Pitani ku nkhani yake

Banja

Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muzisangalala

Muzidalira Kwambiri Mulungu

Kudzifunsa mafunso awiri okha kungathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.

Kodi Mabanja Angatani Kuti Azikhala Osangalala?

Malangizo a m’Baibulo okhudza banja amathandiza kuti banja likhale losangalala chifukwa malangizowo amachokera kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi Woyambitsa ukwati.

Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Banja Losangalala

Kodi amuna, akazi, makolo komanso ana angatani kuti azisangalala m’banja?

Kuti Banja Liziyenda Bwino​—Kuchita Zinthu Mogwirizana

Kodi inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu mumangokhala ngati anthu okhalira limodzi basi?

Kodi Mungatani Kuti Mukhale Woleza Mtima?

Anthu awiri opanda ungwiro akakwatirana, amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Kuleza mtima n’kofunika kwambiri kuti banja likhale lolimba.

Kodi Mungasonyezane Bwanji Ulemu?

Anthu okwatirana ayenera kusonyezana ulemu nthawi zonse. Koma kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mumalemekeza mwamuna kapena mkazi wanu?

Kuti Mukhale Ndi Banja Losangalala: Muzisonyezana Chikondi

Kugwira ntchito, kupanikizika maganizo komanso zochitika za tsiku ndi tsiku zingachititse anthu okwatirana kuti azilephera kusonyezana chikondi. Kodi ndi zotheka kubwezeretsa chikondi m’banja mwanu?

Kodi Mungasonyeze Bwanji kuti Mumayamikira Zimene Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amachita?

Mwamuna ndi mkazi akamayesetsa kuona zabwino zimene mnzawo amachita, nthawi zambiri chikondi chawo chimakula. N’chiyani chingakuthandizeni kuti muziyamikira mwamuna kapena mkazi wanu?

Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumakonda Mwamuna Kapena Mkazi Wanu?

Kodi anthu okwatirana angasonyeze bwanji kuti amakondana? Werengani nkhaniyi ndi kupeza mfundo 4 zochokera m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni pa nkhaniyi.

Mungatani Kuti Mukwaniritse Lonjezo Lanu?

Kodi mumaona kuti lonjezo laukwati lili ngati goli loti simungathe kuchokamonso kapena mumaona kuti lili ngati nangula?

Muzikhala Okhulupirika

Kuti munthu akhale wokhulupirika m’banja ayenera kupewa chigololo komanso zinthu zina.

Mmene Mungakhalire Osangalala Ngati Mwakwatira Kapena Kukwatiwanso

Munthu akakwatira kapena kukwatiwanso amakumana ndi mavuto omwe mwina sankakumana nawo m’banja lake loyamba. Kodi mwanuna ndi mkazi angatani kuti azikhalabe osangalala?

Kodi Amuna Angatani Kuti Akazi Awo Azisangalala?

Amunanu, kodi mumangokwanitsa kupezera banja lanu ndalama, koma n’kulephera kuchitira mkazi wanu zina zofunika kwambiri?

Mungatani Kuti Muzikhala Wosangalala​—Chikondi

Kusonyezana chikondi kumathandiza kuti anthu azikhala mosangalala.

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Ukwati wa Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Mulungu amene anayambitsa ukwati amadziwa bwino zimene anthu okwatirana angachite kuti akhale ndi banja lolimba komanso losangalala.

Kodi Mulungu Amaloleza Mitala?

Kodi Mulungu ndi amene anayambitsa mitala? Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi.

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yokwatirana ndi Munthu wa Mtundu Wina?

Onani mfundo zina za m’Baibulo zimene zingathandize pa nkhani ya kusiyana mitundu ndiponso ukwati.

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Banja?

Mfundo za m’Baibulo zingathandize mwamuna ndi mkazi wake kuti apewe kapenanso kuthetsa mavuto am’banja lawo.

Kodi Ukwati Ndi Mgwirizano Woti Ukhoza Kungotha Chisawawa?

Werengani nkhaniyi kuti muone mmene kutsatira maudindo amene Mulungu anapereka kwa mwamuna ndi mkazi kungathandizire anthu apabanja kuti azisangalala.

Mavuto Komanso Njira Zowathetsera

Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani

M’malo molowa kuti zinthu zimene zimakukwiyitsani zisokoneze banja lanu, muziyesetsa kuona zinthuzo moyenera.

Zimene Mungachite Kuti Musamagwire Ntchito Pamene Simuli Kuntchito

Mfundo 5 zimene zingakuthandizeni kuti ntchito yanu isamasokoneze banja lanu.

Mfundo Zothandiza Anthu Omwe Achitiridwa Nkhanza Zosiyanasiyana

Dziwani kuti wolakwa si inuyo ndipo sikuti muli nokha.

N’zotheka Kuthetsa Nkhanza za M’banja

Kodi malangizo a m’Baibulo angathandize bwanji mwamuna ndi mkazi kuti asiye khalidwe la nkhanza?

Mungatani Kuti Muzigwirizana Ndi Apongozi Anu?

Mfundo zitatu zomwe zingakuthandizeni kuti nkhani zokhudza apongozi zisasokoneze banja lanu.

Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale

N’zotheka kulemekeza makolo anu popanda kusokoneza banja lanu.

Zimene Mungachite Ngati Mumaona Zinthu Mosiyana

Kodi anthu okwatirana angatani kuti athetse kusamvana popanda kukangana?

Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Amaonera Zolaula

Kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti ayambirenso kukhulupirirana komanso kuti azithandizana ngati wina ali ndi vuto loonera zolaula?

Kuonera Zolaula Kungasokoneze Banja Lanu

Nkhaniyi ili malangizo amene angakuthandizeni kuti musiye chizolowezi choonera zolaula komanso kukonza ubale wanu ndi mwamuna kapena mkazi wanu.

Zimene Mungachite Ngati Mumakonda Zosiyana

Kodi mumaona kuti ndinu wosiyana kwambiri ndi mwamuna kapena mkazi wanu?

Kodi Mungatani Kuti Musamasunge Chakukhosi?

Kodi kukhululuka kumatanthauza kuti mukuchepetsa vutolo kapena mukuona kuti silinachitike n’komwe?

Kuti Banja Liziyenda Bwino​—Kukhululukirana

Kodi mungatani kuti musamaganizire kwambiri zimene mwamuna kapena mkazi wanu amalakwitsa?

Ana Akakula N’kuchoka Pakhomo

Okwatirana ena amakumana ndi mavuto aakulu ana awo akakula n’kuchoka pakhomo. Kodi makolo ayenera kuchita chiyani kuti azolowerenso kukhala okha?

Mukakumana ndi Mavuto Amwadzidzidzi

Lolani kuti ena akuthandizeni.

Kodi Mungatani Kuti Musamachitirane Nsanje M’banja?

Banja silingayende bwino ngati mwamuna ndi mkazi wake amakayikirana. Ndiye kodi mungatani kuti musamachitirane nsanje pa zifukwa zosamveka?

Zimene Mungachite Ngati Mumacheza Kwambiri ndi Munthu Amene si Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

Mukamacheza kwambiri ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi wanu, kodi mumaona kuti palibe vuto lina lililonse? Ngati mumaona choncho, werengani nkhaniyi kuti muone mfundo za m’Baibulo zosonyeza kuti maganizo amenewo ndi oopsa.

Kupatukana Komanso Kuthetsa Banja

Mmene Kutha Kwa Banja Kumakhudzira Ana

Ngakhale kuti anthu ena amaganiza kuti kuthetsa banja kungathandize ana, kafukufuku akusonyeza kuti zimenezi zimabweretsa mavuto ambiri kwa anawo.

Ngati Banja Lanu Silikuyenda Bwino

Kodi simukondananso ndi mwamuna kapena mkazi wanu ndipo mumangomuona ngati munthu wokhala naye nyumba imodzi basi? Mfundo 5 zimene zingathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.

Kodi Pangakhale Chifukwa Chokhalira ndi Moyo Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Akakhala Wosakhulupirika?

Anthu ambiri amene mwamuna kapena mkazi wawo anachita zosakhulupirika anaona kuti Baibulo linawathandiza kupirira.

Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Chigololo

Kodi ukwati uyenera kutha wina akachita chigololo?

Kodi Baibulo Limaloleza Kuthetsa Ukwati?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene Mulungu amaloleza komanso zimene amadana nazo.

Zimene Mungachite Ngati Banja Latha

Anthu ambiri amene amathetsa banja amaona kuti zinthu siziyendabe bwino ngati mmene amaganizira. Mfundo za m’Baibulo zikhoza kukuthandizani kuti zinthu ziziyendabe bwino ngakhala banja lanu latha.

Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani Yothetsa Banja?

Kodi a Mboni za Yehova amathandiza mabanja amene akukumana ndi mavuto? Kodi akulu ayenera kuvomereza ngati wa Mboni akufuna kuthetsa banja?