Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 11

Kodi Timapindula Bwanji ndi Mfundo za M’Baibulo?

Kodi Timapindula Bwanji ndi Mfundo za M’Baibulo?

1. N’chifukwa chiyani timafunikira malangizo?

Kodi mfundo za m’Baibulo zingatithandize bwanji kupewa ngozi?—SALIMO 36:9.

Mlengi wathu ndi wanzeru kwambiri kuposa ifeyo. Popeza kuti iye ndi Atate wachikondi, amatisamalira. Komanso sanatilenge kuti tizidzilamulira tokha. (Yeremiya 10:23) Mofanana ndi mwana wamng’ono yemwe amadalira makolo ake kuti azimuuza zochita, tonsefe timafunika kutsogoleredwa ndi Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Choncho mfundo za m’Baibulo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.​—Werengani 2 Timoteyo 3:16.

Malamulo komanso mfundo za Yehova zimatithandiza kwambiri. Zimatiphunzitsa zimene tiyenera kuchita kuti tizikhala osangalala komanso zimene tingachite kuti tidzapeze madalitso osatha m’tsogolo. Choncho popeza Mulungu ndi amene anatilenga tiyenera kumumvera nthawi zonse.​—Werengani Salimo 19:7, 11; Chivumbulutso 4:11.

2. Kodi mfundo za m’Baibulo n’zosiyana bwanji ndi malamulo?

Nthawi zambiri, malamulo amagwira ntchito pa nthawi inayake kapena pa zochitika zinazake. (Deuteronomo 22:8) Mfundo za m’Baibulo ndi mfundo za choonadi zofunika kwambiri zimene sizisintha. Ndipotu malamulo ambiri a Mulungu amachokera pa mfundo za m’Baibulo. Timafunika kugwiritsa ntchito luso lathu la kuganiza kuti timvetse bwino mfundo zimenezi ndi kuzigwiritsa ntchito pa moyo wathu. (Miyambo 2:10-12) Mwachitsanzo, m’Baibulo timapezamo mfundo yoti moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Kuganizira mfundo imeneyi kungatithandize kuti tizichita zinthu zotithandiza kupewa ngozi tikakhala kuntchito, kunyumba kapena m’galimoto.​—Werengani Machitidwe 17:28.

3. Kodi ndi mfundo ziwiri ziti za m’Baibulo zomwe ndi zofunika kwambiri?

Yesu anatchula malamulo awiri a Mulungu ndipo m’malamulo amenewa timapezamo mfundo zofunika kwambiri. Lamulo loyamba limasonyeza cholinga chachikulu pa moyo wa munthu, chomwe ndi kudziwa Mulungu ndi kumutumikira mokhulupirika. Tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo yoyamba imeneyi nthawi zonse tikafuna kusankha zochita pa moyo wathu. (Miyambo 3:6) Aliyense amene amagwiritsa ntchito mfundo imeneyi amakhala pa ubwenzi ndi Mulungu, amakhala wosangalala komanso adzapeza moyo wosatha.​—Werengani Mateyu 22:36-38.

Lamulo lachiwiri lilinso ndi mfundo zothandiza kuti tizitha kukhala bwino ndi anzathu. (1 Akorinto 13:4-7) Munthu angasonyeze kuti akugwiritsira ntchito mfundo imeneyi potsanzira mmene Mulungu amachitira zinthu ndi anthu.​—Werengani Mateyu 7:12; 22:39, 40.

4. Kodi timapindula bwanji ndi mfundo za m’Baibulo?

Mfundo za m’Baibulo zimathandiza kuti mabanja akhale ogwirizana komanso kuti anthu m’banjamo azikondana. (Akolose 3:12-14) Mawu a Mulungu amatetezanso mabanja chifukwa amanena kuti anthu akakwatirana ayenera kukhala limodzi moyo wawo wonse.​—Werengani Genesis 2:24.

Tikamatsatira mfundo za m’Baibulo zinthu zingatiyendere bwino komanso tingapewe kuvutika maganizo. Mwachitsanzo, mabwana akafuna kulemba anthu ntchito, amafuna anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo, monga kuona mtima komanso kulimbikira ntchito. (Miyambo 10:4, 26; Aheberi 13:18) Mawu a Mulungu amatiphunzitsanso kuti tiyenera kukhala okhutira ndi zimene tili nazo komanso kuona kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi wofunika kwambiri kuposa zinthu zakuthupi.​—Werengani Mateyu 6:24, 25, 33; 1 Timoteyo 6:8-10.

Mfundo zopezeka m’Malemba zingatithandizenso kuti tikhale ndi thanzi labwino. (Miyambo 14:30; 22:24, 25) Mwachitsanzo, lamulo la Mulungu loletsa kuledzera limatiteteza kuti tisadwale matenda oopsa komanso kuti tisachite ngozi. (Miyambo 23:20, 29, 30) Yehova saletsa anthu kumwa mowa pang’ono, koma safuna kuti aziledzera. (Salimo 104:15; 1 Akorinto 6:10) Mfundo za Mulungu zimatithandiza kupewa makhalidwe ndi maganizo oipa. (Salimo 119:97-100) Koma sikuti Akhristu oona amatsatira mfundo za Mulungu pongofuna kuti zinthu ziwayendere bwino. Iwo amachita zimenezi chifukwa chakuti amalemekeza Yehova.​—Werengani Mateyu 5:14-16.