Levitiko 4:1-35

4  Yehova analankhulanso ndi Mose, kuti:  “Uza ana a Isiraeli kuti, ‘Munthu+ akachimwa mosadziwa+ mwa kuchita zinthu zimene Yehova analamula kuti musachite, iye akachita chimodzi mwa zimenezo muzichita izi:  “‘Ngati wansembe, wodzozedwa,+ wachita tchimo+ limene lapalamulitsa anthu onse, azipereka kwa Yehova ng’ombe yaing’ono yamphongo yopanda chilema monga nsembe yamachimo chifukwa cha tchimo lakelo.+  Azibweretsa ng’ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova pakhomo la chihema chokumanako+ ndipo aziika dzanja lake pamutu wa ng’ombeyo,+ kenako aziipha pamaso pa Yehova.  Pamenepo wansembe, wodzozedwayo,+ azitengako pang’ono magazi a ng’ombeyo ndi kulowa nawo m’chihema chokumanako.  Kenako wansembe aziviika chala chake+ m’magaziwo ndi kudontheza pansi ena mwa magaziwo maulendo 7+ pamaso pa Yehova, patsogolo pa nsalu yotchinga ya m’malo oyera.  Wansembeyo azipaka ena mwa magaziwo panyanga+ za guwa lansembe la zofukiza zonunkhira pamaso pa Yehova, limene lili m’chihema chokumanako. Magazi ena onse a ng’ombeyo aziwathira pansi+ pa guwa lansembe zopsereza, limene lili pakhomo la chihema chokumanako.  “‘Koma mafuta onse a ng’ombe ya nsembe yamachimo, aziwachotsa. Azichotsa mafuta okuta matumbo, mafuta onse okuta matumbo.+  Azichotsanso impso ziwiri ndi mafuta okuta impsozo, omwenso ndi mafuta a m’chiuno. Koma mafuta a pachiwindi, aziwachotsa pamodzi ndi impsozo.+ 10  Zinthu zimenezi zizikhala zofanana ndi zomwe azichotsa pa ng’ombe ya nsembe yachiyanjano.+ Ndipo wansembe azizitentha paguwa lansembe zopsereza.+ 11  “‘Koma kunena za chikopa cha ng’ombeyo ndi nyama yake yonse pamodzi ndi mutu wake, ziboda zake, matumbo ake ndi ndowe zake,+ 12  ng’ombe yonseyo aziitenga ndi kupita nayo kunja kwa msasa.+ Azipita nayo kumalo oyera kumene amataya phulusa losakanizika ndi mafuta+ ndipo aziitentha pamoto wa nkhuni.+ Azitentha ng’ombeyo kumalo otayako phulusa losakanizika ndi mafuta. 13  “‘Tsopano ngati khamu lonse la Isiraeli lachita cholakwa,+ mwa kuchita chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite ndipo chawapalamulitsa, koma mpingo wonse sunazindikire kuti walakwa,+ 14  ndipo tchimo limene achitalo ladziwika,+ pamenepo mpingowo uzipereka ng’ombe yaing’ono yamphongo monga nsembe yamachimo, azibwera nayo pakhomo la chihema chokumanako. 15  Kumeneko akulu a khamu la Isiraeli aziika manja awo pamutu wa ng’ombeyo+ pamaso pa Yehova, ndipo aziipha pamaso pa Yehova. 16  “‘Pamenepo wansembe, wodzozedwa,+ azibweretsa ena mwa magazi a ng’ombeyo m’chihema chokumanako.+ 17  Ndipo wansembe aziviika chala chake m’magaziwo ndi kuwadontheza pansi maulendo 7 pamaso pa Yehova, patsogolo pa nsalu yotchinga.+ 18  Ena mwa magaziwo aziwapaka panyanga za guwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova, m’chihema chokumanako. Magazi ena onse aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza,+ limene lili pakhomo la chihema chokumanako. 19  Akatero azichotsa mafuta ake onse ndi kuwatentha paguwa lansembe.+ 20  Ng’ombeyo azichita nayo ngati mmene amachitira ndi ng’ombe ya nsembe yamachimo ija. Azichita momwemo. Ndipo wansembe aziwaphimbira machimo+ awo kuti akhululukidwe. 21  Azitenganso ng’ombe ndi kukaitentha kunja kwa msasa monga mmene anatenthera ng’ombe yoyamba ija.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo ya mpingo wonse.+ 22  “‘Ngati mtsogoleri+ wachimwa mwa kuchita mwangozi chimodzi mwa zinthu zimene Yehova Mulungu wake analamula kuti asachite+ ndipo wapalamula, 23  kapena ngati wauzidwa kuti wachimwa mwa kuphwanya lamulo,+ azibweretsa mbuzi yaing’ono yamphongo,+ yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yake. 24  Akatero aziika dzanja lake pamutu+ pa mbuzi yaing’onoyo ndipo aziipha pamaso pa Yehova,+ pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza nthawi zonse. Imeneyi ndi nsembe yamachimo.+ 25  Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimoyo ndi chala chake n’kuwapaka panyanga+ za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza. 26  Mafuta onse a mbuziyo aziwatentha paguwa lansembe mofanana ndi mafuta a nsembe yachiyanjano.+ Pamenepo wansembe aziphimba tchimo la mtsogoleriyo,+ ndipo azikhululukidwa. 27  “‘Ngati munthu aliyense pakati panu wachimwa mwa kuchita mwangozi chimodzi mwa zinthu zimene Yehova analamula kuti asachite ndipo wapalamula,+ 28  kapena ngati wauzidwa kuti wachimwa, azibweretsa mbuzi yaing’ono yaikazi,+ yopanda chilema, kuti ikhale nsembe chifukwa cha machimo akewo. 29  Akatero aziika dzanja lake pamutu+ pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo azipha nyamayo pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza aja.+ 30  Ndiyeno wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake n’kuwapaka panyanga+ za guwa lansembe zopsereza. Magazi ena onse a mbuziyo aziwathira pansi pa guwa lansembe+ zopsereza. 31  Kenako azichotsa mafuta onse+ a mbuziyo, monga mmene amachotsera mafuta a nsembe yachiyanjano.+ Pamenepo wansembe azitentha mafutawo paguwa lansembe kuti likhale fungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova.+ Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo la munthuyo, ndipo azikhululukidwa.+ 32  “‘Koma ngati akubweretsa nkhosa+ monga nsembe yake yamachimo, azibweretsa nkhosa yaing’ono yaikazi yopanda chilema.+ 33  Akatero aziika dzanja lake pamutu pa nyama ya nsembe yamachimoyo ndipo aziipha kuti ikhale nsembe yamachimo, pamalo ophera nyama ya nsembe yopsereza nthawi zonse.+ 34  Wansembe azitenga ena mwa magazi a nyamayo ndi chala chake n’kuwapaka panyanga za guwa lansembe zopsereza.+ Magazi ena onse a nkhosayo aziwathira pansi pa guwa lansembe zopsereza. 35  Ndiyeno azichotsa mafuta onse a nkhosayo, monga mmene amachotsera mafuta a nkhosa yaing’ono yamphongo ya nsembe yachiyanjano. Pamenepo wansembe azitentha zinthu zimenezi paguwa lansembe pamwamba pa nsembe zotentha ndi moto zoperekedwa kwa Yehova.+ Ndipo wansembe aziphimba+ tchimo limene munthuyo wachita, ndipo azikhululukidwa.+

Mawu a M'munsi