2 Samueli 13:1-39

13  Pambuyo pa zinthu zimenezi, zinachitika kuti, Abisalomu+ mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola dzina lake Tamara.+ Ndipo Aminoni+ mwana wa Davide anayamba kukonda kwambiri+ Tamara.  Zimenezi zinam’vutitsa maganizo kwambiri Aminoni, moti anadwala+ chifukwa cha mlongo wake Tamara. Popeza Tamara anali namwali, zinali zovuta kwambiri+ kwa Aminoni kuti achite naye kalikonse.+  Tsopano Aminoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu,+ mwana wa Simeya,+ m’bale wake wa Davide. Yehonadabu anali munthu wanzeru kwambiri.  Ndiyeno Yehonadabu anafunsa Aminoni kuti: “N’chifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu tsiku ndi tsiku umaoneka wosasangalala? Kodi sungandiuze?”+ Pamenepo Aminoni anamuuza kuti: “Ine ndikukonda kwambiri+ Tamara, mlongo+ wa m’bale wanga Abisalomu.”  Atatero, Yehonadabu anamuuza kuti: “Ugone pabedi lako ndi kunamizira kudwala.+ Mosakayikira bambo ako adzabwera kudzakuona, ndipo udzawauze kuti, ‘Chonde lolani kuti mlongo wanga Tamara abwere adzandipatse chakudya monga munthu wodwala. Ndikufuna kuti andipangire chakudya chonditonthoza pamaso panga, ine ndikuona, ndipo ndidye kuchokera m’manja mwake.’”+  Pamenepo Aminoni anagona pansi ndi kunamizira kudwala.+ Zitatero mfumu inabwera kudzamuona ndipo Aminoni anauza mfumuyo kuti: “Chonde, lolani kuti mlongo wanga Tamara abwere adzandiphikire makeke pamaso panga, kuti ndidye chakudya kuchokera m’manja mwake monga wodwala.”  Zitatero, Davide anatumiza uthenga kwa Tamara amene anali kunyumba ndi kumuuza kuti: “Chonde, pita kunyumba ya Aminoni m’bale wako ukamupangire chakudya chomutonthoza.”  Choncho Tamara anapita kunyumba ya Aminoni+ m’bale wake, Aminoniyo atagona. Ndiyeno anatenga ufa ndi kuukanda ndipo kenako anaumba makeke* pamaso pa Aminoni ndi kuwaphika.  Pomalizira, anatenga chiwaya ndi kukhuthula makekewo Aminoni akuona. Koma Aminoni anakana kudya ndipo anati: “Uzani aliyense atuluke!”+ Pamenepo aliyense anatuluka. 10  Ndiyeno Aminoni anauza Tamara kuti: “Bweretsa chakudya chonditonthoza kuchipinda chogona kuti ndidye kuchokera m’manja mwako monga wodwala.” Pamenepo Tamara anatenga makeke amene anapangawo ndi kupita nawo kwa Aminoni m’bale wake m’chipinda chogona. 11  Atamuyandikira kuti adye, Aminoni anamugwira+ ndi kumuuza kuti: “Gona ndi ine+ mlongo wanga.”+ 12  Koma Tamara anamuuza kuti: “Ayi, m’bale wanga! Usandichititse manyazi,+ chifukwa zimenezi n’zachilendo mu Isiraeli.+ Usachite chinthu chopusa, chochititsa manyazi ngati chimenechi.+ 13  Ndipo ine nditani ndi chitonzo chimenechi? Komanso iwe ukhala ngati mmodzi mwa amuna opusa mu Isiraeli. Chonde lankhula ndi mfumu, pakuti sangakuletse kuti unditenge.” 14  Koma Aminoni sanamvere mawu ake. Popeza anali ndi mphamvu zoposa Tamara, anamuchititsa manyazi+ mwa kugona naye.+ 15  Aminoni atachita zimenezo anayamba kudana naye kwambiri. Anadana naye kwambiri kuposa mmene ankamukondera, moti Aminoni anamuuza kuti: “Nyamuka, choka muno!” 16  Pamenepo Tamara anati: “Ayi usatero m’bale wanga. Pakuti kundithamangitsa kumene ukuchitaku n’koipa kwambiri kuposa zimene wandichitazi!” Koma Aminoni sanamvere zimenezo. 17  Pamenepo Aminoni anaitana mtumiki wake womupatsira chakudya n’kumuuza kuti: “Chotsa munthu ameneyu pamaso panga ndi kupita naye panja, ndipo ukhome chitseko akatuluka.” 18  (Tamara anali atavala malaya amizeremizere,+ pakuti umu ndi mmene ana aakazi a mfumu amene anali anamwali anali kuvalira. Iwo anali kuvala malaya akunja odula manja amizeremizere.) Choncho mtumiki wake uja anamutenga ndi kupita naye panja, ndipo atamutulutsa anakhoma chitseko. 19  Kenako Tamara anadzithira phulusa+ kumutu ndi kung’amba malaya ake amizeremizere aja. Ndiyeno anaika manja ake pamutu+ n’kunyamuka kumapita, akulira. 20  Zitatero, m’bale wake Abisalomu+ anamuuza kuti: “Kodi si m’bale wako Aminoni+ amene wakuchitira choipa chimenechi? Tsopano khala chete mlongo wanga. Iyeyo ndi m’bale wako.+ Usadandaule ndi nkhani imeneyi.” Ndiyeno Tamara anayamba kukhala kunyumba ya m’bale wake Abisalomu ndipo sanali kucheza ndi wina aliyense. 21  Tsopano Mfumu Davide anamva zonse zimene zinachitika+ ndipo anakwiya kwambiri.+ 22  Abisalomu sanalankhule chilichonse, chabwino kapena choipa kwa m’bale wake Aminoni, pakuti Abisalomu anadana+ ndi Aminoni chifukwa chochititsa manyazi Tamara mlongo wake. 23  Patapita zaka ziwiri zathunthu, anthu ena anali kumeta ubweya wa nkhosa+ za Abisalomu ku Baala-hazori, pafupi ndi Efuraimu.+ Choncho Abisalomu anaitanira ana onse aamuna a mfumu kumeneko.+ 24  Ndiyeno Abisalomu anapita kwa mfumu ndi kunena kuti: “Ine mtumiki wanu ndili ndi anthu amene akumeta ubweya wa nkhosa! Chonde, ndikupempha kuti inu mfumu ndi atumiki anu mupite pamodzi ndi ine mtumiki wanu.” 25  Koma mfumu inayankha Abisalomu kuti: “Ayi mwana wanga. Tisachite kupita tonse, chifukwa tingakhale mtolo wolemetsa kwa iwe.” Ngakhale kuti Abisalomu anachondererabe,+ mfumu sinalole kupita koma inamudalitsa.+ 26  Pamapeto pake Abisalomu anati: “Ngati inuyo simubwera, chonde lolani kuti Aminoni m’bale wanga apite nafe.”+ Pamenepo mfumu inamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukufuna kuti apite nawe?” 27  Ndiyeno Abisalomu anayamba kumuchonderera,+ moti mfumu inalola kuti Aminoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye. 28  Kenako Abisalomu analamula omutumikira kuti: “Muonetsetse chonde kuti Aminoni akangosangalala mumtima mwake ndi vinyo,+ ine n’kukuuzani kuti, ‘Mukantheni Aminoni!’ pamenepo mumuphe. Musaope.+ Kodi si ndine amene ndakulamulani? Chitani zinthu mwamphamvu ndipo khalani olimba mtima.” 29  Pamenepo atumiki a Abisalomu anachitira Aminoni monga mmene Abisalomuyo anawalamulira.+ Zitatero, ana onse a mfumu ananyamuka ndipo aliyense anakwera nyulu* yake ndi kuthawa. 30  Kenako ana amenewa ali m’njira, uthenga unafika kwa Davide kuti: “Abisalomu wapha ana onse a mfumu ndipo palibe amene watsala.” 31  Mfumu itamva zimenezi inaimirira ndi kung’amba zovala zake+ n’kugona pansi.+ Atumiki ake onse anaimirira pafupi ndi mfumuyo atang’ambanso zovala zawo.+ 32  Koma Yehonadabu+ mwana wa Simeya,+ m’bale wake wa Davide anati: “Inu mbuyanga musaganize kuti ndi ana onse a mfumu amene aphedwa, pakuti ndi Aminoni yekha amene wafa.+ Abisalomu ndi amene walamula zimenezi kuti zichitike pakuti anakonzeratu+ zimenezi kuyambira pa tsiku limene Aminoniyo anachititsa manyazi+ Tamara mlongo wake.+ 33  Tsopano mbuyanga mfumu, musavutike mtima ndi mawu amenewa onena kuti, ‘Ana onse a mfumu afa,’ pakuti ndi Aminoni yekha amene wafa.” 34  Panthawiyi n’kuti Abisalomu atathawa.+ Pambuyo pake mnyamata wina amene anali mlonda,+ anakweza maso ndipo anaona anthu ambiri akubwera kumbuyo kwake mumsewu umene unali m’mphepete mwa phiri. 35  Pamenepo Yehonadabu+ anauza mfumu kuti: “Taonani! Ana a mfumu akubwera. Zachitika monga mwa mawu a mtumiki wanu.”+ 36  Ndiyeno atangomaliza kulankhula, ana a mfumu aja anafika ndipo anayamba kulira mokweza mawu. Mfumu nayonso pamodzi ndi atumiki ake onse analira kwadzaoneni. 37  Koma Abisalomu anathawa ndi kupita kwa Talimai,+ mfumu ya dziko la Gesuri,+ amene anali mwana wamwamuna wa Amihudi. Davide anali kulira+ tsiku ndi tsiku chifukwa cha imfa ya Aminoni mwana wake. 38  Chotero Abisalomu anathawa ndi kupita ku Gesuri+ ndipo anakhala kumeneko zaka zitatu. 39  Pamapeto pake mfumu Davide inalakalaka kupita kwa Abisalomu, pakuti anali atadzitonthoza pambuyo pa imfa ya Aminoni.

Mawu a M'munsi

Makeke amenewa sanali ophikidwa mu uvuni ngati mkate, koma ayenera kuti anali ophikidwa m’mafuta ambiri ngati madonasi.
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.