2 Samueli 18:1-33

18  Ndiyeno Davide anayamba kuwerenga anthu amene anali naye ndi kuwasankhira atsogoleri a magulu a anthu 1,000 ndi atsogoleri a magulu a anthu 100.+  Atatero, Davide anagawa anthuwo m’magulu atatu.+ Gulu loyamba analipereka kwa Yowabu,+ gulu lachiwiri analipereka kwa Abisai+ mwana wa Zeruya, m’bale wake wa Yowabu,+ ndipo gulu lachitatu analipereka kwa Itai+ Mgiti. Kenako mfumu inauza anthuwo kuti: “Inenso ndipita nanu sindilephera.”  Koma anthuwo anati: “Iyayi musapite,+ pakuti ngati titathawa kumeneko, sakasamala za ife.+ Ndipo ngati hafu ya ife tingafe, sakasamala za ife chifukwa inuyo ndinu wofunika kuposa anthu 10,000.+ Tsopano zingakhale bwino kuti muzititumikira ndi kutithandiza+ muli mumzinda mom’muno.”  Choncho mfumu inawauza kuti: “Ndichita zilizonse zimene inu mukuona kuti n’zabwino.”+ Pamenepo mfumu inangoima pambali pa chipata,+ ndipo anthu onse anapita kunkhondo m’magulu a anthu 100 ndi 1,000.+  Ndiyeno mfumu inalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti: “Musachitire nkhanza+ mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ubwino wanga.” Anthu onse anamva zimene mfumu inalamula atsogoleri onsewa za nkhani yokhudza Abisalomu.  Ndiyeno anthu anapitiriza ulendo wawo wopita kuthengo kukakumana ndi Isiraeli. Kumeneko nkhondo inayambika m’nkhalango ya Efuraimu.+  Pamapeto pake, anthu a Isiraeli+ anagonjetsedwa+ ndi atumiki a Davide, ndipo tsiku limenelo anthu ambiri anaphedwa, anthu 20,000.  Nkhondo imeneyi inafalikira dziko lonselo. Kuwonjezera apo, tsiku limenelo nkhalango inadya anthu ambiri kuposa amene anakanthidwa ndi lupanga.  Pamapeto pake, Abisalomu anakumana ndi atumiki a Davide. Abisalomu anali atakwera nyulu,* ndipo nyuluyo inadutsa paziyangoyango za nthambi za mtengo waukulu kwambiri. Choncho mutu wa Abisalomu unakola muziyangoyango za mtengo waukuluwo moti anali lendelende,+ koma nyulu imene anakwerapo ija inadutsa. 10  Ndiyeno munthu wina anaona zimenezo ndi kupita kukauza Yowabu kuti: “Ine ndaona Abisalomu ali lendelende+ mumtengo waukulu.” 11  Pamenepo Yowabu anafunsa munthu amene anali kumuuzayo kuti: “Tsopano iwe unamuona, nanga bwanji sunamuphe? Ukanamupha, unali udindo wanga kukupatsa ndalama 10 zasiliva ndi lamba.”+ 12  Koma munthuyo anauza Yowabu kuti: “Ngakhale ndikanalandira ndalama 1,000 zasiliva m’manja mwanga, sindikanatambasula dzanja langa ndi kupha mwana wa mfumu. Pakuti ife tinamva mfumu ikukulamulani inuyo, Abisai ndi Itai kuti, ‘Aliyense wa inu ateteze mnyamatayo Abisalomu.’+ 13  Apo ayi, ndikanachitira mfumu chinyengo, moti nkhani yonse sikanabisika kwa mfumu+ ndipo inu mukanandikanira.” 14  Pamenepo Yowabu anati: “Ndisachedwe chonchi ndi iwe!” Atatero anatenga mikondo itatu m’manja mwake ndi kulasa+ nayo mtima wa Abisalomu ali ndi moyo+ pakati pa mtengo waukulu. 15  Kenako atumiki 10 onyamula zida za Yowabu anafika pafupi ndi kukantha Abisalomu kuti afe.+ 16  Tsopano Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ kuti anthu abwerere, kusiya kuthamangitsa Isiraeli. Chotero Yowabu analetsadi anthuwo. 17  Pamapeto pake anatenga Abisalomu ndi kum’ponya m’dzenje lalikulu m’nkhalangomo ndipo anamuunjikira mulu waukulu kwambiri wa miyala.+ Koma Aisiraeli onse, aliyense anathawira kunyumba yake. 18  Tsopano Abisalomu akali moyo anadzimangira chipilala.+ Chipilala chimenechi chili m’Chigwa cha Mfumu,+ pakuti iye anati: “Ine ndilibe mwana wamwamuna woti asunge dzina langa monga chikumbukiro.”+ Choncho chipilala chimenecho anachitcha dzina lake+ ndipo chikudziwikabe ndi dzina lakuti Chipilala cha Abisalomu kufikira lero. 19  Ndiyeno Ahimazi+ mwana wa Zadoki anati: “Ndiloleni ndithamange ndikapereke uthenga kwa mfumu, chifukwa Yehova wamuweruza kuti amulanditse m’manja mwa adani ake.”+ 20  Koma Yowabu anamuuza kuti: “Iwe sindiwe woyenera kukapereka uthenga lero, udzapereka uthenga tsiku lina. Lero usakapereke uthenga chifukwa chakuti mwana wa mfumu wafa.”+ 21  Ndiyeno Yowabu anauza Mkusi+ kuti: “Pita ukauze mfumu zimene waona.” Pamenepo Mkusiyo anaweramira Yowabu ndi kuyamba kuthamanga. 22  Tsopano Ahimazi mwana wa Zadoki anauzanso Yowabu kuti: “Chilichonse chichitike, chonde ndiloleni inenso ndithamange kutsatira Mkusiyu.” Koma Yowabu anati: “N’chifukwa chiyani iwenso ukufuna kuthamanga mwana wanga pamene ulibe uthenga woti ukanene?” 23  Iye anapitiriza kunena kuti: “Chilichonse chichitike, ndiloleni ndithamange.” Choncho Yowabu anati: “Thamanga!” Pamenepo Ahimazi anayamba kuthamanga kulowera njira ya ku Chigawo*+ ndipo kenako anamudutsa Mkusi uja. 24  Tsopano Davide anali atakhala pakati pa zipata ziwiri.+ Pa nthawiyi mlonda+ anakwera padenga la mpanda kuchipata. Ndiyeno atakweza maso anaona munthu akuthamanga ali yekha. 25  Choncho mlondayo anaitana mfumu ndi kuiuza zimenezo. Pamenepo mfumuyo inati: “Ngati ali yekha, ndiye kuti akudzanena uthenga.” Munthu uja anali kubwera ndithu, ndipo pang’ono ndi pang’ono anali kuyandikira. 26  Kenako mlonda uja anaonanso munthu wina akuthamanga. Ndiyeno mlondayo anaitana mlonda wa pachipata ndi kumuuza kuti: “Taona! Munthu winanso akuthamanga ali yekha.” Pamenepo mfumu inati: “Ameneyunso akubweretsa uthenga.” 27  Ndiyeno mlondayo anapitiriza kunena kuti: “Ndikuona kuti kathamangidwe ka munthu woyambayu kakufanana ndi kathamangidwe+ ka Ahimazi+ mwana wa Zadoki.” Atatero, mfumu inati: “Ahimazi ndi munthu wabwino,+ ndipo uthenga umene wabweretsa uyenera kukhala wabwino.”+ 28  Kenako Ahimazi anaitana mfumu ndi kuiuza kuti: “Zonse zili bwino!” Atatero anagwada pamaso pa mfumu ndi kuwerama. Ndiyeno anati: “Adalitsike+ Yehova Mulungu wanu, amene wapereka+ amuna amene anatambasula manja awo ndi kuukira inu mbuyanga mfumu!” 29  Koma mfumu inati: “Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino?” Poyankha Ahimazi anati: “Pamene Yowabu anali kutuma mtumiki wa mfumu ndi ine mtumiki wanu, ndinaona chipwirikiti chachikulu, koma sindinadziwe chimene chinali kuchitika.”+ 30  Pamenepo mfumu inati: “Patuka, ima pambalipa.” Choncho anapatuka ndi kuima pambali. 31  Kenako Mkusi+ uja anafika, ndi kuyamba kunena kuti: “Ndabweretsa uthenga mbuyanga mfumu, pakuti Yehova wakuweruzani lero kuti akulanditseni m’manja mwa anthu onse okuukirani.”+ 32  Koma mfumu inafunsa Mkusiyo kuti: “Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino?” Poyankha Mkusiyo anati: “Adani anu mbuyanga mfumu ndi anthu onse ofuna kukuchitirani zoipa akhale ngati mnyamatayo.”+ 33  Pamenepo mfumu inasokonezeka ndipo inakwera m’chipinda cha padenga+ cha pachipata ndi kuyamba kulira. Mfumu inali kuyenda n’kumanena kuti: “Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga+ Abisalomu! Haa! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine m’malo mwa iwe, Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.