2 Samueli 19:1-43

19  Patapita nthawi, uthenga unafika kwa Yowabu kuti: “Mfumu ikulira, ikupitiriza kulirira Abisalomu.”+  Choncho tsiku limenelo chipulumutso chinasanduka nthawi yoti anthu onse alire maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti: “Mfumu yakhumudwa ndi imfa ya mwana wake.”  Ndipo tsiku limenelo anthu anayamba kulowa mumzinda+ mozemba ngati mmene anthu amazembera chifukwa cha manyazi akathawa kunkhondo.  Ndiyeno mfumu inaphimba nkhope yake, ndipo inapitiriza kulira mokweza mawu kuti: “Mwana wanga Abisalomu! Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”+  Pamapeto pake, Yowabu anafika kunyumba ya mfumu ndi kuiuza kuti: “Lero mwachititsa manyazi nkhope za atumiki anu onse, amene lero apulumutsa moyo wanu+ komanso moyo wa ana anu aamuna,+ ana anu aakazi,+ akazi anu+ ndi adzakazi anu,+  mwa kukonda anthu odana nanu ndi kudana ndi anthu okukondani. Lero mwasonyeza kuti akulu ndi atumiki alibe ntchito kwa inu, chifukwa ine ndikudziwa bwino kuti Abisalomu akanakhala ndi moyo koma ena tonsefe n’kufa, pamenepo zikanakhala bwino kwa inu.  Tsopano nyamukani, mutuluke kukalankhula ndi atumiki anu ndi kuwalimbikitsa,+ chifukwa ngati simupita kukalankhula nawo, ndithu ndikulumbira pali Yehova, sipapezeka munthu wogona kuno lero.+ Zimenezi zikhala zoipa kwambiri kwa inu kuposa zoipa zonse zimene mwakumana nazo kuyambira pa ubwana wanu mpaka pano.”  Choncho mfumu inanyamuka ndi kukakhala kuchipata.+ Zitatero uthenga unapita kwa anthu onse kuti: “Mfumu yakhala kuchipata.” Pamenepo anthu onse anayamba kubwera kwa mfumu. Koma Aisiraeli onse amene anagonjetsedwa, aliyense anathawira kunyumba yake.+  Ndiyeno anthu onse anayamba kukangana m’mafuko onse a Isiraeli kuti: “Mfumuyi ndi imene inatilanditsa m’manja mwa adani athu,+ ndipo ndi mfumu yomweyi imene inatipulumutsa m’manja mwa Afilisiti. Tsopano yachoka m’dziko lino kuthawa Abisalomu.+ 10  Koma Abisalomu amene tinamudzoza kukhala mtsogoleri wathu+ wafa kunkhondo.+ Nanga n’chifukwa chiyani simukuchitapo kanthu kuti mfumu ibwerere?”+ 11  Ndiyeno Mfumu Davide inatumiza uthenga kwa Zadoki+ ndi Abiyatara+ ansembe kuti: “Lankhulani ndi akulu a Yuda+ kuti, ‘N’chifukwa chiyani inu nokha simukuchitapo kanthu kuti mfumu ibwerere kunyumba yake, pamene Aisiraeli onse atumiza uthenga kwa mfumu kumene ikukhala? 12  Inu ndinu abale anga, ndinu fupa langa ndi mnofu wanga.+ Ndiye n’chifukwa chiyani inu nokha simukuchitapo kanthu kuti mfumu ibwerere?’ 13  Amasa mumuuze kuti,+ ‘Kodi iwe sindiwe fupa langa ndi mnofu wanga? Mulungu andilange mowirikiza+ ngati sudzakhala mtsogoleri wa gulu langa lankhondo nthawi zonse m’malo mwa Yowabu.’”+ 14  Pamenepo mitima ya amuna onse a Yuda inakopeka ndipo anamvana chimodzi,+ moti anatumiza uthenga kwa mfumu kuti: “Bwererani, inuyo pamodzi ndi atumiki anu onse.” 15  Ndiyeno mfumu inayamba kubwerera kwawo ndipo inafika ku Yorodano. Pamenepo anthu a Yuda anafika ku Giligala+ kuti apite kukakumana ndi mfumu ndi kuiperekeza pamene inali kuwoloka mtsinje wa Yorodano. 16  Kenako Simeyi+ mwana wa Gera,+ wa fuko la Benjamini, wochokera ku Bahurimu,+ pamodzi ndi amuna a ku Yuda anapita mofulumira kukakumana ndi Mfumu Davide. 17  Iye anali ndi amuna 1,000 ochokera ku Benjamini. (Analinso ndi Ziba+ mtumiki wa nyumba ya Sauli pamodzi ndi ana ake 15+ ndi atumiki ake 20. Iwo anakwanitsa kukafika ku Yorodano mfumu isanafike. 18  Atafika kumeneko, anawolokera tsidya lina+ kuti akawolotse anthu a m’banja la mfumu ndi kuchita zabwino pamaso pake.) Koma mfumu itatsala pang’ono kuwoloka Yorodano, Simeyi mwana wa Gera, anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.+ 19  Ndiyeno anauza mfumu kuti: “Mbuyanga mfumu, musandione ngati munthu wolakwa. Musakumbukire ndi kuikira kumtima cholakwa chimene ine mtumiki wanu ndinachita+ tsiku lija limene inu mbuyanga mfumu munatuluka mu Yerusalemu.+ 20  Pakuti ine mtumiki wanu ndikudziwa bwino kuti ndinachimwa. Tsopano lero ndine woyamba m’nyumba yonse ya Yosefe+ kubwera kuno kudzakumana ndi inu mbuyanga mfumu.” 21  Nthawi yomweyo Abisai+ mwana wa Zeruya+ anayankha kuti: “Pa zimene wanenazi, kodi Simeyi sakuyenera kuphedwa chifukwa chotemberera wodzozedwa wa Yehova?”+ 22  Koma Davide anati: “Ndili nanu chiyani+ inu ana a Zeruya kuti lero mukhale otsutsana+ nane? Kodi mu Isiraeli muyenera kuphedwa munthu aliyense lero?+ Kodi ine sindikudziwa bwino kuti lero ndine mfumu ya Isiraeli?” 23  Kenako mfumu inauza Simeyi kuti: “Suufa.” Pamenepo mfumu inamulumbirira.+ 24  Koma Mefiboseti,+ mdzukulu wake wa Sauli, anabwera kudzaonana ndi mfumu. Iye sanasamalire mapazi ake,+ kumeta ndevu zake zapamlomo+ kapena kuchapa zovala zake kuchokera tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere. 25  Ndiyeno zinachitika kuti, atafika ku Yerusalemu kukakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?” 26  Poyankha anati: “Mbuyanga mfumu, mtumiki wanga ndi amene anandipusitsa. Ine mtumiki wanu+ ndinanena kuti, ‘Ndiikireni chishalo pabulu wamkazi kuti ndikwerepo ndi kupita pamodzi ndi mfumu,’ pakuti ine mtumiki wanu ndine wolumala.+ 27  Choncho mtumiki wangayo anandinenera+ ine mtumiki wanu miseche kwa inu mbuyanga mfumu. Koma inu mbuyanga mfumu muli ngati mngelo+ wa Mulungu woona, motero chitani zimene zili zabwino kwa inu. 28  Pakuti kwa inu mbuyanga mfumu, nyumba yonse ya bambo anga ikanayenera kuwonongedwa, koma m’malomwake mwaika ine mtumiki wanu pakati pa anthu amene akudya chakudya patebulo+ la mfumu. Ndiye ndili ndi chifukwa chanji chomveka chopitirizira kudandaula+ kwa inu mfumu?” 29  Komabe mfumu inamuuza kuti: “N’chifukwa chiyani ukupitiriza kulankhula zonsezi? Ine ndikuti, iwe ndi Ziba mugawane mundawo.”+ 30  Pamenepo Mefiboseti anauza mfumu kuti: “Musiyeni atenge munda wonsewo,+ popeza kuti tsopano inu mbuyanga mfumu mwabwerera kunyumba yanu mu mtendere.” 31  Ndiyeno Barizilai+ Mgiliyadi nayenso anatsika kuchokera ku Rogelimu. Iye anapita ku Yorodano pamodzi ndi mfumu. Barizilai anaperekeza mfumu mpaka kukafika ku Yorodano. 32  Barizilai anali wokalamba kwambiri pakuti anali ndi zaka 80.+ Pamene mfumu inali kukhala ku Mahanaimu,+ Barizilai anali kuipatsa chakudya pakuti iye anali munthu wolemera kwambiri.+ 33  Ndiyeno mfumu inauza Barizilai kuti: “Tiye tiwolokere ku Yerusalemu ndipo tizikadya chakudya pamodzi.”+ 34  Koma Barizilai anauza mfumu kuti: “Kodi masiku a moyo wanga atsala angati kuti ndipite ku Yerusalemu pamodzi ndi mfumu? 35  Ine lero ndili ndi zaka 80.+ Kodi ine mtumiki wanu ndingasiyanitse chabwino ndi choipa kapena kumva kukoma kwa zimene ndadya ndi kumwa?+ Kodi ine ndingathenso kumva+ mawu a amuna ndi akazi oimba?+ Ndiye ine mtumiki wanu ndikhalirenji mtolo wolemetsa+ kwa inu mbuyanga mfumu? 36  Ine mtumiki wanu ndangokuperekezani mtunda waufupi kudzafika kuno ku Yorodano, ndiye n’chifukwa chiyani inu mfumu mukundipatsa mphoto imeneyi?+ 37  Ndiloleni chonde ine mtumiki wanu ndibwerere, ndikafere+ mumzinda wa kwathu pafupi ndi manda a bambo anga ndi mayi anga.+ Koma ndikupereka mtumiki wanu Chimamu.+ Muloleni ameneyu awoloke nanu pamodzi mbuyanga mfumu, ndipo mumuchitire zimene zili zabwino kwa inu.” 38  Pamenepo mfumu inati: “Chimamu awoloka nane pamodzi, ndipo ine ndimuchitira zimene zili zabwino kwa iwe. Chilichonse chimene udzasankha kuti ine ndikuchitire, ine ndidzachita.” 39  Tsopano anthu onse anayamba kuwoloka Yorodano, ndipo mfumu nayonso inawoloka. Koma mfumu inapsompsona+ Barizilai ndi kumudalitsa,+ kenako Barizilai anabwerera kwawo. 40  Pamene mfumu inali kuwolokera ku Giligala,+ Chimamu nayenso anawoloka nayo pamodzi. Anthu onse a Yuda ndi hafu ya anthu a Isiraeli nawonso anawoloka kuti ayende pamodzi ndi mfumu. 41  Pamenepo anthu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “N’chifukwa chiyani+ abale athu a ku Yuda akubweretsani mozemba inu mfumu Davide, pamodzi ndi banja lanu ndi anthu onse amene anali ndi inu kutsidya la Yorodano?”+ 42  Pamenepo anthu a ku Yuda anayankha anthu a ku Isiraeli kuti: “Chifukwa chakuti mfumuyi ndi wachibale wathu wapafupi.+ N’chifukwa chiyani inu mwakwiya nazo zimenezi? Kodi ife tadya zinthu zilizonse za mfumu kapena kulandira mphatso?” 43  Koma anthu a ku Isiraeli anayankha anthu a ku Yuda kuti: “Ifetu tili ndi mafuko 10 mu ufumu umenewu.+ Choncho mu ufumu wa Davide tilitu ndi mphamvu zambiri kuposa inu. Ndiyeno n’chifukwa chiyani mukutinyoza chotero, ndipo kodi ife sitinayenera kukhala patsogolo+ pobweretsa mfumu yathu?” Koma mawu a anthu a ku Yuda anali aukali kwambiri kuposa a anthu a ku Isiraeli.

Mawu a M'munsi