Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Amuna Angatani Kuti Akazi Awo Azisangalala?

Kodi Amuna Angatani Kuti Akazi Awo Azisangalala?

KODI ndi zinthu ziti zomwe mwamuna ayenera kuchitira mkazi wake? Anthu ambiri anakula akukhulupirira kuti udindo wa mwamuna ndi kupeza ndalama zoti banja lake lizigwiritsa ntchito. Komabe, akazi ena amene amuna awo amachita zimenezi, amaona kuti akusoweka kenakake ndipo amakhala osasangalala. Mwachitsanzo, mayi wina wa ku Spain, dzina lake Rosa, anati: “Mwamuna wanga akakhala ndi anthu ena amaoneka kuti ndi munthu wabwino, koma akangofika kunyumba amasinthiratu.” Mayi winanso wa ku Nigeria, dzina lake Joy, anati: “Ine ndi mwamuna wanga tikakhala kuti sitinagwirizane pa nkhani inayake, ankandiuza kuti, ‘Usaiwale kuti ndine mwamuna wako. Uyenera kuchita chilichonse chimene ndanena.’”

Kodi mwamuna angatani kuti azichita zinthu zosonyeza kuti amaganizira mkazi wake komanso kumukonda? Nanga angatani kuti mkazi wake azisangalala?—Rute 1:9.

KODI MWAMUNA ALI NDI UDINDO WOTANI?

Mulungu saona kuti mkazi ndi wotsika poyerekeza ndi mwamuna. Komabe, mwamuna ndi mkazi sali ndi udindo wofanana m’banja. Mwachitsanzo lemba la Aroma 7:2 limanena kuti mkazi wokwatiwa amakhala “womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo.” Mofanana ndi mmene zilili kuti makampani ambiri amasankha munthu woti aziyang’anira kampaniyo, Mulungu anasankha mwamuna kuti akhale mutu wa banja. (1 Akorinto 11:3) Choncho, mwamuna ayenera kutsogolera banja lake.

Ndiye kodi mwamuna angatani kuti akwaniritse udindo wake? Baibulo limalangiza amuna kuti: “Pitirizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondera mpingo.” (Aefeso 5:25) Ngakhale kuti Yesu sanakwatire, chitsanzo chake chingakuthandizeni kukhala mwamuna wabwino. Tiyeni tione.

YESU NDI CHITSANZO CHABWINO KWA AMUNA

Ankalimbikitsa anthu komanso kuwathandiza. Yesu anauza anthu omwe anali ndi mavuto osiyanasiyana kuti: “Bwerani kwa ine, . . . ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Mateyu 11:28, 29) Yesu ankathandiza anthu oterewa ndipo ankawauza zimene angachite kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu azimasuka naye.

Kodi amuna angamutsanzire bwanji? Muzithandiza mkazi wanu ntchito zapakhomo. Akazi ena amapanikizika kwambiri ndi ntchito zapakhomo. Mwachitsanzo, Rosa anati: “Ndinkangokhala ngati wantchito wa mwamuna wanga.” Koma mosiyana ndi mwamuna wa Rosa, Kweku amathandiza mkazi wake ntchito zapakhomo ndipo banja lawo ndi losangalala. Iye anati: “Nthawi zambiri ndimafunsa mkazi wanga kuti, ‘Ndikuthandize chiyani?’ Chifukwa choti ndimamukonda kwambiri, sindidikira kuti achite kundipempha.”

Anali woganizira ena komanso wachifundo. M’nthawi ya Yesu, panali mayi wina yemwe ankadwala matenda oopsa kwa zaka 12. Mayiyu atamva kuti Yesu ali ndi mphamvu zochiritsa, anayamba kuganiza kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” Choncho, anafika pamene panali Yesu n’kugwira malaya ake, ndipo nthawi yomweyo anachiradi. Anthu ena anaona kuti mayiyu sanachite bwino. Koma Yesu anazindikira kuti wachita zimenezi chifukwa chothedwa nzeru. * Mokoma mtima anamuuza kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa, . . . matenda ako aakuluwo atheretu.” Yesu ankamumvera chisoni mayiyu chifukwa cha matenda ake, choncho sanamuchititse manyazi kapena kumudzudzula. Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anali wachifundo komanso woganizira ena.—Maliko 5:25-34.

Kodi amuna angamutsanzire bwanji? Mkazi wanu akamadwala muzileza mtima komanso muzichita zinthu zosonyeza kumuganizira. Muziyesetsa kumumvetsa ndipo musamapse mtima akachita zinazake. Mwachitsanzo, Ricardo anati: “Ndikaona kuti mkazi wanga sakuchedwa kukhumudwa, ndimayesetsa kuti ndisalankhule zomukhumudwitsa.”

Ankalankhula momasuka ndi ophunzira ake. Yesu ankakonda kucheza ndi anzake n’kumawauza nkhani zosiyanasiyana. Iye anati: “Zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.” (Yohane 15:15) N’zoona kuti nthawi zina Yesu ankafuna kukhala payekha kuti apemphere. Koma nthawi zambiri ankakonda kukhala ndi ophunzira ake ndipo ankawauza mmene akumvera. Mwachitsanzo, usiku woti aphedwa mawa lake ngati chigawenga, sanawabisire mmene ankamvera. Anawauza kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni.” (Mateyu 26:38) Ophunzira ake akamukhumudwitsa, sankasiya kuwalankhula.—Mateyu 26:40, 41.

Muzitsanzira Yesu kuti mukhale mwamuna komanso bambo wabwino

Kodi amuna angamutsanzire bwanji? Muzimasuka kufotokozera mkazi wanu zimene mukuganiza komanso mmene mukumvera. Akazi ena amadandaula kuti amuna awo amacheza momasuka ndi anthu ena, koma akafika panyumba amangokhala phee. Komatu akazi amasangalala kwambiri amuna awo akamalankhula nawo momasuka. Mwachitsanzo mayi wina, dzina lake Ana, anati: “Mwamuna wanga akamandiuza maganizo ake komanso mmene akumvera, ndimaona kuti amandikonda ndipo nanenso ndimayamba kumukonda kwambiri.”

Mkazi wanu akakukhumudwitsani, si bwino kusiya kumulankhula n’cholinga choti akhaule. Mayi wina anati: “Mwamuna wanga akakhumudwa, ankatha masiku ambiri osandilankhula. Ankachita zimenezi n’cholinga chondichititsa manyazi komanso pofuna kuti ndizidziimba mlandu.” Koma Edwin amachita zosiyana ndi zimenezi chifukwa amatsanzira Yesu. Iye anati: “Mkazi wanga akandikhumudwitsa, ndimadikira kaye kuti mtima wanga uphwe. Kenako ndimasankha nthawi yabwino yoti tikambirane nkhaniyo.”

Joy yemwe tamutchula koyambirira uja, anaona kuti mwamuna wake atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni, anasintha kwambiri. Joy anati: “Panopa akuyesetsa kukhala mwamuna wabwino komanso kutengera chitsanzo cha Yesu.” Mabanja ambiri ayamba kuyenda bwino chifukwa chophunzira Baibulo. Nanunso mukhoza kukhala ndi banja losangalala ngati mutamaphunzira Baibulo ndi kutsatira zimene mukuphunzirazo. Tikukulimbikitsani kuti mulankhule ndi a Mboni za Yehova kuti ayambe kuphunzira nanu Baibulo kwaulere.

^ ndime 10 Chilamulo cha Mose chinkanena kuti mayi akamadwala matendawa azikhala wodetsedwa. Aliyense yemwe wamukhudza ankakhalanso wodetsedwa.—Levitiko 15:19, 25.