2 Samueli 15:1-37

15  Ndiyeno pambuyo pa zinthu zimenezi, Abisalomu anadzipangira galeta lokokedwa ndi mahatchi, ndipo amuna 50 anali kuthamanga patsogolo pake.+  Tsopano Abisalomu anadzuka m’mawa kwambiri+ ndi kukaima pambali pa msewu wa kuchipata.+ Ndiyeno munthu aliyense amene anali ndi mlandu akafika kuti mlandu wake ukaweruzidwe ndi mfumu,+ Abisalomu anali kumuitana ndi kumuuza kuti: “Wachokera mumzinda uti?” Poyankha munthuyo anali kunena kuti: “Ine mtumiki wanu ndachokera mu limodzi la mafuko a Isiraeli.”  Pamenepo Abisalomu anali kumuuza kuti: “Taona, nkhani yakoyi ili bwino ndipo ndi yosavuta. Koma mfumu ilibe aliyense woti amvetsere nkhani yakoyi.”+  Ndiyeno Abisalomu anali kupitiriza kunena kuti: “Haa! Zikanakhalatu bwino ndikanaikidwa kukhala woweruza m’dziko lino+ kuti munthu aliyense wokhala ndi mlandu kapena wofuna chiweruzo azibwera kwa ine, ndipo ndikanamuchitira chilungamo.”+  Ndiyeno zimene zinali kuchitikanso n’zakuti, munthu akafika pafupi kuti amuweramire, Abisalomu anali kutambasula dzanja lake ndi kumugwira+ kenako n’kumupsompsona.  Abisalomu anapitiriza kuchita zinthu zoterezi kwa Aisiraeli onse amene anali kubwera kwa mfumu kuti iwaweruzire milandu yawo, moti Abisalomu anapitiriza kukopa mitima ya anthu a mu Isiraeli.+  Tsopano kumapeto kwa zaka 40,* Abisalomu anauza mfumu kuti: “Chonde, ndiloleni ndichoke, ndipite ku Heburoni+ kukakwaniritsa lonjezo langa lalikulu limene ndinalonjeza Yehova.+  Pakuti ine mtumiki wanu ndinalonjeza lonjezo lalikulu+ pamene ndinali kukhala ku Gesuri,+ ku Siriya, ndipo ndinati, ‘Yehova akandilola kubwerera ku Yerusalemu, ndiyenera kupereka nsembe kwa Yehova.’”+  Pamenepo mfumu inamuyankha kuti: “Pita mu mtendere.”+ Zitatero, ananyamuka ndi kupita ku Heburoni. 10  Ndiyeno Abisalomu anatumiza akazitape+ m’mafuko onse a Isiraeli ndipo anawauza kuti: “Mukangomva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, munene kuti, ‘Abisalomu wakhala mfumu+ ku Heburoni!’”+ 11  Pochoka, Abisalomu anatenga anthu 200 mu Yerusalemu. Amenewa anawaitana ndipo ananyamuka m’chimbulimbuli+ osadziwa kena kalikonse. 12  Kuwonjezera apo, pamene Abisalomu anali kupereka nsembe, anaitanitsa Ahitofeli+ Mgilo,+ phungu wa Davide,+ kuchoka kumzinda wakwawo wa Gilo.+ Chiwembu+ chimenecho chinapitiriza kukula ndipo chiwerengero cha anthu amene anali kutsatira Abisalomu chinapitiriza kuwonjezeka.+ 13  Patapita nthawi, munthu wina anauza Davide kuti: “Mitima+ ya anthu a mu Isiraeli yatsatira Abisalomu.” 14  Nthawi yomweyo, Davide anauza atumiki ake onse amene anali naye limodzi mu Yerusalemu, kuti: “Nyamukani, tiyeni tithawe,+ pakuti sipapezeka munthu wopulumuka m’manja mwa Abisalomu. Chitani changu, pakuti mwina angafike mofulumira ndi kutipeza n’kutichitira choipa komanso kukantha mzinda ndi lupanga!”+ 15  Pamenepo atumiki a mfumu anauza mfumu kuti: “Ife atumiki anu tichita mogwirizana ndi zimene inu mbuyathu mfumu mwasankha.”+ 16  Choncho mfumu inanyamuka ndi kutuluka ndipo anthu onse a m’nyumba yake anaitsatira.+ Koma mfumuyo inasiya akazi 10, amene anali adzakazi ake,+ kuti asamalire nyumba. 17  Mfumu inatulukadi ndi kupitiriza ulendo wake pamodzi ndi anthu onse amene anali kuitsatira ndipo anaima ku Beti-merehaki.* 18  Kumeneko atumiki onse a mfumu, Akereti onse ndi Apeleti+ onse, anali kudutsa pamaso pake. Komanso Agiti+ onse, amuna 600 amene anamutsatira* kuchokera ku Gati+ anali kudutsa pamaso pake. 19  Kenako mfumu inauza Itai+ Mgiti kuti: “Kodi iweyo ukupita nafe chifukwa chiyani? Bwerera+ ukakhale ndi mfumu, pakuti ndiwe mlendo komanso ndiwe wothawa kwanu. 20  Iwe wabwera dzulo lomweli, kodi lero uyende+ ndi ife kupita kulikonse kumene ine ndikupita? Bwerera, tenga abale ako ndi kubwerera nawo limodzi, ndipo Yehova akusonyeze kukoma mtima kosatha+ ndi kukhulupirika kwake!”+ 21  Koma Itai anayankha mfumu kuti: “Pali Yehova, Mulungu wamoyo, komanso pali moyo wanu mbuyanga mfumu,+ kulikonse kumene inu mbuyanga mfumu mudzapita ine mtumiki wanu ndidzapitanso komweko, ndipo ndili wokonzeka ngakhale kufa nanu limodzi!”+ 22  Pamenepo Davide anauza Itai+ kuti: “Dutsa, upite.” Choncho Itai Mgiti anadutsa pamaso pake komanso amuna onse amene anali kuyenda naye ndi ana onse amene anali naye. 23  Anthu onse a m’dzikoli anali kulira mokweza mawu,+ ndipo anthu onse amene anali ndi Davide anali kudutsa pamaso pake. Mfumu inaimirira pafupi ndi chigwa* cha Kidironi,+ ndipo anthu onse anali kudutsa mumsewu waukulu wopita kuchipululu. 24  Kumeneko kunalinso Zadoki+ pamodzi ndi Alevi+ onse atanyamula+ likasa+ la pangano la Mulungu woona. Choncho Aleviwo anatula pansi likasa la Mulungu woona pafupi ndi Abiyatara+ kufikira anthu onse atamaliza kudutsa kuchokera mumzinda. 25  Ndiyeno mfumu inauza Zadoki kuti: “Tenga likasa+ la Mulungu woona ndi kubwerera nalo mumzinda.+ Yehova akandikomera mtima adzandibwezeretsa mumzinda ndipo ndidzaliona. Ndidzaonanso malo amene limakhala.+ 26  Koma akanena kuti, ‘Sindikusangalala nawe,’ ine ndidzavomereza zilizonse zimene adzandichitira.”+ 27  Pamenepo mfumu inapitiriza kuuza Zadoki wansembe kuti: “Iwe ndi wamasomphenya,*+ si choncho kodi? Bwerera kumzinda mu mtendere. Bwerera pamodzi ndi Ahimazi mwana wako wamwamuna ndi Yonatani+ mwana wamwamuna wa Abiyatara. Mubwerere ndi ana anu awiri amene muli nawowa. 28  Taona, ine ndikhalabe pamalo owolokera amene ali pafupi ndi chipululu kufikira amuna inu mutatumiza uthenga wondidziwitsa mmene zinthu zilili.”+ 29  Choncho Zadoki ndi Abiyatara anatenga likasa la Mulungu woona ndi kubwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo anapitiriza kukhala kumeneko. 30  Davide anali kukwezeka zitunda za phiri la Maolivi+ akulira, ataphimba kumutu kwake.+ Anali kuyenda wosavala nsapato ndipo aliyense mwa anthu amene anali naye anaphimba kumutu kwake ndipo onse anali kuyenda akulira.+ 31  Kenako uthenga unafika kwa Davide wonena kuti: “Ahitofeli nayenso ali pakati pa anthu amene akukonza chiwembu+ pamodzi ndi Abisalomu.”+ Pamenepo Davide anati:+ “Inu Yehova!+ Chonde, sandutsani malangizo a Ahitofeli kuti akhale opusa.”+ 32  Ndiyeno pamene Davide anafika pamwamba pa phiri pamene anthu anali kugwadira Mulungu, anaona Husai+ Mwareki+ akubwera kudzakumana naye, atang’amba chovala chake ndiponso atadzithira dothi kumutu.+ 33  Pamenepo Davide anamuuza kuti: “Ukapita nane limodzi, ukhala mtolo wolemetsa kwa ine.+ 34  Koma ukabwerera kumzinda ndi kukauza Abisalomu kuti, ‘Inu Mfumu ine ndine mtumiki wanu. Kale ndinali mtumiki wa bambo anu, koma tsopano ndine mtumiki wanu,’+ pamenepo ukanditsutsire+ malangizo a Ahitofeli. 35  Kodi kumeneko suli ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembe?+ Chilichonse chimene ukamve kuchokera kunyumba ya mfumu ukauze Zadoki ndi Abiyatara ansembe.+ 36  Taona, iwo ali ndi ana amuna awiri, Ahimazi+ mwana wa Zadoki ndi Yonatani+ mwana wa Abiyatara. Choncho amuna inu mukatume amenewa kuti adzandiuze zonse zimene mungamve.” 37  Pamenepo Husai, mnzake wa Davide,+ anabwerera kumzinda. Ndipo Abisalomu+ anabwera ku Yerusalemu.

Mawu a M'munsi

N’zotheka kuti zaka 40 zimenezi akuziwerenga kuchokera pamene Davide anadzozedwa kukhala mfumu. Onani 1Sa 16:13.
Dzinali limatanthauza, “Nyumba Yakutali.”
Apa akunena za amene anatsatira “Itai,” wotchulidwa m’vesi 19.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.
Onani mawu a m’munsi pa 1Mb 29:29.