2 Samueli 22:1-51
22 Davide analankhula ndi Yehova mawu a nyimbo iyi,+ pa tsiku limene Yehova anamulanditsa kwa adani ake+ onse ndiponso m’manja mwa Sauli.+
2 Iye anati:“Yehova ndiye thanthwe langa,+ malo anga achitetezo+ ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+
3 Mulungu wanga ndiye thanthwe langa.+ Ine ndidzathawira kwa iye,Iye ndi chishango changa,+ nyanga* yanga+ ya chipulumutso ndi malo anga okwezeka achitetezo.+Iye ndi malo anga othawirako,+ Mpulumutsi wanga.+ Mumandipulumutsa ku chiwawa.+
4 Ndidzaitanira pa Yehova, Iye woyenera kutamandidwa,+Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+
5 Pakuti mafunde akupha anandizungulira.+Panali chikhamu cha anthu opanda pake amene anali kundiopseza.+
6 Zingwe za Manda* zinandizungulira.+Ndinakumana ndi misampha ya imfa.+
7 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,+Ndinaitana Mulungu wanga.+Pamenepo iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake,+Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
8 Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+Maziko a kumwamba anagwedezeka.+Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+
9 Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+Makala onyeka anatuluka mwa iye.+
10 Iye anaweramitsa kumwamba n’kutsika.+Mdima wandiweyani unali kunsi kwa mapazi ake.+
11 Iye anafika atakwera pakerubi+ wouluka.Anaonekera pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+
12 Kenako anaika mdima momuzungulira ngati misasa,+Anaika madzi akuda ndi mtambo wakuda.+
13 M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka makala oyaka moto.+
14 Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake.+
15 Anayamba kuponya mivi kuti awabalalitse.+Anaponya mphezi kuti awasokoneze.+
16 Ndipo ngalande za pansi pa nyanja zinaonekera,+Maziko a dziko lapansi+ anakhala poonekera,Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwa Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwake.+
17 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba ndi kunditenga,+Anandivuula m’madzi akuya.+
18 Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+
19 Adaniwo anandifikira m’tsiku la tsoka langa,+Koma Yehova anandichirikiza.+
20 Ananditenga ndi kundiika pamalo otakasuka.+Anandipulumutsa chifukwa anakondwera nane.+
21 Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+
22 Pakuti ndasunga njira za Yehova,+Sindinachoke kwa Mulungu wanga.+ Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.
23 Pakuti zigamulo+ zake zonse zili pamaso panga.Ndipo sindidzapatuka pa malamulo ake.+
24 Ndidzakhalabe wopanda cholakwa+ pamaso pake,Ndipo ndidzayesetsa kupewa cholakwa.+
25 Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+Andibwezere mogwirizana ndi kukhala kwanga woyera pamaso pake.+
26 Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+Munthu wamphamvu wopanda cholakwa, mudzamuchitira mwachilungamo.+
27 Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+Kwa munthu wopotoka maganizo mudzachita zinthu ngati wopusa.+
28 Anthu odzichepetsa mudzawapulumutsa.+Koma mumatsutsa odzikweza, kuti muwatsitse.+
29 Inu Yehova ndinu nyale yanga,+Ndipo Yehova ndiye amandiunikira pamene ndili mu mdima.+
30 Pakuti ndi thandizo lanu ndingathamangitse gulu la achifwamba.+Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+
31 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+
32 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+Kodi pali thanthwe linanso loposa Mulungu wathu?+
33 Mulungu woona ndiye malo anga otetezeka kwambiri,+Ndipo adzasalaza njira yanga.+
34 Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+
35 Iye akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo.+Ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.+
36 Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.+
37 Mudzakulitsa malo opondapo mapazi anga.+Ndipo mapazi anga sadzagwedezeka.+
38 Ndidzathamangitsa adani anga kuti ndiwafafanize,Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+
39 Ndidzawawononga onse ndi kuwaphwanya zibenthuzibenthu+ kuti asadzukenso.+Iwo adzagwa pansi ndipo ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+
40 Inu mudzandiveka mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.+Mudzakomola ondiukira.+
41 Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+
42 Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+
43 Ndidzawapera kukhala ngati fumbi la padziko lapansi.Ndidzawapondaponda ngati matope a mumsewu,+Ndipo ndidzawasasantha.
44 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+Mudzanditeteza kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu yonse.+Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+
45 Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+Anthu adzamvetsera mawu anga ndi kuwatsatira.+
46 Alendo adzatha mphamvu,Ndipo adzatuluka m’malo awo achitetezo akunjenjemera.+
47 Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+Mulungu wanga, thanthwe limene limandipulumutsa likhale lokwezeka.+
48 Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga,+Iye amaika mitundu ya anthu kunsi kwa mapazi anga.+
49 Iye amandichotsa pakati pa adani anga.+Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+Mudzandilanditsa kwa munthu wochita zachiwawa.+
50 N’chifukwa chake ndidzayamika inu Yehova pakati pa mitundu.+Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+
51 Ndidzaimbira Iye wochita ntchito zazikulu zachipulumutso kwa mfumu yake,+Iye wosonyeza kukoma mtima kosatha kwa wodzozedwa wake,+Kwa Davide ndi mbewu yake mpaka kalekale.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 5.
^ Kapena kuti “mapiko a mphepo.”
^ Kapena kuti, “Mudzandipatsa kumbuyo kwa khosi la adani anga.”