2 Samueli 6:1-23

6  Davide anasonkhanitsanso amuna onse osankhidwa mwapadera mu Isiraeli,+ okwana 30,000.  Ndiyeno Davide ndi anthu onse amene anali naye ananyamuka ndi kupita ku Baale-yuda+ kuti akatenge likasa+ la Mulungu woona. Pa likasa limeneli amaitanira dzina+ la Yehova wa makamu,+ wokhala pamwamba pa akerubi.+  Koma iwo anakweza likasa la Mulungu woona pangolo yatsopano+ kuti alichotse kunyumba ya Abinadabu+ imene inali paphiri. Uza ndi Ahiyo,+ ana aamuna a Abinadabu, anali kutsogolera ngolo yatsopanoyo.  Choncho ananyamula likasa la Mulungu woona kulichotsa kunyumba ya Abinadabu imene inali paphiri, ndipo Ahiyo anali kuyenda patsogolo pa Likasa.  Davide pamodzi ndi nyumba yonse ya Isiraeli anali kusangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Anali kuimbanso zeze,+ zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana.  Kenako anafika kumalo opunthira mbewu a ku Nakoni, ndipo Uza+ anatambasulira dzanja lake pa likasa la Mulungu woona n’kuligwira,+ chifukwa ng’ombe zinatsala pang’ono kuligwetsa.  Pamenepo mkwiyo wa Yehova+ unayakira Uza ndipo Mulungu woona anamukantha+ pomwepo chifukwa cha kuchita chinthu chosalemekeza Mulungu chimenechi. Moti Uza anafera pomwepo, pafupi ndi likasa la Mulungu woona.+  Zitatero, Davide anakwiya chifukwa mkwiyo wa Yehova unaphulikira Uza modzidzimutsa. Chotero malo amenewo amatchedwa dzina lakuti Perezi-uza* kufikira lero.+  Tsiku limenelo, Davide anachita mantha kwambiri chifukwa cha Yehova,+ ndipo anati: “Kodi likasa la Yehova lidzabwera bwanji kumene ine ndikukhala?”+ 10  Pamenepo Davide sanafunenso kutenga likasa la Yehova kupita nalo kumene iye anali kukhala, ku Mzinda wa Davide.+ Chotero Davide analipatutsira kunyumba ya Obedi-edomu+ Mgiti.+ 11  Likasa la Yehova linakhalabe kunyumba ya Obedi-edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anapitiriza kudalitsa+ Obedi-edomu ndi banja lake lonse.+ 12  Pamapeto pake uthenga unafika kwa Mfumu Davide wonena kuti: “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-edomu ndi zake zonse chifukwa cha likasa la Mulungu woona.” Davide atamva mawu amenewa anapita kukatenga likasa la Mulungu woona kunyumba kwa Obedi-edomu ndi kupita nalo ku Mzinda wa Davide, akusangalala.+ 13  Tsopano onyamula+ likasa la Yehova atangoyenda mapazi 6, nthawi yomweyo Davide anapereka nsembe ng’ombe yamphongo ndi chiweto chonenepa.+ 14  Davide ankavina mozungulira pamaso pa Yehova ndi mphamvu zake zonse. Apa n’kuti Davide atavala efodi+ wansalu. 15  Davide ndi nyumba yonse ya Isiraeli anali kupita ndi likasa+ la Yehova, akufuula mokondwera+ ndi kuimba lipenga la nyanga ya nkhosa.+ 16  Ndiyeno pamene likasa la Yehova linalowa mu Mzinda wa Davide, Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pawindo kuyang’ana pansi ndipo anaona Mfumu Davide akudumphadumpha ndi kuvina mozungulira pamaso pa Yehova. Pamenepo Mikala anayamba kum’peputsa+ mumtima mwake.+ 17  Ndiyeno analowetsa likasa la Yehova muhema limene Davide anamanga n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako Davide anapereka kwa Yehova nsembe zopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+ 18  Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, anadalitsa+ anthu m’dzina la Yehova+ wa makamu. 19  Kuwonjezera apo, anthu onse, khamu lonse la Isiraeli, mwamuna komanso mkazi, aliyense wa iwo anapatsidwa+ keke yozungulira yoboola pakati, zipatso za kanjedza zouma zoumba pamodzi ndi mphesa zouma zoumba pamodzi.+ Kenako aliyense wa anthuwo anapita kunyumba yake. 20  Tsopano Davide anabwerera kunyumba kwake kuti akadalitse banja lake.+ Pamenepo Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kukakumana naye ndipo anati: “Lerotu mfumu ya Isiraeli yaonetsa ulemerero wake+ mwa kudzivula pamaso pa akapolo aakazi a atumiki ake, monga mmene munthu wopanda nzeru amadzivulira mopanda manyazi ngakhale pang’ono!”+ 21  Poyankha, Davide anauza Mikala kuti: “Ine ndinali kusangalala pamaso pa Yehova amene anandisankha kuti ndikhale mtsogoleri+ wa anthu a Yehova, Aisiraeli, m’malo mwa bambo ako ndi banja lawo lonse, ndipo ndidzasangalala pamaso pa Yehova.+ 22  Ndipotu ndipitiriza kudzipeputsa kuposa pamenepa,+ moti ndidzichepetsa m’maso mwanga. Ndine wotsimikiza mtima kudzipezera ulemerero pamaso pa akapolo aakazi amene ukunenawo.”+ 23  Choncho Mikala+ mwana wamkazi wa Sauli sanakhalepo ndi mwana mpaka tsiku la imfa yake.

Mawu a M'munsi

Dzinali limatanthauza, “Mkwiyo Wophulikira Uza.”