2 Samueli 7:1-29

7  Ndiyeno pamene mfumu inali kukhala m’nyumba yake,+ ndipo Yehova ataipatsa mpumulo kwa adani ake onse oizungulira,+  inauza Natani+ mneneri kuti: “Tsopano taona, ine ndikukhala m’nyumba ya mitengo ya mkungudza,+ pamene likasa la Mulungu woona likukhala m’chihema chansalu.”+  Pamenepo Natani anauza mfumu kuti: “Chitani chilichonse chimene chili mumtima mwanu,+ chifukwa Yehova ali nanu.”  Tsopano usiku umenewo, Yehova analankhula+ ndi Natani, kuti:  “Pita, ukauze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Kodi iwe ungandimangire nyumba yoti ine ndikhalemo?+  Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa ana a Isiraeli mu Iguputo kufikira lero,+ sindinakhalepo m’nyumba koma nthawi zonse ndinali kuyenda+ m’chihema chopatulika.+  Pa nthawi yonse imene ndinali kuyendayenda pakati pa ana a Isiraeli onse,+ kodi ndinalankhulapo mawu ndi limodzi mwa mafuko onse a Isiraeli,+ fuko limene ndinalilamula kutsogolera anthu anga Aisiraeli, kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu inu simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”’  Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa, kumene unali kusamalira nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri+ wa anthu anga Aisiraeli.  Ine ndidzakhala ndi iwe kulikonse kumene udzapite,+ ndipo ndidzawononga ndi kuchotsa adani ako onse pamaso pako.+ Ndidzakupangira dzina lotchuka,+ lofanana ndi dzina la anthu otchuka amene ali m’dziko. 10  Ndipo anthu anga Aisiraeli ndidzawasankhira malo+ ndi kuwakhazika+ pamalowo. Iwo adzakhaladi kumeneko ndipo sadzasokonezedwanso. Anthu osalungama sadzawasautsanso ngati mmene anachitira poyamba,+ 11  kuchokera tsiku limene ndinaika oweruza+ kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli. Ndidzakupatsa mpumulo kwa adani ako onse.+ “‘“Tsopano Yehova wakuuza kuti, Yehova adzakukhazikitsira banja lachifumu.+ 12  Masiku ako akadzakwana,+ ndipo ukadzagona pamodzi ndi makolo ako,+ pamenepo ndidzautsa mbewu yako yobwera pambuyo pako, imene idzatuluka m’chiuno mwako. Ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.+ 13  Iye ndi amene adzamangira dzina langa nyumba,+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+ 14  Ine ndidzakhala atate wake+ ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Akachita zoipa, ine ndidzam’dzudzula ndi ndodo+ ya anthu ndi zikoti za ana a Adamu. 15  Ndipo kukoma mtima kwanga kosatha sikudzachoka pa iye monga mmene ndinakuchotsera pa Sauli,+ amene ndinam’chotsa pamaso pako. 16  Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikika pamaso pako mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+ 17  Natani anauza Davide mawu onsewa ndiponso masomphenya onse amene anaona.+ 18  Pamenepo Mfumu Davide inabwera ndi kukhala pansi pamaso pa Yehova, ndipo inati: “Ndine yani ine,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa? Ndipo nyumba yanga n’chiyani kuti mundifikitse pamene ndili pano? 19  Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, kuwonjezeranso pamenepa, mwangondiuza kumene kuti nyumba ya mtumiki wanu idzakhazikika mpaka m’tsogolo kwambiri. Limenelitu ndi lamulo limene mwapereka kwa anthu,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+ 20  Ndiyeno ine Davide ndinganenenji kuwonjezera pa zimene inu mwanena, pamene ndinu amene mukundidziwa bwino ine mtumiki wanu,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa? 21  Inu mwachita zazikulu zonsezi monga mwa mawu anu,+ komanso mogwirizana ndi zofuna za mtima wanu,+ ndipo mwandidziwitsa ine mtumiki wanu.+ 22  N’chifukwa chake ndinudi wokwezeka,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Ngakhale kuti tamva za milungu ina yambirimbiri, palibe Mulungu wina+ koma inu nokha.+ 23  Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu munawawombola monga anthu anu+ ndi kudzipangira dzina,+ amene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha?+ Munapitikitsa mitundu ina ndi milungu yawo, chifukwa cha anthu anu amene munawawombola+ nokha kuchokera ku Iguputo. 24  Inutu munadzikhazikitsira anthu anu Aisiraeli+ kuti akhaledi anthu anu mpaka kalekale. Ndipo inu Yehova mwakhala Mulungu wawo.+ 25  “Tsopano inu Yehova Mulungu, chitani mpaka kalekale mawu amene mwalankhula okhudza mtumiki wanu ndi nyumba yake. Chitani mmene mwanenera.+ 26  Dzina lanu likwezeke mpaka kalekale.+ Anthu anene kuti, ‘Yehova wa makamu ndi Mulungu wa Isiraeli,’+ ndipo nyumba ya mtumiki wanu Davide ikhazikike pamaso panu.+ 27  Pakuti inu Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, mwaululira ine mtumiki wanu kuti, ‘Ndidzakumangira nyumba.’*+ N’chifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera kwa inu pemphero lino.+ 28  Tsopano inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndinu Mulungu woona. Kunena za mawu anu, akhale oona,+ pakuti mwandilonjeza ine mtumiki wanu zabwino zimenezi.+ 29  Choncho dalitsani+ nyumba ya mtumiki wanu kuti ikhazikike pamaso panu mpaka kalekale.+ Pakuti inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa mwalonjeza, ndipo madalitso anu akhale panyumba ya mtumiki wanu mpaka kalekale.”+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “nyumba” akutanthauza mzere wa mafumu.