2 Samueli 12:1-31

12  Tsopano Yehova anatuma Natani+ kwa Davide. Natani atafika kwa Davide+ anamuuza kuti: “Panali amuna awiri amene anali kukhala mumzinda umodzi. Wina anali wolemera ndipo wina anali wosauka.  Munthu wolemera uja anali ndi nkhosa ndi ng’ombe zambiri.+  Koma munthu wosauka uja anali ndi kamwana ka nkhosa kamodzi kokha kakakazi kamene anagula.+ Iye anali kusunga kamwana ka nkhosako ndipo kanali kukula pamodzi ndi ana ake. Munthuyo anali kudya ndi kumwa nako pamodzi ndipo kanali kugona pachifuwa chake. Kwa iye kanali ngati mwana wake wamkazi.  Patapita nthawi, kwa munthu wolemera uja kunabwera mlendo. Koma munthu wolemerayo sanatenge zina mwa nkhosa zake ndi ng’ombe zake kuti akonzere mlendo amene anabwera kwawoyo. M’malomwake, anatenga kamwana ka nkhosa kakakazi ka munthu wosauka uja ndi kukonzera munthu amene anabwera kwawoyo kuti adye.”+  Davide atamva zimenezi anamukwiyira kwambiri munthuyo,+ moti anauza Natani kuti: “Ndithu, pali Yehova Mulungu wamoyo,+ munthu wochita zimenezi ayenera kufa!+  Ndiponso ayenera kubweza+ nkhosa zinayi+ chifukwa cha kamwana ka nkhosa kakakazi kamene anatenga. Amenewa ndiwo malipiro a zimene wachitazi, pakuti analibe chisoni.”+  Pamenepo Natani anauza Davide kuti: “Munthu ameneyo ndiwe! Choncho Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndinakudzoza+ iwe kuti ukhale mfumu ya Isiraeli ndipo ndinakupulumutsa+ m’manja mwa Sauli.  Ine ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako+ ndi akazi a mbuye wako+ pachifuwa chako. Ndinakupatsanso nyumba ya Isiraeli ndi ya Yuda.+ Zinthu zimenezi zikanakhala kuti sizinakukwanire, ndinali wokonzeka kuziwonjezera ndiponso kukupatsa zinthu zina.+  N’chifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova mwa kuchita chinthu choipa+ pamaso pake? Uriya Mhiti unamupha ndi lupanga, ndipo mkazi wake unamutenga kukhala mkazi wako,+ pamene Uriyayo unamupha ndi lupanga+ la ana a Amoni. 10  Tsopano lupanga+ silidzachoka panyumba yako mpaka kalekale.+ Chimenechi n’chotsatira cha zimene unachita chifukwa chondinyoza mwa kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala mkazi wako.’ 11  Ndiyeno Yehova wanena kuti, ‘Taona, ndikukugwetsera tsoka m’nyumba yako yomwe.+ Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa mwamuna wina,+ ndipo iye adzagona ndi akazi ako anthu onse akuona.+ 12  Iweyo unachita zinthu zimenezi mobisa,+ koma ine ndidzachita zimenezi pamaso pa Isiraeli+ yense, masanasana.’”+ 13  Pamenepo Davide anauza+ Natani kuti: “Ndachimwira Yehova.”+ Ndiyeno Natani anauza Davide kuti: “Yehova wakukhululukira tchimo lako+ ndipo suufa.+ 14  Ngakhale zili choncho, chifukwa chakuti wanyoza+ Yehova mwa kuchita zimenezi, mwana wako wamwamuna amene wangobadwa kumeneyu adzafa ndithu.”+ 15  Kenako Natani anapita kunyumba kwake. Ndiyeno Yehova anakantha+ mwana amene mkazi wa Uriya anaberekera Davide, moti mwanayo anayamba kudwala. 16  Zitatero Davide anayamba kuchonderera Mulungu woona chifukwa cha mwanayo, ndipo anasiyiratu kudya.+ Kenako Davide analowa m’nyumba ndipo usiku umenewo anagona pansi.+ 17  Ndiyeno akulu a m’nyumba yake anabwera pamene iye anagonapo kuti amudzutse. Koma iye sanalole ndipo sanadye chakudya+ pamodzi nawo. 18  Ndiyeno pa tsiku la 7, mwanayo anamwalira. Zitatero, atumiki a Davide anaopa kumuuza kuti mwana uja wamwalira, ndipo anali kunena kuti: “Pamenetu mwanayu anali ndi moyo tinalankhula naye Davide, koma sanatimvere. Ndiye tingamuuze bwanji kuti, ‘Mwana uja wamwalira’? Tikamuuza adzachita chinachake choipa.” 19  Davide ataona kuti atumiki ake akunong’onezana, anazindikira kuti mwana uja wamwalira. Choncho anafunsa atumiki akewo kuti: “Kodi mwana uja wamwalira?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde wamwalira.” 20  Davide atamva zimenezi anadzuka pansi pamene anagonapo n’kukasamba ndi kudzola+ mafuta. Kenako anasintha zovala zake n’kukalowa m’nyumba+ ya Yehova ndipo anagwada n’kuweramira pansi.+ Atachoka kumeneko anakalowa m’nyumba yake ndi kupempha kuti amukonzere chakudya. Mwamsanga anam’bweretsera mkate ndipo anadya. 21  Pamenepo atumiki ake anam’funsa kuti: “Kodi zimene mwachitazi zikutanthauza chiyani? Pamene mwana anali moyo, munali kukana chakudya ndipo munali kulira chifukwa cha mwanayo. Koma mwana atangomwalira, mwadzuka ndi kuyamba kudya mkate.” 22  Iye anayankha kuti: “Pamene mwana anali ndi moyo ndinali kusala kudya+ ndipo ndinali kulira+ chifukwa mumtima mwanga ndinali kunena kuti, ‘Angadziwe ndani, mwina Yehova angandikomere mtima ndipo mwanayu angakhale ndi moyo?’+ 23  Koma tsopano popeza wamwalira, ndisale kudya chifukwa chiyani? Kodi ndingamuukitse?+ Inenso tsiku lina ndidzamwalira,+ koma iyeyo sangabwerere kwa ine.”+ 24  Ndiyeno Davide anayamba kutonthoza mkazi wake Bati-seba.+ Kuwonjezera apo, analowa kwa iye ndipo anagona naye. Patapita nthawi, anamuberekera mwana wamwamuna+ amene anamutcha dzina lakuti Solomo.*+ Yehova anam’konda mwana ameneyu.+ 25  Chotero Mulungu anatuma Natani+ mneneri kuti mwanayo akamutche dzina lakuti Yedediya,* chifukwa Yehova anam’konda.* 26  Ndiyeno Yowabu+ anapitiriza kumenyana ndi mzinda wa Raba+ wa ana a Amoni, ndipo analanda mzinda wachifumu. 27  Choncho Yowabu anatumiza mithenga kwa Davide kuti: “Ndamenyana ndi mzinda wa Raba.+ Ndalandanso mzinda wa madzi.* 28  Tsopano sonkhanitsani anthu otsalawo kuti muuthire nkhondo mzindawu ndi kuulanda, kuti ndisaulande ndine, kuopera kuti lingatchuke ndi dzina langa.” 29  Choncho Davide anasonkhanitsa anthu onse ndi kupita ku Raba kumene anathira nkhondo mzindawo ndi kuulanda. 30  Iye analanda chisoti chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu,*+ ndipo anthu anaveka Davide chisoticho. Golide wa chisoticho anali wolemera talente limodzi,* ndipo chisoticho chinalinso ndi miyala yamtengo wapatali. Zinthu zimene anafunkha+ mumzindawo zinali zochuluka kwambiri. 31  Davide anatulutsa anthu amene anali mumzindawo kuti akawagwiritse ntchito yocheka miyala, kusula zitsulo zakuthwa,+ nkhwangwa zachitsulo ndi kuumba njerwa. Zimenezi n’zimene anachitira mizinda yonse ya ana a Amoni. Pamapeto pake, Davide pamodzi ndi anthu onse anabwerera ku Yerusalemu.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, “Wamtendere.”
Dzinali limatanthauza, “Wokondedwa ndi Ya.”
Mawu ake enieni, “chifukwa cha Yehova.”
N’kutheka kuti mawu akuti “mzinda wa madzi” akutanthauza malo amene madzi a mumzindawo anali kuchokera.
N’kutheka kuti ameneyu anali fano la mulungu wa Aamoni. M’malemba ena amatchedwa “Moleki” kapena “Milikomu.”
Talente limodzi limeneli ndi makilogalamu 34.