2 Samueli 23:1-39

23  Mawu omaliza amene Davide ananena ndi awa:+“Mawu a Davide mwana wa Jese,+Mawu a munthu wamphamvu amene anakwezedwa pamwamba,+Wodzozedwa+ wa Mulungu wa Yakobo,Munthu wosangalatsa wotchulidwa m’nyimbo zokoma+ za Isiraeli.   Mzimu wa Yehova unandilankhulitsa,+Ndipo mawu ake anali palilime langa.+   Mulungu wa Isiraeli analankhula,Thanthwe la Isiraeli linandiuza kuti,+‘Munthu wolamulira anthu akakhala wolungama,+N’kumalamulira moopa Mulungu,+   Ulamuliro wake umakhala ngati kuwala kwa m’mawa pamene dzuwa lawala,+M’mawa wopanda mitambo.Umakhala ngati msipu womera padziko mvula ikakata, dzuwa n’kuwala.’+   Kodi si mmene nyumba yanga ilili kwa Mulungu?+Chifukwa chakuti anachita nane pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+Analikonza bwino ndipo n’lotetezeka.+Chifukwa ndilo chipulumutso changa+ ndi chondikondweretsa,Kodi chimenechi sindicho chifukwa chake adzakulitsa panganoli?+   Koma anthu onse opanda pake+ amawakankhira kutali+ ngati zitsamba zaminga.+Pakuti zitsamba zamingazo sizigwiridwa ndi manja pozichotsa.   Munthu akamazigwiraAyenera kukhala ndi zida zachitsulo ndi mkondo,Ndipo zidzatenthedwa ndi moto n’kupseratu.”+  Mayina a amuna amphamvu+ a Davide ndi awa: Yosebu-basebete+ Mtahakemoni, mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake n’kupha anthu 800 ulendo umodzi.  Womutsatira anali Eleazara+ mwana wa Dodo+ mwana wa Ahohi. Iye anali mmodzi mwa amuna atatu amphamvu amene anali ndi Davide pamene anatonza Afilisiti. Iwo anasonkhana kumeneko kuti amenye nkhondo, ndipo amuna a Isiraeli anali atathawa.+ 10  Eleazara ndi amene anaimirira ndipo anali kupha Afilisiti mpaka dzanja lake linatopa, koma anagwirabe lupanga+ moti Yehova anapereka chipulumutso chachikulu pa tsiku limenelo.+ Koma anthu ena onse anamutsatira pambuyo pake kuti avule zovala za anthu ophedwawo.+ 11  Womutsatira anali Shama, mwana wamwamuna wa Age Mharari.+ Tsopano Afilisiti anasonkhana pamodzi ku Lehi, kumene kunali munda wodzaza ndi mphodza.+ Kumeneko anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo. 12  Koma iye anaima pakati pa kachigawo ka mundako ndi kukalanditsa ndipo anapitiriza kupha Afilisiti, moti tsiku limenelo Yehova anapereka chipulumutso chachikulu.+ 13  Ndiyeno pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri 30+ anapita kwa Davide kuphanga la Adulamu.+ Apa n’kuti Afilisiti atamanga msasa wa mahema m’chigwa cha Arefai.+ 14  Pamenepo n’kuti Davide ali m’malo ovuta kufikako,+ ndiponso n’kuti mudzi wa asilikali+ a Afilisiti uli ku Betelehemu. 15  Patapita nthawi, Davide anafotokoza zimene anali kulakalaka kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chili pachipata!”+ 16  Pamenepo amuna atatu amphamvu aja anakalowa mwamphamvu mumsasa wa Afilisiti, n’kutunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu chimene chinali pachipata. Atatero ananyamula madziwo n’kupita nawo kwa Davide.+ Koma iye anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.+ 17  Ndiyeno iye anati: “Sindingachite zimenezo+ inu Yehova! Kodi ndimwe magazi+ a amuna amene anaika miyoyo yawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Choncho iye sanavomere kumwa madziwo. Izi n’zimene amuna atatu amphamvuwo anachita. 18  Koma Abisai,+ m’bale wake wa Yowabu mwana wa Zeruya+ anali mtsogoleri wa anthu 30 amenewo. Iye ananyamula mkondo ndi kupha nawo anthu 300. Abisai anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+ 19  Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, ndipo anali mtsogoleri wawo, komabe sanafanane ndi amuna atatu oyamba aja.+ 20  Benaya+ mwana wa Yehoyada,+ mwana wa munthu wolimba mtima, anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu, ndipo analowanso m’chitsime chopanda madzi n’kupha mkango+ umene unali m’chitsimemo pa tsiku limene kunagwa chipale chofewa.+ 21  Benaya ndiye anaphanso Mwiguputo wa msinkhu waukulu modabwitsa.+ Ngakhale kuti Mwiguputoyo anali ndi mkondo m’manja mwake, Benaya anapitabe kukakumana naye atanyamula ndodo, n’kulanda mkondowo ndipo anamupha ndi mkondo wake womwewo.+ 22  Zimenezi n’zimene Benaya+ mwana wa Yehoyada anachita. Iye anali wotchuka ngati amuna atatu amphamvu aja.+ 23  Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna ena 30 aja, sanafanane ndi amuna atatu aja. Koma Davide anamuika kukhala msilikali wake womulondera.+ 24  Asaheli+ m’bale wake wa Yowabu anali m’gulu la amuna 30 aja. M’gululi munalinso Elihanani+ mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, 25  Shama+ Mharodi, Elika Mharodi, 26  Helezi+ Mpaliti, Ira+ mwana wa Ikesi+ Mtekowa, 27  Abi-ezeri+ Muanatoti,+ Mebunai Mhusati,+ 28  Zalimoni Mwahohi,+ Maharai+ Mnetofa, 29  Helebi+ mwana wa Bana Mnetofa, Itai+ mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa fuko la ana a Benjamini, 30  Benaya+ Mpiratoni, Hidai wa kuzigwa* za Gaasi,+ 31  Abi-aliboni Mwaraba, Azimaveti+ M’bahurimu, 32  Eliyaba Msaaliboni, ana a Yaseni, Yonatani,+ 33  Shama Mharari, Ahiyamu+ mwana wa Sarari Mharari, 34  Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaakati, Eliyamu mwana wa Ahitofeli+ Mgilo, 35  Heziro+ wa ku Karimeli, Paarai Mwarabu, 36  Igali mwana wa Natani+ wa ku Zoba, Bani Mgadi, 37  Zeleki+ Muamoni, Naharai M’beeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, 38  Ira Muitiri,+ Garebi+ Muitiri, 39  ndi Uriya+ Mhiti, onse pamodzi 37.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.