2 Samueli 4:1-12

4  Mwana+ wa Sauli atamva kuti Abineri wafa ku Heburoni,+ manja ake analefuka+ ndipo Aisiraeli onse anasokonezeka.  Panali amuna awiri, atsogoleri a magulu a achifwamba+ a mwana wa Sauli. Mmodzi dzina lake anali Bana ndipo wina dzina lake anali Rekabu. Onsewa anali ana a Rimoni Mbeeroti+ wa fuko la Benjamini, pakuti dera la Beeroti nalonso linali kuonedwa ngati gawo la fuko la Benjamini.  Ndiyeno anthu a ku Beeroti anathawira ku Gitaimu,+ ndipo akhala kumeneko monga alendo mpaka lero.  Yonatani+ mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna wolumala mapazi.+ Mwanayu anali ndi zaka zisanu pamene kunabwera uthenga wa imfa ya Sauli ndi Yonatani kuchokera ku Yezereeli.+ Uthengawu utafika, mlezi wake anamunyamula ndi kuthawa naye. Pamene anali kuthawa mwamantha, mleziyo anagwetsa mwanayo ndipo analumala. Mwanayo dzina lake anali Mefiboseti.+  Rekabu ndi Bana, ana aamuna a Rimoni Mbeeroti, ananyamuka kupita kunyumba ya Isi-boseti+ masana kutatentha, ndipo anamupeza akugona.  Iwo analowa m’nyumbamo ngati anthu ofuna tirigu, kenako anakantha Isi-boseti pamimba.+ Atatero, Rekabu ndi m’bale wake Bana+ anathawa kuti asadziwike.  Iwo atalowa m’nyumbamo, anapeza Isi-boseti atagona pabedi m’chipinda chake, ndipo anamukantha ndi kumupha.+ Kenako anamudula mutu+ ndipo anautenga ndi kuyenda nawo usiku wonse mumsewu wopita ku Araba.  Kenako mutu wa Isi-boseti+ uja anafika nawo kwa Davide ku Heburoni ndi kuuza mfumuyo kuti: “Nawu mutu wa Isi-boseti mwana wa mdani wanu Sauli,+ amene anali kufunafuna moyo wanu.+ Lero Yehova wabwezera+ Sauli ndi mbadwa zake chifukwa cha inu mbuyanga mfumu.”  Koma Davide anayankha Rekabu ndi m’bale wake Bana, ana a Rimoni Mbeeroti kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo,+ amene anawombola+ moyo wanga+ m’masautso anga onse,+ 10  pamene munthu wina anandibweretsera uthenga+ wakuti, ‘Sauli wafa,’ ndipo iye anali kuganiza kuti wabweretsa uthenga wabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha+ ku Zikilaga m’malo momulipira monga mthenga. 11  Ndiye kuli bwanji pamene anthu oipa+ apha munthu wolungama pabedi m’nyumba yake? Kodi sindiyenera kufuna magazi ake m’manja mwanu+ ndi kukuchotsani padziko?”+ 12  Pamenepo Davide analamula anyamata ake ndipo anapha Rekabu ndi Bana+ ndipo anadula manja ndi mapazi awo. Kenako anawapachika+ pafupi ndi dziwe la ku Heburoni, koma anatenga mutu wa Isi-boseti ndi kuuika m’manda a Abineri ku Heburoni.+

Mawu a M'munsi