Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Lingandithandize kuti Ndikhale ndi Banja Losangalala?

Kodi Baibulo Lingandithandize kuti Ndikhale ndi Banja Losangalala?

Yankho la m’Baibulo

 Inde lingakuthandizeni. Malangizo amene ali m’munsiwa ndi ena mwa malangizo ochokera m’Baibulo omwe athandiza anthu mamiliyoni ambiri kuti akhale ndi banja losangalala.

  1.   Lembetsani ukwati wanu kuboma. Anthu akamalembetsa ukwati wawo kuboma amalonjeza mwalamulo kuti adzakhala limodzi kwa moyo wonse ndipo zimenezi zimathandiza kuti akhale ndi banja losangalala.—Mateyu 19:4-6.

  2.   Muzikondana komanso muzilemekezana. Muzichitira zinthu mwamuna kapena mkazi wanu zimene inuyo mungakonde mutamachitiridwa.—Mateyu 7:12; Aefeso 5:25, 33.

  3.   Musamalankhule mokhadzula. Muziyesetsa kulankhula mwachifundo ngakhale mwamuna kapena mkazi wanu atanena kapena kuchita zinthu zimene sizinakusangalatseni. (Aefeso 4:31, 32) Palemba la Miyambo 15:1, Baibulo limanena kuti: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”

  4.   Mukhale wokhulupirika. Musamasonyeze munthu wina chikondi chimene mumayenera kusonyeza kwa mkazi kapena mwamuna wanu basi. (Mateyu 5:28) Baibulo limanena kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa.”—Aheberi 13:4.

  5.   Muziphunzitsa ana anu mwachikondi. Muzipewa kuchita zinthu molekerera ana anu komanso musamawachitire nkhanza.—Miyambo 29:15; Akolose 3:21.