Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?

Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?

Zimene Owerenga Amafunsa

Kodi Mulungu Amavomereza Mitala?

Yankho ndi lakuti ayi, chifukwa ukwati umene Mulungu anayambitsa m’munda wa Edene unali wa mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi. Yesu Khristu nayenso anatsindika mfundo imeneyi kwa otsatira ake.​—Genesis 2:18-24; Mateyo 19:4-6.

Nanga n’chifukwa chiyani anthu ngati Abulahamu, Yakobo, Davide ndiponso Solomo, omwe anakhalapo Chikhristu chisanayambe, anali ndi akazi ambiri? Kodi Baibulo limanena chiyani pankhani ya mitala? Baibulo limasonyeza kuti mitala imabweretsa mavuto ambiri monga mmene zinalili m’banja la Abulahamu komanso la Yakobo. (Genesis 16:1-4; 29:18–30:24) Kenako, Mulungu analamula kuti munthu aliyense yemwe ndi mfumu “asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake.” (Deuteronomo 17:15, 17) Koma Solomo sanamvere lamulo limeneli ndipo anakwatira akazi oposa 700. N’zomvetsa chisoni kuti mtima wake unasiya kukonda Yehova chifukwa chokwatira akazi ambirimbiri omwe sankalambira Mulungu. (1 Mafumu 11:1-4) Motero, Baibulo limasonyeza moonekeratu kuti mitala siyabwino.

Komabe, ena angafunse kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu ankalolera kuti anthu azikwatira mitala?’ Kuti timvetse zimenezi, taganizirani izi: Tiyerekezere kuti muli pantchito inayake yomwe simakusangalalatsani. Mwina mumangogwira ntchitoyo chifukwa mumadziwa kuti ngati mutasiya n’kumakafunafuna ina, banja lanu likhoza kuvutika kwambiri. Zimenezi n’zofanana ndi zimene Yehova anachita. N’zoona kuti zochita ndiponso nzeru za Mulungu n’zakuya kwambiri kuposa zathu. (Yesaya 55:8, 9) Komabe, tikhoza kumvetsa zina mwa zifukwa zimene zinam’chititsa kuti azilolera anthu kuchita mitala panthawi imeneyo.

Kumbukiraninso kuti m’munda wa Edene, Yehova analonjeza “mbewu” imene idzawonongeratu Satana. Ndipo patapita nthawi, Abulahamu analonjezedwa kuti adzakhala tate wa fuko lalikulu ndiponso kuti Mbewu yolonjezedwayo idzachokera m’banja lake. (Genesis 3:15; 22:18) Koma Satana anayesetsa kuti alepheretse Mbewu imeneyi. Choncho, iye ankachita zinthu zoti awonongeretu mtundu wonse wa Isiraeli. Nthawi zambiri Satana ankakopa mtunduwu kuti uzichita machimo, n’cholinga choti Mulungu asamauyanje ndiponso asamuteteze.

Pofuna kuthandiza Aisiraeli kuti asakodwe m’misampha ya Satana, Yehova ankati akaona kuti iwo ayamba kunyalanyaza mfundo zake zolungama, ankatumiza aneneri kuti awachenjeze. Komabe, iye ankadziwa kuti anthu akewo nthawi zambiri azilephera kutsatira malamulo ake, ngakhale osavuta, monga lamulo loletsa kulambira mafano. (Eksodo 32:9) Ngati ankalephera kutsatira lamulo lofunika komanso lophweka kwambiri ngati limeneli, kodi akanakwanitsa kumvera lamulo loletsa mitala? Popeza Yehova amamvetsa bwino kwambiri mmene anthufe tilili, iye anaona kuti imeneyo sinali nthawi yabwino yoti aletse mitala, chifukwa anthu ambiri anali atazolowera kale. Yehova akanaletsa mitala nthawiyo, zikanakhala zosavuta kuti Satana akope Aisiraeli ambiri kuti asamamvere lamulolo.

Zomwe Mulungu anachita polola mitala nthawi imeneyo zinali ndi ubwino wake. Zinathandiza kuti mtunduwo ukule kwambiri m’nthawi yochepa ndipo zimenezi zinachititsanso kuti mtunduwu ukhalepobe mpaka m’nthawi ya Mesiya. Komanso khalidwe lokwatira mitala liyenera kuti linathandiza azimayi ena, omwe mwina sakanakwatiwa, kuti apeze mwayi wokwatiwa. Zimenezi zinkathandiza azimayiwo kuti akhale ndi nyumba zawozawo ndiponso kuti akhale otetezeka pamodzi ndi mabanja awo m’nthawi zovuta.

Koma kumbukirani kuti Yehova si amene anayambitsa mitala. Iye anangololera khalidweli kwa nthawi yochepa ndipo anapereka malamulo omveka bwino othandiza kuti amuna asamachite nkhanza m’mabanja a mitala. (Eksodo 21:10, 11; Deuteronomo 21:15-17) Koma pamene Yehova anasankha zothetsa mitala, anagwiritsa ntchito Mwana wake kuti atsindikenso mfundo yakuti ukwati uyenera kukhala pakati pa mwamuna ndi mkazi mmodzi, ngati mmene zinalili m’munda wa Edene. Motero, Yesu analamula kuti otsatira ake asamachite mitala. (Maliko 10:8) Zimenezi, zachititsa kuti anthu amvetse mfundo ya choonadi yakuti: Chilamulo cha Mose chinali chabwino, koma “chilamulo cha Khristu” n’chabwino kwambiri.​—Agalatiya 6:2.