2 Samueli 17:1-29

17  Ndiyeno Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Ndilole chonde, ndisankhe amuna 12,000 kuti ndithamangitse Davide lero usiku.+  Ndimupeza ali wotopa ndi wofooka manja ake onse,+ ndipo adzanjenjemera ndithu chifukwa cha ine. Pamenepo anthu onse amene ali naye adzathawa, ndipo ine ndidzapha mfumu ili yokha.+  Ndilole ndibweretse anthu onse kwa iwe. Pakuti kubwerera kwa anthu onse kukudalira zimene zingachitikire munthu amene ukumusakasakayu, ndipo anthu onse adzakhala mu mtendere.”  Mawu amenewa anali abwino kwa Abisalomu+ ndi kwa akulu onse a Isiraeli.  Koma Abisalomu anati: “Kaitanenso Husai+ Mwareki kuti timve maganizo ake.”  Choncho Husai anabwera kwa Abisalomu. Ndiyeno Abisalomu anamuuza kuti: “Mawu amenewa ndi amene Ahitofeli wanena. Kodi tichite zimene wanenazi? Ngati unena kuti ayi, iweyo tiuze zochita.”  Pamenepo Husai anauza Abisalomu kuti: “Malangizo amene Ahitofeli wapereka ulendo uno sali bwino ayi!”+  Ndiyeno Husai anapitiriza kunena kuti: “Iwe ukuwadziwa bwino bambo wako ndi amuna amene ali nawo kuti iwo ndi amphamvu+ ndipo mitima ikuwapweteka+ ngati chimbalangondo chimene chataya ana ake kuthengo.+ Ukudziwanso bwino kuti bambo wako ndi munthu wankhondo+ ndipo sangagone kumene kuli anthu.  Ndipotu panopa akubisala+ m’dzenje linalake kapena m’malo ena. Ndiyeno iyeyo akakhala woyamba kuukira anthu, nkhani idzafala kuti, ‘Anthu amene akutsatira Abisalomu agonjetsedwa!’ 10  Choncho ngakhale mwamuna wolimba mtima amene ali ndi mtima ngati wa mkango+ adzafooka+ ndithu. Izi zili choncho chifukwa Isiraeli yense akudziwa kuti bambo wako ndi mwamuna wamphamvu,+ ngatinso mmene alili amuna olimba mtima amene ali naye.+ 11  Ndiye ine malangizo anga ndi onena kuti: Sonkhanitsa ndithu Isiraeli yense pamaso pako kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ Akhale ochuluka ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja,+ ndipo iweyo uwatsogolere kunkhondo.+ 12  Ukatero, tikamuukire kumene tikudziwa kuti tikhoza kum’peza,+ ndipo tikam’fikira ngati mmene mame+ amagwera pansi. Pamenepo sipadzakhala aliyense wopulumuka, iyeyo ngakhale amuna onse amene ali naye. 13  Ngati angathawire mumzinda uliwonse, ife tidzapita ndi Isiraeli yense kukawononga mzinda umenewo ndi kuukokera kuchigwa* ndi zingwe. Mumzindawo simudzatsala ngakhale mwala wa nkhulungo.”+ 14  Kenako Abisalomu ndi amuna onse a Isiraeli anati: “Malangizo a Husai Mwareki ndi abwino+ kusiyana ndi malangizo a Ahitofeli!” Ndipo Yehova anaonetsetsa+ kuti anthuwo asatsatire malangizo+ a Ahitofeli ngakhale kuti anali abwino.+ Yehova anachita zimenezi kuti adzetsere Abisalomu tsoka.+ 15  Pambuyo pake Husai anauza Zadoki+ ndi Abiyatara ansembe, kuti: “Ahitofeli wapereka malangizo kwa Abisalomu ndi akulu a Isiraeli ndipo wanena zakutizakuti, koma malangizo amene ine ndapereka, ndanena zakutizakuti. 16  Ndipo tsopano tumizani uthenga mwamsanga kwa Davide+ wakuti, ‘Lero musagone m’chipululu, muwoloke ndithu+ kuopera kuti inu mfumu pamodzi ndi anthu onse amene muli nawo mungamezedwe.’”+ 17  Pamene Yonatani+ ndi Ahimazi+ anali ataimirira pa Eni-rogeli,+ kapolo wamkazi anapita kumeneko ndi kuwauza zonse. Choncho iwo anachoka pakuti anafunika kukauza Mfumu Davide. Iwowa sanayese n’komwe kulowa mumzinda kuopera kuti angawazindikire. 18  Komabe mnyamata wina anawaona ndipo anapita kukauza Abisalomu. Choncho awiriwo anachoka mofulumira ndi kupita kunyumba ya munthu wina amene anali ndi chitsime pakhomo pake ku Bahurimu,+ ndipo iwo analowa m’chitsimemo. 19  Atalowa m’chitsimemo, mkazi wa munthuyo anatenga chotchingira ndi kuchiyala pachitsimepo, kenako anaunjikapo tirigu wosinja,+ ndipo palibe amene anadziwa chilichonse. 20  Tsopano atumiki a Abisalomu anafika kunyumba ya mkaziyo n’kunena kuti: “Kodi Ahimazi ndi Yonatani ali kuti?” Poyankha mkaziyo anawauza kuti: “Adutsa pano kulowera kumtsinje.”+ Pamenepo anapitiriza kuwafunafuna koma sanawapeze,+ choncho anabwerera ku Yerusalemu. 21  Ndiyeno atumiki a Abisalomu atachoka, Ahimazi ndi Yonatani anatuluka m’chitsimemo ndi kupita kukauza Mfumu Davide kuti: “Anthu inu nyamukani mwamsanga muwoloke mtsinje, pakuti Ahitofeli wapereka malangizo+ ndipo wanena zakutizakuti kuti athane nanu.” 22  Nthawi yomweyo Davide ananyamuka pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, ndipo anawoloka Yorodano mpaka m’mawa.+ Onse anawoloka Yorodano popanda wotsala. 23  Koma Ahitofeli ataona kuti malangizo ake sanawagwiritse ntchito,+ anakwera bulu wake ndi kunyamuka kupita kunyumba yake kumzinda wakwawo.+ Kenako anakonzekeretsa banja lake+ ndipo anadzimangirira+ moti anafa.+ Chotero anaikidwa m’manda+ a makolo ake. 24  Davide anafika ku Mahanaimu+ ndipo Abisalomu nayenso anawoloka Yorodano pamodzi ndi amuna onse a Isiraeli amene anali naye. 25  Ndiyeno Abisalomu anasankha Amasa+ kukhala mtsogoleri wagulu lankhondo kulowa m’malo mwa Yowabu.+ Amasa anali mwana wa munthu wina dzina lake Itara,+ Mwisiraeli amene anagona ndi Abigayeli,+ mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wake wa Zeruya, mayi wake wa Yowabu. 26  Isiraeli ndi Abisalomu anamanga msasa m’dziko la Giliyadi.+ 27  Ndiyeno zimene zinachitika n’zakuti, Davide atangofika ku Mahanaimu, Sobi mwana wamwamuna wa Nahasi, wochokera ku Raba,+ mzinda wa ana a Amoni,+ komanso Makiri+ mwana wa Amiyeli,+ wochokera ku Lo-debara ndi Barizilai+ Mgiliyadi wochokera ku Rogelimu,+ 28  anabweretsa makama, mabeseni, ziwiya zadothi, tirigu, balere, ufa,+ tirigu wokazinga,+ nyemba zikuluzikulu,+ mphodza+ ndi tirigu wowamba. 29  Iwo anabweretsanso uchi,+ mafuta a mkaka,+ wa ng’ombe ndiponso nkhosa. Anabweretsa zinthu zimenezi kuti Davide ndi anthu onse amene anali naye adye.+ Iwo anali kunena kuti: “Anthu amenewa ali ndi njala, atopa ndipo ali ndi ludzu m’chipululu.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.