Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 9

Muzilambira Yehova Mogwirizana

Muzilambira Yehova Mogwirizana

‘Lambirani amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.’—Chivumbulutso 14:7

M’kabukuka taona kuti Baibulo lili ndi mfundo zambiri zimene zingathandize banja lanu. Yehova amafuna kuti mukhale osangalala. Iye amalonjeza kuti mukamaika zofuna zake pamalo oyamba, “zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Amafunitsitsa mutakhala naye pa ubwenzi wabwino. Choncho muziyesetsa kulimbitsa ubwenziwu. Uwutu ndi mwayi waukulu kwambiri.—Mateyu 22:37, 38.

1 MUZILIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Yehova anati: “Ndidzakhala atate wanu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi.” (2 Akorinto 6:18) Mulungu amafuna kuti mukhale mnzake wapamtima. Pemphero lingakuthandizeni kuchita zimenezi. Yehova amatiuza kuti ‘tizipemphera mosalekeza.’ (1 Atesalonika 5:17) Iye amafunitsitsa kumva zakukhosi kwanu. (Afilipi 4:6) Mukamapemphera limodzi, banja lanu lidzaona kuti Mulungu ndi mnzanu weniweni.

Koma sikuti muzingolankhula ndi Mulungu. Muyeneranso kumvetsera akamakulankhulani. Mungachite zimenezi pophunzira Mawu ake ndiponso mabuku ofotokoza Baibulo. (Salimo 1:1, 2) Muziganiziranso kwambiri zimene mwaphunzira. (Salimo 77:11, 12) Kuti mumvetsere Mulungu muyeneranso kufika pa misonkhano yachikhristu nthawi zonse.—Salimo 122:1-4.

Kuuza anthu ena za Yehova kungakuthandizeninso kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu. Choncho muzigwira ntchitoyi mwakhama.—Mateyu 28:19, 20.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzikhala ndi nthawi yowerenga Baibulo ndiponso yopemphera tsiku lililonse

  • Muziona kuti zinthu zokhudza kulambira n’zofunika kuposa zosangalatsa

2 KULAMBIRA KWA PABANJA N’KOFUNIKA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Banja lanu liyenera kukhala ndi pulogalamu yolambira Yehova limodzi ndipo muziyesetsa kuti musamaphonye. (Genesis 18:19) Koma si zokhazi. Muyeneranso kuganizira za Mulungu nthawi zonse. Muzithandiza banja lanu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu polankhula za iye ‘mukakhala pansi m’nyumba mwanu, poyenda pamsewu, pogona ndi podzuka.’ (Deuteronomo 6:6, 7) Tsanzirani Yoswa amene ananena kuti: “Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.”—Yoswa 24:15.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Pokonza pulogalamu yophunzitsa banja lanu, muziganizira zimene zingathandize aliyense