2 Samueli 3:1-39

3  Nkhondo ya pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide inatenga nthawi yaitali.+ Davide anapitirizabe kukhala wamphamvu+ koma nyumba ya Sauli inali kufookerafookera.+  Pa nthawiyi, Davide anabereka ana aamuna+ ku Heburoni,+ ndipo mwana wake woyamba anali Aminoni+ wobadwa kwa Ahinowamu+ wa ku Yezereeli.  Mwana wake wachiwiri anali Kileyabu+ wobadwa kwa Abigayeli+ wa ku Karimeli, amene anali mkazi wa Nabala, ndipo wachitatu anali Abisalomu+ wobadwa kwa Maaka, mwana wamkazi wa Talimai+ mfumu ya ku Gesuri.  Wachinayi anali Adoniya+ wobadwa kwa Hagiti,+ ndipo wachisanu anali Sefatiya+ wobadwa kwa Abitali.  Wa 6 anali Itireamu+ wobadwa kwa Egila, mkazi wa Davide. Amenewa ndi ana amene Davide anabereka ali ku Heburoni.  Ndiyeno pamene nkhondo ya pakati pa nyumba ya Sauli ndi nyumba ya Davide inali kupitirira, Abineri+ nayenso anali kukula mphamvu m’nyumba ya Sauli.  Tsopano Sauli anali ndi mdzakazi, dzina lake Rizipa,+ mwana wamkazi wa Aya.+ Patapita nthawi, Isi-boseti+ anafunsa Abineri kuti: “N’chifukwa chiyani unagona ndi mdzakazi*+ wa bambo anga?”  Abineri atamva mawu amenewa a Isi-boseti anakwiya kwambiri+ n’kunena kuti: “Kodi ine ndine galu+ wopanda pake wa Yuda? Ineyo ndikusonyeza kukoma mtima kosatha ku nyumba ya Sauli bambo ako, abale ake ndi mabwenzi ake apamtima, ndipo ndikukuteteza kuti usagwe m’manja mwa Davide, koma lero ukundiimba mlandu wa cholakwa chokhudza mkazi.  Mulungu alange ine Abineri mowirikiza,+ ngati sindidzachitira Sauli mogwirizana ndi zimene Yehova analumbira kwa Davide,+ 10  ndi kusamutsa ufumu kuuchotsa m’nyumba ya Sauli, n’kukhazikitsa mpando wachifumu wa Davide mu Isiraeli ndi mu Yuda, kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba.”+ 11  Pamenepo Isi-boseti sanathe kuyankha Abineri ngakhale liwu limodzi chifukwa anali kumuopa.+ 12  Chotero, Abineri anatumiza mithenga kwa Davide nthawi yomweyo, kuti akamuuze kuti: “Kodi mwini dziko ndani?” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Chita nane pangano, ndipo inetu ndidzakuthandiza kutembenuza Isiraeli yense kukhala kumbali yako.”+ 13  Davide anamuyankha kuti: “Chabwino! Ineyo ndichitadi nawe pangano. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi ichi, ‘Usadzaone nkhope yanga+ pokhapokha utabweretsa Mikala,+ mwana wamkazi wa Sauli pobwera kuno.’” 14  Davide anatumizanso mithenga kwa Isi-boseti+ mwana wa Sauli ndi uthenga wonena kuti: “Ndipatse mkazi wanga Mikala, amene ndinalonjeza kumukwatira mwa kupereka makungu 100 akunsonga+ a Afilisiti.” 15  Choncho Isi-boseti anatuma anthu kuti akatenge Mikala kwa mwamuna wake Palitiyeli,*+ mwana wa Laisi. 16  Koma mwamuna wake anali kumutsatira. Iye anali kumutsatira pambuyo akulira mpaka kukafika ku Bahurimu.+ Kenako Abineri anamuuza kuti: “Bwerera!” Pamenepo iye anabwerera. 17  Izi zili choncho, Abineri analankhulana ndi akulu a Isiraeli kuti: “Kwa nthawi yaitali,+ mwakhala mukufuna Davide kuti akhale mfumu yanu. 18  Tsopano chitanipo kanthu, pakuti Yehova anauza Davide kuti, ‘Ndidzapulumutsa anthu anga Aisiraeli m’manja mwa Afilisiti ndiponso m’manja mwa adani awo onse pogwiritsa ntchito dzanja la Davide+ mtumiki wanga.’” 19  Abineri analankhulanso ndi Abenjamini,+ kenako anapita kukauza Davide ku Heburoni zinthu zonse zimene zinali zabwino kwa Isiraeli ndi ku nyumba yonse ya Benjamini. 20  Abineri atafika kwa Davide ku Heburoni pamodzi ndi amuna 20, Davide anakonzera phwando+ Abineri ndi amuna amene anali naye. 21  Kenako Abineri anauza Davide kuti: “Ndiloleni ndinyamuke ndi kupita kuti ndikasonkhanitse Isiraeli yense kwa mbuyanga mfumu, kuti anthuwo achite pangano ndi inu ndipo mudzakhaladi mfumu pa zonse zimene moyo wanu umalakalaka.”+ Pamenepo Davide analola Abineri kupita ndipo ananyamukadi mwamtendere.+ 22  Tsopano atumiki a Davide ndi Yowabu, anali kuchokera kunkhondo, atafunkha+ zinthu zambiri. Koma Abineri sanali ndi Davide ku Heburoni popeza anali atanyamuka mwamtendere ndipo anali pa ulendo wake. 23  Ndiyeno Yowabu+ anafika pamodzi ndi gulu lankhondo limene anali nalo, ndipo anthu anauza Yowabu kuti: “Abineri+ mwana wa Nera+ anafika kwa mfumu, ndipo mfumu yamulola kupita moti ali pa ulendo wake mwamtendere.” 24  Pamenepo Yowabu anapita kwa mfumu n’kunena kuti: “N’chiyani chimene mwachitachi?+ Abineri anabwera kwa inu. N’chifukwa chiyani mwamulola kuti anyamuke ndi kupita mwamtendere? 25  Inu mukum’dziwa bwino Abineri mwana wa Nera. Iye anabwera kuno kudzakupusitsani kuti adziwe kutuluka ndi kulowa kwanu,+ ndiponso kuti adziwe chilichonse chimene mukuchita.”+ 26  Atanena mawu amenewa, Yowabu anachoka pamaso pa Davide ndipo anatumiza mithenga kuti itsatire Abineri. Mithengayo inabweza Abineri+ pachitsime cha Sira, koma Davide sanadziwe kena kalikonse. 27  Abineri atabwerera ku Heburoni,+ Yowabu anam’tengera pambali kuchipata kuti alankhulane naye pa awiri.+ Koma kumeneko anamubaya pamimba+ moti anafa chifukwa chokhetsa magazi a Asaheli,+ m’bale wake wa Yowabu. 28  Davide atamva zimenezi pambuyo pake, ananena kuti: “Pamaso pa Yehova, ineyo ndi ufumu wanga, mlandu wa magazi+ a Abineri mwana wa Nera sukutikhudza mpaka kalekale.* 29  Mlandu umenewu ubwerere pamutu+ pa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya bambo ake. M’nyumba ya Yowabu+ simudzasowa munthu wa nthenda yakukha kumaliseche+ ndiponso wakhate.+ Simudzasowanso mwamuna wogwira ndodo yowombera nsalu,+ wokanthidwa ndi lupanga kapena wosowa mkate!”+ 30  Yowabu ndi m’bale wake Abisai,+ anapha Abineri+ chifukwa chakuti iye anapha Asaheli m’bale wawo pa nkhondo ku Gibeoni.+ 31  Ndiyeno Davide anauza Yowabu ndi anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Ng’ambani zovala zanu+ ndipo muvale ziguduli*+ kuti mulire maliro a Abineri.” Ngakhale Mfumu Davide nayenso anayenda pambuyo pa chithatha cha Abineri. 32  Choncho Abineri anamuika m’manda ku Heburoni. Ali kumandako, mfumu inayamba kulira mokweza mawu ndipo anthu onse anayambanso kulira.+ 33  Zitatero, mfumu inayamba kuimba nyimbo yolira Abineri kuti:“Kodi zoona Abineri afe imfa ngati ya munthu wopanda pake?+ 34  Manja ako sanali omangidwa,+Ndipo mapazi ako sanaikidwe m’matangadza amkuwa.+Wagwa ngati munthu wogwa pamaso pa anthu osalungama.”+Pamenepo anthu onse anamuliranso.+ 35  Pambuyo pake, anthu onse anabwera kwa Davide tsiku lomwelo kudzam’patsa chakudya+ chomutonthoza, koma Davide analumbira kuti: “Mulungu andilange+ mowirikiza ngati ndidzalawa chakudya kapena kena kalikonse dzuwa lisanalowe!”+ 36  Anthu onse anaona zimene zachitika, ndipo anaona kuti zimene mfumu ikuchita zili bwino. Mofanana ndi zonse zimene mfumuyo inachita, anthu onse anaona kuti izinso zili bwino.+ 37  Anthu onse a Davide komanso Isiraeli yense anadziwa tsiku limenelo kuti si mfumu imene inachititsa kuti Abineri mwana wa Nera aphedwe.+ 38  Ndiyeno mfumu inapitiriza kuuza atumiki ake kuti: “Kodi simukudziwa kuti amene wafa leroyu ndi kalonga komanso munthu wamphamvu mu Isiraeli?+ 39  Ine lero ndafooka ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa,+ ndipo ine ndikuona kuti amuna awa, ana a Zeruya,+ achita nkhanza kwambiri.+ Yehova abwezere aliyense wochita zinthu zoipa mogwirizana ndi kuipa kwake.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Pa 1Sa 25:44 akutchedwa Paliti.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “saka.”