2 Samueli 11:1-27

11  Ndiyeno ku chiyambi kwa chaka,+ pa nthawi imene mafumu anali kupita kukamenya nkhondo,+ Davide anatumiza Yowabu, atumiki ake ndi Isiraeli yense kuti akawononge ana a Amoni+ ndi kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.  Ndiyeno tsiku lina madzulo, Davide anadzuka pabedi lake, n’kupita kukayendayenda padenga*+ la nyumba yachifumu. Ali pamenepo anaona+ mkazi akusamba, ndipo mkaziyo anali wooneka bwino kwambiri.+  Zitatero, Davide anatuma nthumwi kukafufuza za mkaziyo.+ Ndiyeno munthu wina ananena kuti: “Kodi ameneyu si Bati-seba+ mwana wa Eliyamu,*+ mkazi wa Uriya+ Mhiti?”+  Kenako Davide anatuma nthumwi kuti akamutenge.+ Choncho mkaziyo anabweradi kwa Davide+ ndipo Davide anagona naye+ pa nthawi imene mkaziyo anali kudziyeretsa ku chodetsa chake.+ Zitatero mkaziyo anabwerera kunyumba yake.  Tsopano mkaziyo anakhala ndi pakati. Choncho anatumiza uthenga kwa Davide wonena kuti: “Ndili ndi pakati.”  Pamenepo Davide anatumiza uthenga kwa Yowabu wonena kuti: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Choncho Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide.  Uriya atafika kwa Davide, Davideyo anayamba kumufunsa za umoyo wa Yowabu, za umoyo wa anthu ndi mmene nkhondo inali kuyendera.  Pamapeto pake, Davide anauza Uriya kuti: “Pita kunyumba kwako ukasambe mapazi ako.”+ Uriya anatuluka m’nyumba ya mfumu ndipo pambuyo pake mfumuyo inamutumizira mphatso.  Koma Uriya anagona pakhomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi atumiki ena a mbuye wake, moti sanapite kunyumba yake. 10  Choncho anthu anauza Davide kuti: “Uriya sanapite kunyumba kwake.” Atamva zimenezi, Davide anauza Uriya kuti: “Iweyo wayenda ulendo wautali, si choncho kodi? Bwanji sunapite kunyumba kwako?” 11  Pamenepo Uriya anayankha Davide kuti: “Likasa,+ Isiraeli ndi Yuda akukhala m’misasa, ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi atumiki anu mbuyanga+ ali mumsasa kuthengo. Ndiye ine ndikalowe m’nyumba yanga kukadya chakudya, kumwa ndi kugona ndi mkazi wanga?+ Ndithu, pali inu ndi moyo wanu,+ sindingachite zimenezo.” 12  Ndiyeno Davide anauza Uriya kuti: “Leronso usanyamuke ndipo mawa ndikulola kupita.” Choncho Uriya anakhalabe ku Yerusalemu tsiku limenelo ndiponso tsiku lotsatira. 13  Kuwonjezera apo, Davide anamuitana kuti adye ndi kumwa naye pamodzi, ndipo anamuledzeretsa.+ Ngakhale zinali choncho, madzulo Uriya anapita kwa atumiki a mbuye wake kukagona pabedi, ndipo sanapite kunyumba kwake. 14  Ndiyeno m’mawa mwake, Davide analembera kalata+ Yowabu n’kupatsira Uriya. 15  M’kalatamo analembamo kuti:+ “Muike Uriya kutsogolo kumene nkhondo yakula,+ ndipo inu mubwerere m’mbuyo kuti amukanthe ndipo afe ndithu.”+ 16  Pamene Yowabu anazungulira mzinda wa Raba, anaika Uriya pamalo amene anadziwa kuti akumana ndi amuna amphamvu.+ 17  Pamene amuna a mzindawo anatuluka kudzamenyana ndi Yowabu, ena mwa anthu, atumiki a Davide anakanthidwa ndi kugwa, ndipo Uriya Mhiti nayenso anafa.+ 18  Tsopano Yowabu anatumiza mthenga kuti akauze Davide zonse zimene zikuchitika kunkhondo. 19  Yowabu analamula mthengayo kuti: “Ukakangomaliza kufotokozera mfumu zonse zokhudza nkhondoyi, 20  ndiyeno mfumu n’kukwiya ndi kukufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mumamenya nkhondo moyandikira mzindawo kwambiri choncho? Kodi amuna inu simunali kudziwa kuti adzaponya mivi kuchokera pamwamba pa mpanda? 21  Ndani uja anapha Abimeleki+ mwana wa Yerubeseti?*+ Kodi si mkazi amene anaponya mwala wokhala pamwamba wa mphero+ ali pamwamba pa mpanda, ndipo Abimeleki anafera ku Tebezi+ komweko? N’chifukwa chiyani amuna inu munauyandikira kwambiri mpandawo?’ Pamenepo ukanene kuti, ‘Nayenso Uriya Mhiti, mtumiki wanu, wafa.’”+ 22  Choncho mthengayo anapita, ndipo atafika kwa Davide anamuuza zonse zimene Yowabu anamutuma. 23  Ndiyeno mthengayo anauza Davide kuti: “Amunawo anakula mphamvu kuposa ife, moti anatuluka kudzamenyana nafe kuthengo, koma tinayesetsa kuwapanikiza mpaka kuchipata cha mzinda. 24  Koma oponya mivi anapitirizabe kulasa atumiki anu kuchokera pamwamba pa mpanda,+ moti ena mwa atumiki a mfumu afa. Nayenso Uriya Mhiti, mtumiki wanu wafa.”+ 25  Pamenepo Davide anauza mthengayo kuti: “Ukamuuze Yowabu kuti, ‘Usavutike mtima chifukwa cha nkhani imeneyi, pakuti lupanga lingakanthe+ wina aliyense. Inuyo menyani nkhondo mwamphamvu ndi mzindawo ndipo muugonjetse.’+ Choncho, ukamulimbikitse Yowabu.” 26  Pamenepo mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake+ wafa, ndipo anayamba kumulira.+ 27  Nyengo yolira maliro+ itatha, nthawi yomweyo Davide anatumiza nthumwi kukatenga Bati-seba ndi kubwera naye kunyumba kwake, ndipo anakhala mkazi wake.+ Patapita nthawi, anamuberekera mwana wamwamuna. Koma zimene Davide anachitazi zinamuipira kwambiri Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “tsindwi.”
Pa 1Mb 3:5 akutchedwa “Amiyeli.”
Pa Owe 6:32; Owe 7:1; Owe 9:1, 16, 24, 28, akutchedwa “Yerubaala.”