2 Samueli 24:1-25

24  Mkwiyo wa Yehova unayakiranso+ Isiraeli pamene winawake anaukira Isiraeli mwa kulimbikitsa Davide kuti: “Pita ukawerenge+ anthu a Isiraeli ndi Yuda.”  Choncho mfumu inauza Yowabu+ mkulu wa magulu ankhondo amene anali naye kuti: “Yendayenda m’mafuko onse a Isiraeli kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba.+ Ndipo amuna inu muwerenge anthu+ kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”+  Koma Yowabu anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu awonjezere anthu kuwirikiza nthawi 100 pa kuchuluka kwawo, maso anu inu mbuyanga mfumu akuona. Koma inu mbuyanga mfumu, n’chifukwa chiyani mukufuna kuchita zimenezi?”+  Pamapeto pake mawu a mfumu anaposa+ mawu a Yowabu ndi atsogoleri a magulu ankhondo. Choncho Yowabu ndi atsogoleri a magulu ankhondowo anachoka pamaso pa mfumu ndi kupita kukawerenga+ anthu a Isiraeli.  Kenako anawoloka Yorodano ndi kumanga msasa ku Aroweli+ kudzanja lamanja la mzinda umene uli pakati pa chigwa,* kuyang’ana kudziko la Agadi+ ndi ku Yazeri.+  Atachoka kumeneko anafika ku Giliyadi+ ndi kudziko la Tatimu-hodisi, ndipo anapitirira mpaka ku Dani-jaana ndi kuzungulira kukafika ku Sidoni.+  Kenako anafika kumzinda wa mpanda wolimba wa Turo+ ndiponso kumizinda yonse ya Ahivi+ ndi Akanani. Pamapeto pake anafika ku Beere-seba+ ku Negebu,+ m’dziko la Yuda.  Chotero anayendayenda m’dziko lonse ndipo patatha miyezi 9 ndi masiku 20 anafika ku Yerusalemu.  Tsopano Yowabu anapereka chiwerengero chonse+ cha anthu kwa mfumu. Aisiraeli analipo 800,000, amuna amphamvu ogwira lupanga, ndipo amuna a Yuda analipo 500,000.+ 10  Davide atawerengadi anthuwo anavutika mumtima mwake.+ Choncho Davide anauza Yehova kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimene ndachitazi. Tsopano Yehova, khululukani cholakwa cha ine mtumiki wanu+ chonde, pakuti ndachita chinthu chopusa kwambiri.”+ 11  Davide atadzuka m’mawa, mawu a Yehova anafika kwa mneneri Gadi,+ wamasomphenya wa Davide+ kuti: 12  “Pita, ukauze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndaika zilango zitatu pamaso pako.+ Sankha wekha chimodzi mwa zitatuzi chimene ukufuna kuti ndikuchitire.”’”+ 13  Pamenepo Gadi anapita kwa Davide ndi kumuuza kuti:+ “Kodi m’dziko lanu mubwere njala yaikulu zaka 7,+ kapena muzithawa adani anu akukuthamangitsani miyezi itatu,+ kapena kodi kugwe mliri wa masiku atatu m’dziko lanu?+ Ganizirani mofatsa zoti ndikayankhe kwa Amene wandituma.” 14  Atamva zimenezo, Davide anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisautsa kwambiri. Chonde, tilangidwe ndi Yehova,+ pakuti chifundo chake n’chochuluka,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+ 15  Pamenepo Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli kuyambira m’mawa mpaka nthawi yoikidwiratu, moti pa anthu onse kuyambira ku Dani mpaka ku Beere-seba+ panafa anthu 70,000.+ 16  Ndiyeno mngelo+ anali atatambasula dzanja lake kuloza ku Yerusalemu kuti awononge mzindawo. Pamenepo Yehova anamva chisoni+ chifukwa cha tsokalo, choncho anauza mngelo amene anali kupha anthuyo kuti: “Basi pakwanira! Tsopano tsitsa dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehova uja anali pafupi ndi malo opunthira mbewu a Arauna+ Myebusi.+ 17  Ndiyeno Davide atangoona mngelo amene anali kupha anthuyo anauza Yehova kuti: “Tsopano amene ndachimwa ndine, ndipo ine ndi amene ndachita cholakwa, nanga nkhosazi+ zalakwa chiyani? Dzanja lanu likhale pa ine+ chonde ndi panyumba ya bambo anga.” 18  Kenako Gadi anafika kwa Davide tsiku limenelo ndi kumuuza kuti: “Pita ukamangire Yehova guwa lansembe pamalo opunthira mbewu a Arauna Myebusi.”+ 19  Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu a Gadi, mogwirizananso ndi zimene Yehova analamula.+ 20  Arauna atasuzumira panja anaona mfumu ndi atumiki ake akubwera kwa iye. Nthawi yomweyo Arauna anatuluka ndi kugwada+ pamaso pa mfumu ndipo anawerama mpaka nkhope yake pansi.+ 21  Ndiyeno Arauna anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mwabwera kwa ine mtumiki wanu?” Poyankha Davide anati: “Ndabwera kuti undigulitse+ malo ako opunthira mbewu. Ndikufuna kumangira Yehova guwa lansembe pamenepo, kuti mliriwu+ uthe pakati pa anthuwa.” 22  Koma Arauna anauza Davide kuti: “Mbuyanga mfumu, tengani+ malowo ndipo mupereke chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino. Onani, ng’ombe iyi ikhale nsembe yopsereza ndipo chopunthira ndi zipangizo za ng’ombe zikhale nkhuni.+ 23  Ine Arauna ndikupereka chilichonse kwa inu mfumu.” Kenako Arauna anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu asonyeze kuti akukondwera nanu.”+ 24  Koma mfumu inauza Arauna kuti: “Iyayi, ineyo ndigula zimenezi.+ Ine sindipereka nsembe zopsereza za nyama kwa Yehova Mulungu wanga popanda kulipira.”+ Choncho Davide anagula+ malo opunthira mbewu ndi ng’ombe ndipo analipira ndalama zokwana masekeli 50 asiliva. 25  Zitatero, Davide anamangira Yehova guwa lansembe+ pamenepo ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Choncho Yehova anamva kuchonderera kwawo,+ moti mliriwo anauthetsa mu Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.