‘Mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja muziupereka kwa wansembe monga gawo lopatulika+ lochokera pansembe zanu zachiyanjano. 33  Mwana wa Aroni amene wapereka kwa Mulungu magazi a nsembe zachiyanjano ndiponso mafuta, azitenga mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja monga gawo lake.+ 34  Nganga ya nsembe yoweyula+ ndiponso mwendo, umene ndi gawo lopatulika, ndikuzitenga pansembe zachiyanjano za ana a Isiraeli. Ndikuzitenga kwa ana a Isiraeli ndi kuzipereka kwa Aroni wansembe ndi ana ake. Ili ndi lamulo mpaka kalekale. 35  “‘Limeneli ndilo linali gawo la Aroni monga wansembe ndiponso gawo la ana ake monga ansembe. Gawoli linali lochokera pansembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova, malinga ndi zimene anawalamula pa tsiku limene anaperekedwa+ kuti atumikire monga ansembe a Yehova. 36  Pa tsiku lopatula Aroni ndi ana ake pakati pa ana a Isiraeli ndi kuwadzoza,+ Yehova analamula kuti adzawapatse gawoli. Ili ndi lamulo m’mibadwo yawo yonse mpaka kalekale.’”+ 37  Limeneli ndilo lamulo lokhudza nsembe yopsereza,+ nsembe yambewu,+ nsembe yamachimo,+ nsembe ya kupalamula,+ nyama yoperekedwa polonga munthu unsembe+ ndiponso nsembe yachiyanjano,+ 38  monga mmene Yehova analamulira Mose paphiri la Sinai,+ pa tsiku limene analamula ana a Isiraeli kupereka nsembe zawo kwa Yehova m’chipululu cha Sinai.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.