2 Samueli 20:1-26

20  Tsopano panali munthu wina wopanda pake+ dzina lake Sheba,+ mwana wamwamuna wa Bikiri, wafuko la Benjamini. Iye analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ ndi kunena kuti: “Tilibe gawo mwa Davide, ndipo tilibe cholowa mwa mwana wa Jese.+ Aisiraeli inu, aliyense apite kwa milungu+ yake!”  Pamenepo anthu onse a Isiraeli anayamba kuchoka kwa Davide ndi kutsatira Sheba mwana wa Bikiri.+ Koma anthu a ku Yuda, kuyambira ku Yorodano mpaka ku Yerusalemu anamamatira mfumu yawo.+  Patapita nthawi, Davide anafika kunyumba yake ku Yerusalemu.+ Ndiyeno mfumuyo inatenga akazi 10+ aja, adzakazi amene anawasiya kuti azisamalira nyumba yake, ndipo anawatsekera m’nyumba ina koma anapitiriza kuwapatsa chakudya. Iye sanagone nawonso,+ koma anawatsekerabe kufikira tsiku la kufa kwawo. Iwo anakhala akazi amasiye mwamuna wawo ali moyo.  Tsopano mfumu inauza Amasa+ kuti: “Ndisonkhanitsire anthu a mu Yuda m’masiku atatu, ndipo iwe uime pano.”  Choncho Amasa anapita kukasonkhanitsa anthu a mu Yuda, koma anabwera mochedwa kupitirira nthawi imene anamuikira.  Ndiyeno Davide anauza Abisai+ kuti: “Tsopano Sheba+ mwana wamwamuna wa Bikiri atisautsa kwambiri kuposa Abisalomu.+ Iweyo utenge atumiki+ a mbuye wako ndi kumuthamangitsa kuti asapeze mizinda ya mipanda yolimba kwambiri ndi kutizemba ife tikuona.”  Choncho asilikali a Yowabu,+ Akereti,+ Apeleti+ ndi amuna onse amphamvu anayamba kumuthamangitsa. Iwo anatuluka mu Yerusalemu ndi kuthamangitsa Sheba mwana wa Bikiri.  Pamene anali pafupi ndi mwala waukulu umene uli ku Gibeoni,+ Amasa+ anabwera kudzakumana nawo. Tsopano Yowabu anali atavala malaya ankhondo ndi lamba. Iye anali ataika lupanga m’chimake ndi kulipachika m’chiuno mwake. Atayandikira Amasa, lupangalo linagwa pansi.  Ndiyeno Yowabu anafunsa Amasa kuti: “Kodi zili bwino m’bale wanga?”+ Kenako dzanja lamanja la Yowabu linagwira ndevu za Amasa kuti amupsompsone.+ 10  Koma Amasa sanachenjere ndi lupanga limene linali m’manja mwa Yowabu. Choncho Yowabuyo anamubaya+ nalo m’mimba ndipo matumbo ake anakhuthukira pansi, moti sanachite kumubaya kawiri. Chotero Amasa anafa. Pamenepo Yowabu ndi Abisai m’bale wake anathamangitsa Sheba mwana wa Bikiri. 11  Zitatero, mmodzi mwa anyamata a Yowabu anaimirira pafupi ndi Amasa ndipo anali kunena kuti: “Aliyense amene amagwirizana ndi Yowabu ndiponso aliyense wa Davide+ atsatire Yowabu!” 12  Ankachita izi Amasa ali chigonere pamagazi ake,+ pakati pa msewu waukulu. Mwamuna uja ataona kuti anthu onse akuima chilili, anakoka Amasa kumuchotsa pamsewu ndi kumuika patchire. Kenako anamuphimba ndi chovala pakuti anaona kuti aliyense amene anali kufika pamenepo anali kuima chilili.+ 13  Atangomuchotsa pamsewupo, munthu aliyense anali kudutsa pamenepo kutsatira Yowabu pothamangitsa Sheba+ mwana wa Bikiri. 14  Tsopano Sheba anadutsa pakati pa mafuko onse a Isiraeli kupita kumzinda wa Abele wa ku Beti-maaka.+ Nawonso Abikiri onse anasonkhana ndi kuyamba kumuthamangitsa. 15  Anthuwo anafika ndi kumuzungulira ali mumzinda+ wa Abele wa ku Beti-maaka. Iwo anamanga chiunda chomenyerapo nkhondo* ndi mzindawo. Anthu onse amene anali ndi Yowabu anali kukumba pansi pa mpandawo kuti augwetse. 16  Ndiyeno mkazi wina wanzeru+ mumzindawo anayamba kufuula kuti: “Tamverani amuna inu, tamverani! Chonde muuzeni Yowabu kuti abwere pafupipa kuti ndilankhule naye.” 17  Choncho Yowabu anayandikira ndipo mkaziyo anati: “Kodi ndiwe Yowabu?” Pamenepo Yowabu anayankha kuti: “Inde, ndine.” Pamenepo mkaziyo anati: “Tamvera mawu a kapolo wako wamkazi.”+ Yowabu anayankha kuti: “Ndikumvetsera.” 18  Ndiyeno mkaziyo ananena kuti: “Nthawi zakale aliyense anali kunena kuti, ‘Akafunsire nzeru ku Abele, ndipo adzapezadi njira yothetsera nkhani yake.’ 19  Ine ndikuimira anthu ofuna mtendere+ ndi okhulupirika+ a mu Isiraeli. Iwe ukufuna kupha mzinda+ ndi mayi mu Isiraeli. N’chifukwa chiyani ukufuna kuwononga+ cholowa+ cha Yehova?” 20  Pamenepo Yowabu anayankha kuti: “Ine sindingawononge ndi kufafaniza mzindawu, n’zosatheka zimenezo. 21  Nkhani sili choncho ayi, koma mumzinda wanu muli munthu wochokera kudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Sheba+ mwana wa Bikiri, amene waukira Mfumu Davide.+ Choncho anthu inu m’perekeni iye yekhayo+ m’manja mwathu, ndipo ine ndidzachoka kumzinda+ uno.” Pamenepo mkaziyo anauza Yowabu kuti: “Tikuponyerani mutu+ wake kuchokera pamwamba pa mpanda!” 22  Nthawi yomweyo, mkaziyo anapita mwa nzeru+ zake kwa anthu onse, ndipo anthuwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri ndi kuuponya kwa Yowabu. Zitatero, Yowabu analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ moti anthu onse anabalalika kuchoka kumzindawo ndi kupita kwawo. Yowabu nayenso anabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu. 23  Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lonse lankhondo+ la Isiraeli. Benaya+ mwana wa Yehoyada+ anali kutsogolera Akereti+ ndi Apeleti.+ 24  Adoramu+ anali kutsogolera anthu olembedwa ntchito yokakamiza, ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi anali wolemba zochitika. 25  Seva+ anali mlembi,+ ndipo Zadoki+ ndi Abiyatara+ anali ansembe. 26  Ira Myairi anakhalanso wansembe*+ wa Davide.

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 8:18.