2 Samueli 9:1-13

9  Ndiyeno Davide ananena kuti: “Kodi pali aliyense wotsala wa m’nyumba ya Sauli? Ndikufuna kumusonyeza kukoma mtima kosatha+ chifukwa cha Yonatani.”+  Tsopano nyumba ya Sauli inali ndi mtumiki, dzina lake Ziba.+ Choncho anamuitanira kwa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Ziba?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndine mtumiki wanu.”  Ndiyeno mfumu inati: “Kodi palibe aliyense wotsala m’nyumba ya Sauli? Ndikufuna kumusonyeza kukoma mtima kosatha kwa Mulungu.”+ Poyankha Ziba anauza mfumu kuti: “Alipo mwana wamwamuna wa Yonatani, wolumala mapazi.”+  Pamenepo mfumu inamufunsa kuti: “Ali kuti?” Ziba anayankha mfumu kuti: “Ali m’nyumba ya Makiri,+ mwana wamwamuna wa Amiyeli, ku Lo-debara.”+  Nthawi yomweyo Mfumu Davide anatumiza anthu kuti akamutenge kunyumba ya Makiri, mwana wa Amiyeli, ku Lo-debara.  Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, atalowa ndi kuonana ndi Davide, nthawi yomweyo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ Pamenepo Davide anati: “Mefiboseti!” Poyankha, iye anati: “Ndine pano mtumiki wanu.”  Ndiyeno Davide anamuuza kuti: “Usaope. Ndithu, ndikusonyeza kukoma mtima kosatha+ chifukwa cha Yonatani bambo ako.+ Ndikubwezera munda wonse+ wa Sauli agogo ako ndipo iweyo uzidya mkate patebulo langa nthawi zonse.”+  Mefiboseti atamva zimenezi anawerama mpaka nkhope yake pansi ndipo anati: “Kodi ine mtumiki wanu ndine ndani kuti mukumbukire galu wakufa+ ngati ine?”  Ndiyeno mfumu inaitana Ziba, mtumiki wa Sauli, ndi kumuuza kuti: “Chilichonse chimene chinali cha Sauli komanso chilichonse cha m’nyumba yake yonse, ine ndikupereka+ kwa mdzukulu wa mbuye wako. 10  Iweyo, ana ako aamuna ndi antchito ako, muzimulimira munda wake ndi kumukololera kuti anthu a m’nyumba ya mdzukulu wa mbuye wako azikhala ndi chakudya chimene azidya. Koma Mefiboseti, mdzukulu wa mbuye wako, azidya chakudya patebulo langa nthawi zonse.”+ Tsopano Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi antchito 20.+ 11  Pamenepo Ziba anayankha mfumu kuti: “Zonse zimene mbuyanga mfumu yanena kwa ine mtumiki wanu ndichita zomwezo, koma Mefiboseti+ akudya patebulo langa* ngati mmodzi wa ana a mfumu.” 12  Tsopano Mefiboseti anali ndi mwana wamng’ono wamwamuna dzina lake Mika,+ ndipo anthu onse okhala m’nyumba ya Ziba anali antchito a Mefiboseti. 13  Choncho Mefiboseti anali kukhala mu Yerusalemu pakuti anali kudya patebulo la mfumu nthawi zonse.+ Iye anali wolumala mapazi.+

Mawu a M'munsi

Pa mawu akuti “tebulo langa,” mipukutu ina imanena kuti “tebulo la Davide,” kapenanso “tebulo la mfumu.” Choncho ena amanena kuti mawu akuti “tebulo langa” ayenera kukhala “tebulo la Davide.” N’kuthekanso kuti Ziba anali kubwereza mawu amene Davide ananena.