2 Samueli 14:1-33

14  Tsopano Yowabu,+ mwana wa Zeruya+ anadziwa kuti mtima wa mfumu ukulakalaka Abisalomu.+  Choncho Yowabu anatumiza anthu ku Tekowa+ kuti akatenge mkazi wanzeru.+ Atabwera naye, Yowabu anamuuza kuti: “Chonde ukhale ngati munthu amene ali panyengo yolira maliro, ndipo uvale zovala za panyengo yolira maliro, komanso usadzole mafuta.+ Ukatero ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira maliro kwa masiku ambiri.+  Ndiyeno upite kuti ukaonekere kwa mfumu ndipo ukalankhule nayo mawu awa.” Atatero, Yowabu anamuuza zokanena.+  Pamenepo mkazi wa ku Tekowa uja anapita kukaonana ndi mfumu, ndipo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ kenako anadzigwetsa pansi, n’kunena kuti: “Chonde mfumu, ndipulumutseni!”+  Ndiyeno mfumu inamufunsa kuti: “Kodi chavuta ndi chiyani?” Mkaziyo anayankha kuti: “Ine ndine mkazi wamasiye,+ pakuti mwamuna wanga anamwalira.  Ndiyeno ine mtumiki wanu ndinali ndi ana awiri aamuna. Tsiku lina anawo anayamba kulimbana ali kuthengo+ kopanda munthu wowaleretsa.+ Pamapeto pake wina anakantha mnzake ndi kumupha.  Tsopano banja lonse landiukira ine mtumiki wanu ndipo aliyense akunena kuti, ‘Bweretsa wopha m’bale wakeyo+ kuti timuphe chifukwa cha moyo wa m’bale wake amene anamupha,+ ndipo tiwononge wolandira cholowayo!’ Tsopano anthuwa adzazimitsa makala anga onyeka otsalawo, kuti pasakhale wosunga dzina la mwamuna wanga kapena mbewu yake yotsala padziko lapansi.”+  Ndiyeno mfumu inauza mkaziyo kuti: “Pita kunyumba kwako ndipo ine ndisamalira nkhani imeneyi.”+  Pamenepo mkazi wa ku Tekowayo anauza mfumu kuti: “Mbuyanga mfumu, kulakwa kukhale kwanga ndi kwa nyumba ya bambo anga,+ koma mfumu ndi mpando wake wachifumu ndi zosalakwa.” 10  Mfumu inapitiriza kunena kuti: “Ngati aliyense angakufunse nkhani imeneyi, ubwere naye kwa ine ndipo sadzakuzunzanso.” 11  Koma mkaziyo anati: “Chonde mfumu, kumbukirani Yehova Mulungu wanu+ kuti munthu wobwezera magazi+ asapitirize kuwononga, ndi kuti anthu amenewa asaphe mwana wanga.” Pamenepo mfumu inati: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ ngakhale tsitsi limodzi+ la mwana wako silidzagwa pansi.” 12  Ndiyeno mkaziyo anati: “Ndiloleni ine mtumiki wanu,+ chonde, ndilankhule mawu amodzi+ kwa inu mbuyanga mfumu.” Mfumu inamuuza kuti: “Lankhula!”+ 13  Ndiyeno mkaziyo anapitiriza kunena kuti: “N’chifukwa chiyani inu mfumu mwachitira+ anthu a Mulungu+ zinthu zowawononga? Popeza inu mfumu munapitikitsa+ mwana wanu, ndipo mwalephera kumuitanitsa, muli ndi mlandu+ pa zimene mwafotokozazi. 14  Tonsefe tidzafa+ ndi kukhala ngati madzi otayika amene sawoleka. Koma Mulungu wakonza zinthu+ ndipo ali ndi zifukwa zothandiza kuti munthu wopitikitsidwa asapitirize kukhala wopitikitsidwa. 15  Chifukwa chakuti anthu andichititsa mantha, ndabwera kudzalankhula mawu amenewa ndi inu mbuyanga mfumu. N’chifukwa chake ine mtumiki wanu ndinati, ‘Ndiloleni chonde ndilankhule nanu mfumu. Mwina mfumu idzachitapo kanthu pa mawu a kapolo wanu wamkazi. 16  Choncho, chifukwa chakuti mfumu yandimvera kuti indilanditse ine kapolo wake wamkazi m’manja mwa munthu wofuna kuwononga ine ndi mwana wanga wamwamuna yekhayo, kutichotsa pa cholowa chathu choperekedwa ndi Mulungu,’+ 17  ine mtumiki wanu ndinaganiza kuti, ‘Mawu a mbuyanga mfumu andipatsa mpumulo.’ Pakuti inu mbuyanga mfumu muli ngati mngelo+ wa Mulungu woona, wokhoza kusiyanitsa chabwino ndi choipa.+ Ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.” 18  Tsopano mfumu inayankha mkaziyo kuti: “Usandibisire kalikonse pa zimene ndikufuna kukufunsa.”+ Pamenepo mkaziyo ananena kuti: “Lankhulani mbuyanga mfumu.” 19  Ndiyeno mfumu inamufunsa kuti: “Kodi Yowabu+ ndi amene wakutuma?”+ Pamenepo mkaziyo anayankha kuti: “Pali moyo wanu+ mbuyanga mfumu, palibe munthu angapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere pa zonse zimene inu mbuyanga mfumu mwanena. Mtumiki wanu Yowabu ndi amene wandituma ndi kundiuza zonse zimene ndalankhula nanu.+ 20  Mtumiki wanu Yowabu wachita zimenezi kuti asinthe mmene mukuonera nkhaniyi. Koma inu mbuyanga muli ndi nzeru ngati mngelo+ wa Mulungu woona, moti mukudziwa zonse za padziko lapansi.” 21  Zitatero, mfumu inauza Yowabu kuti: “Chabwino, ndichita zimene wanena.+ Choncho pita ukatenge mnyamatayo Abisalomu ndipo ubwere naye.”+ 22  Yowabu atamva zimenezi anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndi kudalitsa mfumu,+ n’kunena kuti: “Lero ndadziwa kuti ine mtumiki wanu mwandikomera mtima,+ mbuyanga mfumu, chifukwa chakuti inu mfumu mwamvera mawu anga ine mtumiki wanu.” 23  Yowabu atanena mawu amenewa ananyamuka ndi kupita ku Gesuri,+ ndipo anabweretsa Abisalomu ku Yerusalemu.+ 24  Koma mfumu inanena kuti: “Apite kunyumba kwake, koma asaone nkhope yanga.”+ Choncho Abisalomu anatembenukira kunyumba kwake, ndipo sanaonane ndi mfumu. 25  Tsopano mu Isiraeli yense munalibe mwamuna wina wotamandika kwambiri koposa Abisalomu chifukwa cha kukongola kwake.+ Iye analibe chilema chilichonse kuyambira kuphazi mpaka paliwombo. 26  Abisalomu anali kumeta tsitsi lake kumapeto kwa chaka chilichonse chifukwa linali kumulemera kwambiri.+ Ndipo akameta tsitsi lakelo, anali kuliyeza kulemera kwake ndipo linali kukwana masekeli* 200 poliyeza ndi mwala wachifumu woyezera kulemera kwa zinthu.* 27  Abisalomu anabereka ana aamuna atatu+ ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake Tamara. Ameneyu anali chiphadzuwa chadzaoneni.+ 28  Abisalomu anapitiriza kukhala m’Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, ndipo sanaonane ndi mfumu.+ 29  Zitatero, Abisalomu anaitanitsa Yowabu kuti amutume kwa mfumu, koma Yowabu sanalole kupita kwa Abisalomu. Iye anamuitanitsanso kachiwiri, koma sanalole kuti apite kwa Abisalomu. 30  Pamapeto pake, Abisalomu anauza atumiki ake kuti: “Pafupi ndi munda wanga pali munda wa Yowabu umene uli ndi balere. Mupite kumeneko ndipo mukautenthe ndi moto.”+ Choncho atumiki a Abisalomu anatentha mundawo ndi moto.+ 31  Pamenepo Yowabu ananyamuka n’kupita kunyumba kwa Abisalomu. Atafika kumeneko anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani atumiki ako anatentha munda wanga?” 32  Abisalomu anayankha kuti: “Ine ndinakutumizira uthenga wonena kuti, ‘Ubwere kuno ndikutume kwa mfumu ukaiuze kuti: “N’chifukwa chiyani ndinabwerako ku Gesuri?+ Zikanakhala bwino ndikanangokhalabe komweko. Tsopano ndikufuna ndionane ndi mfumu, ndipo ngati ndili wolakwa,+ mfumu indiphe.”’” 33  Chotero Yowabu anapita kukaonana ndi mfumu ndipo anaiuza mawu amenewa. Ndiyeno mfumu inaitanitsa Abisalomu, moti iye anabwera kudzaonana ndi mfumu. Abisalomu atafika anagwada ndi kuwerama, kenako anadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Zitatero, mfumu inapsompsona Abisalomu.+

Mawu a M'munsi

“Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
Umenewu uyenera kuti unali muyezo umene anali kuusunga kunyumba ya mfumu kapena linali sekeli “lachifumu” losiyana ndi sekeli wamba. Yerekezerani ndi mawu a m’munsi pa Eks 30:13.