2 Samueli 5:1-25

5  Patapita nthawi, mafuko onse a Isiraeli anapita kwa Davide+ ku Heburoni+ ndi kumuuza kuti: “Ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.+  Kuyambira kale+ pamene Sauli anali mfumu yathu, inuyo munali kutsogolera Isiraeli polowa ndi potuluka.+ Ndipo Yehova anakuuzani kuti, ‘Udzaweta+ anthu anga Aisiraeli ndipo udzakhala mtsogoleri+ wa Isiraeli.’”  Choncho akulu onse+ a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Mfumu Davide anachita nawo pangano+ ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli.+  Davide anali ndi zaka 30 pamene anakhala mfumu. Iye analamulira monga mfumu kwa zaka 40.+  Ku Heburoni analamulira monga mfumu ya Yuda zaka 7 ndi miyezi 6.+ Ku Yerusalemu+ analamulira monga mfumu ya Isiraeli yense ndiponso Yuda zaka 33.  Patapita nthawi, mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene anali kukhala kumeneko. Ayebusiwo anayamba kuuza Davide kuti: “Sulowa mumzinda uno, pakuti upitikitsidwa ndi anthu akhungu ndi olumala.”+ Mumtima mwawo iwo anali kunena kuti: “Davide sangalowe mumzinda uno.”  Ngakhale zinali choncho, Davide analanda Ziyoni, malo okhala mumpanda wolimba kwambiri,+ umene ndi Mzinda wa Davide.+  Choncho Davide pa tsiku limenelo anati: “Aliyense wofuna kukaukira Ayebusi+ adutse m’ngalande zamadzi+ ndi kukakumana ndi anthu olumala ndi akhungu, anthu amene ine Davide ndimadana nawo kwambiri!” N’chifukwa chake pali mawu onena kuti: “Wakhungu ndi wolumala asalowe m’nyumba.”  Davide anayamba kukhala m’malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, ndipo anawatcha Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati. 10  Chotero ulamuliro wa Davide unakulirakulira,+ ndipo Yehova Mulungu wa makamu+ anali naye.+ 11  Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo anatumiza amithenga+ kwa Davide. Anatumizanso mitengo ya mkungudza,+ anthu a ntchito zamatabwa ndi a ntchito za miyala yomangira khoma,* ndipo anayamba kumanga nyumba ya Davide.+ 12  Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike mu Isiraeli,+ komanso kuti wamukwezera+ ufumu wake chifukwa cha anthu ake Aisiraeli.+ 13  Pambuyo pake, Davide anatenganso adzakazi+ ndi akazi+ ena mu Yerusalemu atachoka ku Heburoni, moti anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14  Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo ndi awa: Samuwa,+ Sobabu,+ Natani,+ Solomo,+ 15  Ibara, Elisua,+ Nefegi,+ Yafiya,+ 16  Elisama,+ Eliyada ndi Elifeleti.+ 17  Tsopano Afilisiti anamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli.+ Choncho Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide. Davide atamva zimenezi, anakabisala kumalo ovuta kufikako.+ 18  Afilisitiwo anafika ndi kuyamba kuyendayenda m’chigwa cha Arefai.+ 19  Ndiyeno Davide anafunsira+ kwa Yehova kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwapereka m’manja mwanga?” Pamenepo Yehova anauza Davide kuti: “Pita, ndipereka ndithu Afilisitiwa m’manja mwako.”+ 20  Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu,+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero anati: “Yehova wayenda patsogolo panga ngati madzi a chigumula ndi kuwononga adani anga.”+ N’chifukwa chake malowo anawatcha Baala-perazimu.*+ 21  Pa nthawiyi, Afilisiti anasiya mafano awo+ kumeneko, choncho Davide ndi anthu ake anawatenga.+ 22  Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso+ ndi kuyamba kuyendayenda m’chigwa cha Arefai.+ 23  Pamenepo Davide anafunsira+ kwa Yehova ndipo anamuyankha kuti: “Ayi usapite. Koma uwazembere kumbuyo kwawo ndi kuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 24  Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka, pamenepo ukachitepo kanthu mwachangu,+ chifukwa pa nthawiyo Yehova adzakhala atatsogola kukapha gulu lankhondo la Afilisiti.”+ 25  Pamenepo Davide anachitadi momwemo, monga mmene Yehova anamulamulira,+ moti anapha+ Afilisiti kuchokera ku Geba*+ mpaka kukafika ku Gezeri.+

Mawu a M'munsi

M’Chiheberi, mawu akuti “Chimulu cha Dothi” ndi mil·lohʹ. Mwina chinali chinyumba chokhala ndi chitetezo champhamvu.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Dzinali limatanthauza, “Ambuye wa Zigumula.”
Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.
M’malo mwa “Geba,” pa 1Mb 14:16 pali dzina lakuti “Gibeoni.”