Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 6

Zimene Mungachite Mwana Akabadwa

Zimene Mungachite Mwana Akabadwa

“Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.”—Salimo 127:3

Anthu akakhala ndi mwana amasangalala kwambiri koma akhoza kupanikizikanso. Makolo ena angadabwe kuona kuti akufunika kuchita zambiri posamalira mwana. Nthawi zina zingavute kuti agwirizane m’banja chifukwa chakuti akupanikizika mwinanso sakugona mokwanira. Choncho mwamuna ndi mkazi wake ayenera kusintha zina ndi zina kuti asamalire bwino mwana popanda kusokoneza ubwenzi wawo. Kodi malangizo a m’Baibulo angakuthandizeni bwanji kuchita zimenezi?

1 MUZIDZIWA ZIMENE ZINGASINTHE

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ‘Chikondi n’choleza mtima, n’chokoma mtima, sichisamala zofuna zake zokha komanso sichikwiya.’ (1 Akorinto 13:4, 5) Mwachibadwa, maganizo onse a mayi amakhala pa mwana. Koma mayi ayeneranso kusamalira zofuna za mwamuna wake kuti mwamunayo asamamve ngati wayamba kuiwalidwa. Ayenera kuthandiza mwamuna wake moleza mtima komanso mokoma mtima kuti nayenso azithandiza posamalira mwanayo ndiponso azidzimva kuti ndi wofunika.

“Inunso amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino.” (1 Petulo 3:7) Muzidziwa kuti mkazi wanu ayenera kuchita zambiri posamalira mwana. Iye ali ndi udindo watsopano ndipo akhoza kupanikizika, kutopa ngakhalenso kuvutika maganizo. Nthawi zina angakukwiyireni koma muziupeza mtima n’kumakumbukira kuti “munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.” (Miyambo 16:32) Muzingomumvetsa n’kumuthandiza.—Miyambo 14:29.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Abambo: Muzithandiza mkazi wanu kusamalira mwana ngakhale usiku. Muzisiya zinthu zina kuti mukhale ndi nthawi yokhala ndi mkazi wanu ndiponso mwana wanu

  • Amayi: Mwamuna wanu akafuna kukuthandizani kusamalira mwana, muyenera kuvomera. Ngati sakumusamalira bwino, muyenera kumuthandiza mokoma mtima osati kumutsutsa

2 MUZILIMBITSA UBWENZI WANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Mwana akabadwa, muzikumbukirabe kuti inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu ndinu “thupi limodzi.” Choncho muziyesetsa kwambiri kulimbitsa ubwenzi wanu.

Akazinu, muziyamikira zimene amuna anu amachita pokuthandizani. Mawu anu oyamikira angalimbikitse kwambiri mwamuna wanu. (Miyambo 12:18) Nanunso amuna muziuza akazi anu kuti mumawakonda komanso kuwaona kuti ndi amtengo wapatali. Muziwayamikiranso chifukwa cha zimene amachita posamalira banja.—Miyambo 31:10, 28.

“Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:24) Nthawi zonse muziyesetsa kuchita zinthu zimene zingathandize mwamuna kapena mkazi wanu. Muzipeza nthawi yolankhulana, kuyamikirana komanso muzimvetsera wina akamalankhula. Musamangoganizira zofuna zanu zokha pa nkhani yogonana. Muziganiziranso zofuna za mnzanuyo. Paja Baibulo limati: “Musamanane, kupatulapo ngati mwagwirizana kuimitsa kaye mangawawo.” (1 Akorinto 7:3-5) Choncho muzikambirana momasuka nkhani imeneyi. Ubwenzi wanu ukhoza kulimba kwambiri ngati mumaleza mtima komanso kumvetsetsana.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzipeza nthawi yokhala awiriwiri n’kumacheza

  • Muzichita tinthu ting’onoting’ono tosonyeza kuti mumakonda mnzanuyo. Mwachitsanzo mukhoza kumutumizira meseji kapena kumupatsa kamphatso kenakake

3 MUZIPHUNZITSA MWANA WANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba oyera amene angathe kukupatsa nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke.” (2 Timoteyo 3:15) Muzikonzeratu njira zophunzitsira mwana wanu. Dziwani kuti mwana amatha kuphunzira zambiri ngakhale ali m’mimba. Akhoza kuzindikira mawu anu ndipo ngati mwasangalala nayenso amasangalala komanso mukakhumudwa naye amakhumudwa. Muzimuwerengera tinkhani kuyambira ali wakhanda. Ngakhale sangazindikire zimene mukuwerengazo, zingamuthandize kuti akadzakula azidzakonda kuwerenga.

Musaganize kuti mwana wanuyo ndi wamng’ono kwambiri moti simungamuuze za Mulungu. Ndi bwino kuti azikumvani mukupemphera kwa Yehova. (Deuteronomo 11:19) Ngakhale pamene mukusewera naye, muzitchulapo zinthu zimene Mulungu analenga. (Salimo 78:3, 4) Mwanayo akamakula adzazindikira kuti mumakonda kwambiri Yehova ndipo nayenso adzayamba kumukonda.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzipempha Mulungu kuti akupatseni nzeru kuti muziphunzitsa bwino mwana wanu

  • Muzitchula mobwerezabwereza mawu kapena mfundo zofunika kuti mwanayo ayambe kuzidziwa mwamsanga