Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala

Mukhoza kukhala ndi banja losangalala mukamatsatira mfundo za m’Baibulo.

Mawu Oyamba

Banja lanu likhoza kukhala losangalala ngati mutatsatira malangizo a m’Baibulo omwe ali m’kabuku kano.

MUTU 1

Muzidalira Kwambiri Mulungu

Kudzifunsa mafunso awiri okha kungathandize kuti banja lanu liziyenda bwino.

MUTU 2

Muzikhala Okhulupirika

Kuti munthu akhale wokhulupirika m’banja ayenera kupewa chigololo komanso zinthu zina.

MUTU 3

Zimene Mungachite Pothetsa Mavuto

Zimene mumachita pothetsa mavuto zingachititse kuti banja lanu likhale lolimba komanso losangalala kapena ayi.

MUTU 4

Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama

Kodi kukhulupirirana ndiponso kukambirana momasuka n’zothandiza bwanji?

MUTU 5

Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale

N’zotheka kulemekeza makolo anu popanda kusokoneza banja lanu.

MUTU 6

Zimene Mungachite Mwana Akabadwa

Kodi kulera mwana kungathandize banja lanu kukhala lolimba?

MUTU 7

Zimene Mungachite Pophunzitsa Mwana Wanu

Muyenera kuthandiza ana kumvetsa malamulo anu komanso zifukwa zimene mumawalangira.

MUTU 8

Mukakumana ndi Mavuto Amwadzidzidzi

Lolani kuti ena akuthandizeni.

MUTU 9

Muzilambira Yehova Mogwirizana

Kodi mungatani kuti muzisangalala pochita kulambira kwa pabanja?