Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Ukwati wa Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Ukwati wa Amuna Kapena Akazi Okhaokha?

Yankho la m’Baibulo

 Mlengi wathu anapereka malamulo okhudza ukwati kale kwambiri, maboma a anthu asanayambe n’komwe kuika malamulo okhudza ukwati. Buku loyambirira m’Baibulo limatiuza kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Malinga ndi buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo, mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “mkazi” palembali, “amatanthauza munthu yemwe si mwamuna.” (Vine’s Expository Dictionary of Biblical Words) Yesu nayenso ananena kuti anthu okwatirana ayenera kukhala “mwamuna ndi mkazi.”—Mateyu 19:4.

 Choncho, cholinga cha Mulungu chinali chakuti anthu okwatiranawo azikhala mwamuna ndi mkazi ndipo banja lisamathe. Amuna ndi akazi analengedwa moyenererana kuti azitha kukwatirana n’kumathandizana m’njira zosiyanasiyana, ndiponso kumasangalala ndi kugonana komanso kumabereka ana.