Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 1

Muzidalira Kwambiri Mulungu

Muzidalira Kwambiri Mulungu

“Amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi.”—Mateyu 19:4

Yehova * Mulungu ndi amene anayambitsa ukwati. Baibulo limanena kuti iye anapanga mkazi woyamba n’kumupereka kwa mwamuna. Zitatero, Adamu anasangalala kwambiri n’kunena kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Genesis 2:22, 23) Yehova amafunabe kuti anthu okwatirana azisangalala.

Mukangolowa m’banja mungaganize kuti chilichonse chiziyenda bwinobwino. Koma zoona zake n’zakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi amene amakondana kwambiri amakumana ndi mavuto. (1 Akorinto 7:28) M’kabukuka muli mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize banja lanu kukhala losangalala mukamazitsatira.—Salimo 19:8-11.

1 MUZIKWANIRITSA UDINDO UMENE YEHOVA ANAKUPATSANI

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Mwamuna ndi mutu wa banja.—Aefeso 5:23.

Ngati ndinu mwamuna, Yehova amafuna kuti muzisamalira mkazi wanu mwachikondi. (1 Petulo 3:7) Yehova anamupanga monga mnzanu wokuyenererani ndipo amafuna kuti muzichita naye zinthu mwaulemu ndiponso mwachikondi. (Genesis 2:18) Muyenera kukonda mkazi wanu kwambiri n’kumaika zofuna zake patsogolo osati zanu.—Aefeso 5:25-29.

Ngati ndinu mkazi, Yehova amafuna kuti muzilemekeza kwambiri mwamuna wanu ndiponso kumuthandiza kuti azikwaniritsa udindo wake. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:33) Muzithandiza kuti zimene wasankha zitheke komanso muzigwirizana naye ndi mtima wonse. (Akolose 3:18) Mukamachita zimenezi mudzakhala wokongola kwambiri kwa mwamuna wanuyo komanso kwa Yehova.—1 Petulo 3:1-6.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muyenera kufunsa mwamuna kapena mkazi wanu zimene muyenera kusintha kuti mukhale ndi banja labwino. Muzimvetsera akamakuuzani maganizo ake ndipo muziyesetsa kusintha

  • Muzileza mtima chifukwa zimatenga nthawi kuti muyambe kuchita zinthu zimene zingasangalatse mnzanuyo

2 MUZIGANIZIRA KWAMBIRI MAGANIZO A MNZANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Muziganizira zofuna za mwamuna kapena mkazi wanu. (Afilipi 2:3, 4) Muziona kuti mnzanuyo ndi wamtengo wapatali kwambiri ndipo muzikumbukira kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azikhala ‘odekha kwa onse.’ (2 Timoteyo 2:24) Muzisankha bwino mawu polankhula chifukwa ‘mawu a munthu wolankhula mosaganiza amalasa ngati lupanga koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.’ (Miyambo 12:18) Mzimu wa Yehova ungakuthandizeni kuti muzilankhula mokoma mtima komanso mwachikondi.—Agalatiya 5:22, 23; Akolose 4:6.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Musanayambe kukambirana nkhani yofunika kwambiri muzipemphera kuti musapse mtima komanso musaumirire maganizo anu

  • Muziganizira kwambiri zimene munganene komanso mmene munganenere zinthuzo

3 MUZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Anthu akakwatirana amakhala “thupi limodzi.” (Mateyu 19:5) Komabe amakhala anthu awiri oganiza mosiyana. Choncho muyenera kuyesetsa kuganiza ndiponso kuchita zinthu mogwirizana. (Afilipi 2:2) Kukhala ogwirizana posankha zochita n’kofunika kwambiri. Baibulo limati: “Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana.” (Miyambo 20:18) Muzitsatira mfundo za m’Baibulo mukamasankha limodzi zochita.—Miyambo 8:32, 33.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muziuza mwamuna kapena mkazi wanu maganizo anu komanso zakukhosi kwanu

  • Muzikambirana ndi mnzanuyo musanavomere kuchita zinazake

^ ndime 4 Yehova ndi dzina la Mulungu limene limapezeka m’Baibulo.