Pitani ku nkhani yake

Kodi Mulungu Amaloleza Mitala?

Kodi Mulungu Amaloleza Mitala?

Yankho la m’Baibulo

Pa nthawi inayake Mulungu ankalola zoti mwamuna azikwatira akazi angapo. (Genesis 4:19; 16:1-4; 29:18-29) Komabe Mulungu si amene anayambitsa mitala. Izi zili choncho chifukwa anapereka mkazi m’modzi yekha kwa Adamu.

Mulungu anauza Yesu Khristu kuti aikenso lamulo loyambirira la Mulunguyo lokhudza ukwati, losonyeza kuti mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi m’modzi yekha. (Yohane 8:28) Anthu ena atafunsa Yesu pa nkhani yokhudza ukwati, anayankha kuti: “Amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’”—Mateyu 19:4, 5.

Patapita nthawi, m’modzi mwa ophunzira a Yesu analemba mouziridwa ndi Mulungu kuti: “Mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.” (1 Akorinto 7:2) Baibulo limanenanso kuti mwamuna wokwatira amene ali ndi udindo mumpingo wachikhristu ayenera kukhala “mwamuna wa mkazi mmodzi.”—1 Timoteyo 3:2, 12.