2 Samueli 10:1-19

10  Pambuyo pake, mfumu ya ana a Amoni+ inamwalira, ndipo Hanuni mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwa bambo ake.+  Zitachitika zimenezi, Davide anati: “Ndidzasonyeza Hanuni mwana wa Nahasi kukoma mtima kosatha,+ monga mmene bambo ake anandisonyezera kukoma mtima kosatha.” Chotero Davide anatumiza uthenga kudzera mwa atumiki ake+ kuti akatonthoze Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo ake, ndipo atumiki a Davidewo anafika m’dziko la ana a Amoni.  Koma akalonga a ana a Amoni anauza Hanuni mbuye wawo kuti: “Kodi ukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthoza kuti alemekeze bambo ako pamaso pako? Kodi iye sanatumize atumiki akewa kwa iwe kuti adzaonetsetse mzindawu ndi kuchita ukazitape,+ kuti adzaulande?”+  Pamenepo Hanuni anatenga atumiki a Davide aja ndi kuwameta ndevu zonse za mbali imodzi,+ kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza m’matako, n’kuwauza kuti azipita.+  Pambuyo pake anthu anauza Davide zimene zinachitika, ndipo iye nthawi yomweyo anatumiza anthu kuti akakumane ndi atumiki akewo chifukwa atumikiwo anaona kuti awachititsa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ kufikira ndevu zanu zitachuluka ndithu, kenako mudzabwere.”  Patapita nthawi, ana a Amoni anaona kuti akhala chinthu chonunkha+ kwa Davide. Choncho anatumiza nthumwi kuti akalembe ganyu Asiriya a ku Beti-rehobu+ ndi Asiriya a ku Zoba,+ amuna 20,000 oyenda pansi. Anapitanso kwa mfumu ya ku Maaka+ ndi kulemba ganyu amuna 1,000 ndi ku Isitobu amuna 12,000.  Davide atamva zimenezi anatumiza Yowabu ndi gulu lonse lankhondo pamodzi ndi amuna amphamvu.+  Ndiyeno ana a Amoni anapita kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuchipata cha mzinda. Nawonso Asiriya a ku Zoba, a ku Rehobu,+ a ku Isitobu ndi a ku Maaka anafola paokha kutchire.+  Yowabu ataona kuti asilikali a adani ake akubwera mofulumira kuchokera kutsogolo ndi kumbuyo kudzamenyana naye, nthawi yomweyo anatenga amuna ochita kusankhidwa mwapadera+ a mu Isiraeli ndipo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti akumane ndi Asiriya. 10  Anthu ena onse anawapereka m’manja mwa Abisai+ m’bale wake, kuti awatsogolere pofola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ndi kukumana ndi ana a Amoni.+ 11  Ndiyeno anamuuza kuti: “Asiriya akandiposa mphamvu, iweyo undipulumutse. Koma ana a Amoni akakukulira mphamvu, ineyo ndifika kudzakupulumutsa.+ 12  Chita zinthu mwamphamvu, ndipo tisonyeze kulimba mtima+ chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu.+ Yehova adzachita zimene zili zabwino m’maso mwake.”+ 13  Choncho Yowabu ndi amuna amene anali naye anapita kukamenyana ndi Asiriya, moti Asiriya anathawa pamaso pake.+ 14  Pamenepo ana a Amoni ataona kuti Asiriya athawa, nawonso anathawa pamaso pa Abisai ndi kubwerera kwawo.+ Kenako Yowabu anasiya kutsatira ana a Amoni ndi kubwerera ku Yerusalemu.+ 15  Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli, anasonkhana pamodzi. 16  Choncho Hadadezeri+ anatumiza nthumwi kukatenga Asiriya amene anali m’dera la ku Mtsinje.*+ Atatero anabwera ku Helamu pamodzi ndi Sobaki+ mtsogoleri wa gulu lankhondo la Hadadezeri. 17  Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse ndi kuwoloka Yorodano kupita ku Helamu. Ndiyeno Asiriya anafola kuti akumane ndi Davide ndi kuyamba kumenyana naye.+ 18  Asiriyawo anathawa+ pamaso pa Isiraeli, ndipo Davide anapha asilikali a Siriya 700 okwera magaleta,+ ndi asilikali 40,000 okwera pamahatchi. Iye anakanthanso Sobaki, mtsogoleri wa gulu lankhondo la Siriya, moti anafera pomwepo.+ 19  Mafumu onse+ amene anali atumiki a Hadadezeri, ataona kuti agonja pamaso pa Isiraeli,+ nthawi yomweyo anakhazikitsa mtendere ndi Aisiraeli ndi kuyamba kuwatumikira.+ Asiriya sanayesenso kupulumutsa ana a Amoni chifukwa anali kuchita mantha.+

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.