2 Samueli 1:1-27

1  Sauli atamwalira, ndiponso Davide atabwera kuchokera kokakantha Aamaleki,+ Davideyo anakhala ku Zikilaga+ masiku awiri.  Ndiyeno pa tsiku lachitatu anaona munthu wina+ akubwera kuchokera kumsasa, kwa Sauli. Iye anali atang’amba zovala zake+ komanso atadzithira dothi kumutu.+ Atafika kwa Davide, nthawi yomweyo anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi+ kenako anagona pansi.  Pamenepo Davide anamufunsa kuti: “Wachokera kuti?” Poyankha iye anati: “Ndathawa kumsasa wa Isiraeli.”  Kenako Davide anamufunsa kuti: “Zayenda bwanji kumeneko? Chonde, ndiuze.” Iye anayankha kuti: “Anthu athawa kunkhondo komanso anthu ambiri agwa ndipo afa,+ ngakhalenso Sauli+ ndi mwana wake Yonatani+ afa.”  Pamenepo Davide anafunsa mnyamata amene anali kumuuza nkhaniyo kuti: “Iweyo wadziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afadi?”+  Mnyamatayo anayankha kuti: “Ndinapezeka kuti ndili paphiri la Giliboa,+ ndipo ndinaona Sauli atatsamira mkondo+ wake. Zili choncho, ndinaona asilikali oyenda m’magaleta ndi asilikali okwera pamahatchi* akumuyandikira.+  Sauliyo atatembenuka n’kundiona, anandiitana, ndipo ine ndinayankha kuti, ‘Ine mbuyanga!’  Kenako anandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe ndani?’ Ine ndinamuyankha kuti, ‘Ndine Mwamaleki.’+  Ndiyeno anandiuza kuti, ‘Bwera kuno chonde, undiphe pakuti zinthu zandivuta,* koma ndidakali ndi moyo.’+ 10  Choncho ndinapita pamene iye anali ndi kumupha,+ chifukwa ndinadziwa kuti sakhalanso ndi moyo popeza anali atavulala kwambiri. Kenako ndinatenga chisoti chachifumu+ chimene anavala ndi khoza limene linali kudzanja lake kuti ndibwere nazo kuno kwa inu mbuyanga.” 11  Davide atamva zimenezi anagwira zovala zake ndi kuzing’amba.+ Nawonso amuna onse amene anali ndi Davide anang’amba zovala zawo. 12  Atatero, anayamba kulira ndi kubuma+ komanso kusala kudya+ mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi Yonatani mwana wake, komanso chifukwa cha anthu a Yehova ndi anthu a nyumba ya Isiraeli,+ amene anali atakanthidwa ndi lupanga. 13  Ndiyeno Davide anafunsa mnyamata amene anali kumuuza nkhaniyo kuti: “Kodi kwanu n’kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndine mwana wa Mwamaleki, mlendo wokhala pakati pa Aisiraeli.”+ 14  Pamenepo Davide anati: “Zinatheka bwanji iwe osaopa+ kutambasula dzanja lako ndi kukantha wodzozedwa+ wa Yehova?” 15  Atatero, Davide anaitana mmodzi mwa anyamata ake ndi kumuuza kuti: “Mukanthe.” Chotero anamukanthadi, moti anafa.+ 16  Kenako Davide anamuuza kuti: “Mlandu wa magazi ako ukhale pamutu pako,+ chifukwa wadzichitira wekha umboni+ ponena kuti, ‘Ineyo ndapha wodzozedwa wa Yehova.’”+ 17  Ndiyeno Davide anayamba kuimba nyimbo iyi yoimba polira,+ pamene anali kulira Sauli ndi Yonatani mwana wake.+ 18  Iye ananenanso kuti, ana a Yuda+ aphunzitsidwe nyimboyi, yotchedwa “Uta.”+ Nyimbo imeneyi inalembedwa m’buku la Yasari:+ 19  “Isiraeli iwe, anthu ako aulemerero aphedwa pamalo ako okwezeka.+Haa! Anthu amphamvu agwa. 20  Anthu inu musanene zimenezi mumzinda wa Gati.+Musalengeze zimenezi m’misewu ya Asikeloni,+Kuopera kuti ana aakazi a Afilisiti angasangalale,+Kuopera kuti ana aakazi a anthu osadulidwa angakondwere. 21  Inu mapiri a Giliboa,+ musalole kuti mame kapena mvula igwe pa inu. Musalole kuti minda imene ili pa inu ibale zipatso zokaperekedwa kwa Mulungu.*+Chifukwa pa inu chishango cha amuna amphamvu chinadetsedwa,Chishango cha Sauli, moti palibenso chishango chimene chinadzozedwa ndi mafuta.+ 22  Uta wa Yonatani sunkalephera kupha adani ndi kukhetsa magazi awo,Sunkalephera kubaya mafuta a anthu amphamvu.+Lupanga la Sauli silinkabwerako chabe osakwaniritsa ntchito yake.+ 23  Sauli ndi Yonatani,+ anthu okondeka ndi osangalatsa pamene anali ndi moyo,Ngakhale pa imfa yawo sanasiyane.+Iwo anali aliwiro kuposa chiwombankhanga,+Amphamvu kuposa mikango.+ 24  Ana aakazi a Isiraeli inu, mulirireni Sauli,Amene anakuvekani zovala zamtengo wapatali* ndi zinthu zokongoletsa,Amene anaika zokongoletsa zagolide pazovala zanu.+ 25  Haa! Anthu amphamvu agwa pa nkhondo.+Yonatani waphedwa pamalo anu okwezeka!+ 26  Mtima wanga ukuwawa chifukwa cha iwe m’bale wanga Yonatani,Unali wosangalatsa kwambiri kwa ine.+Chikondi chako chinali chapamwamba kwambiri kuposa chikondi cha akazi.+ 27  Haa! Anthu amphamvu agwa,+Ndipo zida zankhondo zawonongeka.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “hosi” kapena “kavalo.”
N’kutheka kuti mawu akuti “zinthu zandivuta,” akusonyeza kuti chinachake chinali chitamuchitikira moti sakanathanso kudziteteza.
Mawu ake enieni, “minda ya zopereka zopatulika.”
Mawu ake enieni, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.